“Dziko Labwino ndi Lalikulu”
PACHITSAMBA choyaka moto, Mulungu anauza Mose kuti Iye ‘adzalanditsa [anthu Ake] m’manja a Aigupto, ndi . . . kuwaloŵetsa m’dziko labwino ndi lalikulu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.’—Eks. 3:8.
Zithunzi ziŵiri zili apazi zochita kupanga pakompyuta zingakuthandizeni kumvetsa zinthu zachilengedwe zosiyanasiyana za m’Dziko Lolonjezedwa ndi mmene deralo linalili. (Zithunzizi zakuzidwa kuti muthe kusiyanitsa bwinobwino mapiri, zigwa, nyanja, ndi mitsinje.) Pitani pa galafuyo ya tizigawo tamitundu yosiyanasiyana kuti muone kukwera kwa kumtunda poyerekeza ndi pamene pamalekeza madzi a nyanja zazikulu.
Tchati chikusonyeza njira ina yolongosolera mndandanda wa zinthu zachilengedwe m’dzikolo. M’Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version, mawu akuti Araba ndi Shefela mwambiri anawamasulira kuti “kuchidikha,” pamene mawu akuti Negebu anawamasulira kuti “kum’mwera.”a—Gen. 13:1; Deut. 1:7; Yos. 11:16.
[Mawu a M’munsi]
a Mafotokozedwe ake ndi malemba ake a m’Baibulo a malowo mungawapeze mu buku la “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial” (Study 1, masamba 270-8) ndi la Insight on the Scriptures (Voliyumu 2, masamba 568-71). Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova m’Chingelezi ndi zinenero zina zambiri.
[Tchati/Mapu patsamba 12, 13]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Mmene Dzikolo Lilili
Tchati cha Zinthu Zachilengedwe
A. Gombe la Nyanja Yaikulu
B. Zidikha Kumadzulo kwa Yordano
1. Chidikha cha Aseri
2. Mkwasa wa Gombe la Doro
3. Mabusa a Saroni
4. Chidikha cha Filistiya
5. Chigwa Chapakati Chochokera Kum’maŵa Kupita Kumadzulo
a. Chidikha cha Megido
b. Chigwa cha Yezreeli
C. Mapiri Kumadzulo kwa Yordano
1. Mapiri a Galileya
2. Mapiri a Karimeli
3. Mapiri a Samariya
4. Shefela (zitunda)
5. Dera la Mapiri la Yuda
6. Chipululu cha Yuda
7. Negebu
8. Chipululu cha Parana
D. Araba (Chigwa)
1. Thamanda la Hula
2. Dera la Nyanja ya Galileya
3. Chigwa cha Yordano
4. Nyanja ya Mchere (Nyanja Yakufa)
5. Araba (kum’mwera kwa Nyanja ya Mchere)
E. Mapiri/Malo Okwera Kum’maŵa kwa Yordano
1. Basana
2. Gileadi
3. Amoni ndi Moabu
4. Dera la M’mapiri la Edomu
F. Mapiri a Lebano
[Map]
Phiri la Herimoni
Dani
Jerusalemu
Beere—seba
Kuona Dziko Lolonjezedwa Titalidula
mamita mafiti
2,500 7,500
2,000 6,000
1,500 4,500
1,000 3,000 Dera la Mapiri Dziko la
la Yuda Moabu
500 1,500
Shefela Chipululu
Chidikha cha Cha Yuda
Filistiya Rift
0 0 (Polekeza Madzi a Valley
Nyanja Zazikulu) Nyanja ya Mchere
-500 -1,500
[Chithunzi patsamba 13]
Phiri la Hermoni (2,814 m; 9,232 ft)
[Chithunzi patsamba 13]
Gombe la Nyanja ya Mchere; malo otsika kwambiri padziko lapansi (kuchoka polekeza madzi a nyanja zazikulu, lili pafupifupi mamita 400, mafiti 1,300 kutsika kupita pansi)