Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gl tsamba 4-5
  • Mayiko Otchulidwa M’baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mayiko Otchulidwa M’baibulo
  • ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu a Mulungu Abwerera Kudziko Lawo
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Girisi ndi Roma Akhudza Moyo wa Ayuda
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Chikristu Chifalikira Kumayiko Ena
    ‘Onani Dziko Lokoma’
  • Maufumu Athira Nkhondo Dziko Lolonjezedwa
    ‘Onani Dziko Lokoma’
Onani Zambiri
‘Onani Dziko Lokoma’
gl tsamba 4-5

Mayiko Otchulidwa M’baibulo

AISRAYELI ali m’kati mokonzekera kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anapempha Mulungu chimene mtima wake unali kulakalaka. Iye anati: “Ndiwoloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordano, mapiri okoma aja.”—Deut. 3:25.

Chimene Mose anapemphacho sichinatheke, koma anakwera m’phiri lina loyang’anizana ndi Yeriko n’kuliona dzikolo. Anaona, ‘Gileadi, kufikira ku Dani ndi dziko la Yuda kufikira nyanja ya m’tsogolo ndi [ku Negebu], ndi chigwa cha Yordano.’ (Deut. 3:27; 34:1-4) Kodi munamvapo mayina ameneŵa? Kodi mukudziŵa kumene anali?

Mwa anthu a Yehova lerolino ndi anthu oŵerengeka chabe amene angathe kupita kukaona malo ambiri amene nkhani zake amaziŵerenga m’Baibulo. Satha kuchita zomwe Mulungu anauza Abrahamu kuti achite, zoyendayenda m’litali ndi m’mimba mwa Dziko Lolonjezedwa. (Gen. 13:14-17) Komabe Akristu oona ali ndi chidwi chofuna kudziŵa za malo otchulidwa m’Baibulo ndiponso kuona mmene malowo akugwirizanirana ndi malo ena.

‘Onani Dziko Lokoma’ ndi buku limene mungaligwiritse ntchito kuti muwamvetse bwino Malemba. Lili ndi zithunzi zosonyeza mmene madera ena alili panopo, monga dera la Gileadi lomwe talisonyeza pachikuto. Mungaphunzire zambiri kudzera m’mapu a m’buku lino, omwe angakuthandizeni kudziŵa bwino malo otchulidwa m’Baibulo.

Mapu omwe ali pamasamba 2 ndi 3 akusonyeza makamaka mayiko kapena madera akuluakulu. Mwachitsanzo, mutaona pamene Asuri ndi Igupto anali poyerekeza ndi Dziko Lolonjezedwa, mungamvetse maulosi amene amanena za mayiko ameneŵa. (Yes. 7:18; 27:13; Hos. 11:11; Mika 7:12) Chigawo chaching’ono chotchedwa kuti Dziko Lolonjezedwa chinali dera lomwe kalelo munkadutsa njira zambiri, ndipo mitundu ina inkafuna kumalamulira nthaka yake yachonde yolola mbewu zosiyanasiyana, minda yamphesa, ndiponso mitengo ya azitona.—Deut. 8:8; Ower. 15:5.

Mayiko ndi Mizinda ya M’Baibulo

Nthaŵi zina mungafunike kuyerekeza mapu angapo. Mwachitsanzo, Yona anatumidwa ku likulu la Asuri, koma iye anakwera chombo kupita ku Tarisi. (Yona 1:1-3) Kodi madera ameneŵa akupezeka pamapu oyamba aja? Komatu osasokoneza Tarisi ndi Tariso, komwe mtumwi Paulo anabadwira. Pamapu ali panoŵa mungapezepo Tariso ndiponso mizinda ina yotchuka.

Taganizirani za mtunda ndiponso njira yomwe Abrahamu anadutsa paulendo wake mutapeza pamene pali Uri, Harana, ndi Yerusalemu. Yehova atauza Abrahamu kuti achoke ku Uri, iye anakakhala ku Harana ndipo kenako anasamukira ku Dziko Lolonjezedwa. (Gen. 11:28–12:1; Mac. 7:2-5) Muumvetsa bwino ulendo wa Abrahamu mukaŵerenga nkhani yakuti “Moyo wa Makolo Akale,” pamasamba 6 mpaka 7.

Mapu oyamba aja ndiponso aŵa ali panoŵa sakunena za nthaŵi iliyonse. Koma mapu ena onse akuyenderana ndithu ndi zochitika zofotokozedwazo. Midzi kapena zina ndi zina zosonyezedwa pamapupo, zikukhudza zinthu zimene zinachitika panthaŵi ina yake. Ngakhale kuti Mlozera Malo (pamasamba 34-35) alibe malo onse omwe asonyezedwa m’mapu, angakuthandizenibe kudziŵa kuti ndi mapu ati amene akufotokoza za mfundo yomwe mukufufuzayo.

Mapu omwe ali pakati (pamasamba 18-19) ali ndi midzi yambiri ya m’Dziko Lolonjezedwa. Bokosi la Zizindikiro za Pamapu lingakuthandizeni kupeza midzi ya Alevi ndiponso midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako komanso lingakuthandizeni kudziŵa ngati malo ena ake anatchulidwa m’Malemba Achihebri, m’Malemba Achigiriki, kapena m’Malemba Achihebri ndi Achigiriki omwe.

Pakalipano malo ena otchulidwa m’Baibulo sakudziŵika kuti anali pati, motero mapu amene ali pakatiwo alibe malo ambiri oterowo. Komanso, sizinatheke kusonyeza midzi yonse yomwe ili pa mndandanda wa malire a mafuko. (Yos., machaputala 15-19) Komabe mapu ameneŵa ali ndi midzi yoyandikana nayo, motero mungathe kungoyerekezera pamene panali midziyo. Taika zizindikiro pa zinthu zina zachilengedwe (monga mapiri, mitsinje, ndiponso zigwa), ndipo kukwera komanso mmene malowo alili tazisonyeza ndi mitundu yosiyanasiyana. Zimenezi zingakuthandizeni kukhala ngati mukuona zochitika zofotokozedwa m’Baibulo.

Buku la Insight on the Scriptures, limafotokoza zambiri zokhudza malo otchulidwa m’Baibulo, ndipo bukuli limapezeka m’zinenero zambiri.a Pamene mukugwiritsa ntchito buku limenelo ndi mabuku ena othandiza pophunzira Baibulo, buku lino lakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ lizikhala pafupi. Ligwiritseni ntchito pamene mukuphunzira Malemba onse amene ali opindulitsa kwambiri pamoyo wanu.—2 Tim. 3:16, 17.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 5]

MABUKU A BAIBULO ANALEMBEDWERA KU

Babulo

Kaisareya

Korinto

Igupto

Efeso

Yerusalemu

Makedoniya

Moabu

Patmo

Dziko Lolonjezedwa

Roma

Susani

[Mapu patsamba 4, 5]

(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)

Bible Lands and Key Cities

A1 ITALIYA

A2 ROMA

A3 SICILY

A3 MALTA

C2 MAKEDONIYA

C2 Filipi

C2 GIRISI

C3 ATENE

C3 Korinto

C3 KRETE

C4 LIBYA

D3 Antiokeya (ku Pisidiya)

D3 Efeso

D3 PATMO

D3 RODE

D4 MOFI

D5 IGUPTO

E2 ASIYA MINA

E3 Tariso

E3 Antiokeya (ku Suriya)

E3 KUPRO

E4 Sidoni

E4 Damasiko

E4 Turo

E4 Kaisareya

E4 DZIKO LOLONJEZEDWA

E4 YERUSALEMU

E4 MOABU

E4 Kadesi

E4 EDOMU

F3 Munda wa Edene?

F3 ASURI

F3 Harana

F3 SURIYA

F5 ARABIYA

G3 NINEVE

G4 BABULO

G4 KALDAYO

G4 Susani

G4 Uri

H3 MEDIYA

[Mapiri]

E5 Phiri la Sinai

G2 MAPIRI A ARARATI

[Nyanja]

C3 Nyanja ya Mediterranean (Nyanja Yaikulu)

E1 Nyanja Yakuda

E5 Nyanja Yofiira

H2 Nyanja ya Caspian

H5 Nyanja ya Perisiya

[Mitsinje]

D5 Mtsinje wa Nile

F3 Mtsinje wa Firate

G3 Mtsinje wa Tigirisi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena