Yerusalemu ndi Kachisi Amene Yesu Ankamudziŵa
PATAPITA nthaŵi pang’ono Yesu atabadwa, Yosefe ndi Mariya anamutenga kupita naye kumzinda wa Yerusalemu kumene Atate wake wakumwamba anaikako dzina Lake. (Luka 2:22-39) Ali ndi zaka 12, Yesu anapitanso ku Yerusalemu ku Paskha. Iye anadabwitsa aphunzitsi a pakachisi ndi nzeru zake. (Luka 2:41-51) Ntchito yomanga kachisiyo, yomwe inali ina mwa ntchito zambiri zomanga za Herode Wamkulu, inatenga “zaka makumi anayi ndi zisanu ndi chimodzi.”—Yoh. 2:20.
Pa utumiki wake, Yesu anali kukhala nawo pa maphwando ku Yerusalemu, kumene nthaŵi zambiri anali kuphunzitsa anthu ambirimbiri. Kaŵiri konse anathamangitsa anthu osintha ndalama ndi amalonda kuwachotsa m’bwalo la kachisi.—Mat. 21:12; Yoh. 2:13-16.
Kumpoto kwa kachisiyo, pathamanda la Betesda, Yesu anachiritsa munthu yemwe anadwala zaka 38. Mwana wa Mulungu ameneyu anachiritsanso munthu wakhungu, yemwe anamuuza kuti akasambe m’thamanda la Siloamu lomwe linali kum’mwera kwa mzindawo.—Yoh. 5:1-15; 9:1, 7, 11.
Yesu nthaŵi zambiri anali kukacheza kwa mabwenzi ake Lazaro, Mariya, ndi Marita ku Betaniya, “pafupifupi makilomita atatu” kum’maŵa kwa Yerusalemu. (Yoh. 11:1, 18, NW, mawu a m’munsi; 12:1-11; Luka 10:38-42; 19:29; onani “Dera la Yerusalemu,” patsamba 18.) Patatsala masiku ochepa kuti aphedwe, Yesu anafika ku Yerusalemu podutsira ku Phiri la Azitona. Tangoyerekezerani kuti mukumuona akuima ndi kuyang’ana kumadzulo pa mzindawo, n’kumaulirira. (Luka 19:37-44) Zimene iye anaona zingakhale zofanana ndi zimene mukuona patsamba lotsatirali pamwamba. Kenako Yesu analoŵa m’Yerusalemu atakwera pabulu, ndipo ayenera kuti analoŵera pa chimodzi mwa zipata za kum’maŵa kwa mzindawo. Makamu a anthu anam’tamanda monga Mfumu ya Israyeli ya m’tsogolo.—Mat. 21:9-12.
Zinthu zofunika zimene zinachitika Yesu asanafe, zinachitikira m’Yerusalemu kapena malo ena pafupi ndi mzindawo: m’munda wa Getsemane, kumene Yesu anapemphera; Bwalo la Akulu (Sanihedrini); m’nyumba ya Kayafa; m’nyumba ya Kazembe Pilato ndipo pomaliza ku Gologota.—Marko 14:32, 14:53–15:1, 16, 22; Yoh. 18:1, 13, 24, 28.
Yesu ataukitsidwa, anaonekera ku Yerusalemu ndi malo ena apafupi ndi mzindawu. (Luka 24:1-49) Kenako anakwera kumwamba kuchokera pa Phiri la Azitona.—Mac. 1:6-12.
[Chithunzi patsamba 31]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Jerusalem/Herod’s Temple
Mbali za Kachisi
1. Malo Opatulikitsa
2. Malo Opatulika
3. Guwa la Nsembe Yopsereza
4. Thawale Lamkuwa
5. Bwalo la Ansembe
6. Bwalo la Israyeli
7. Bwalo la Akazi
8. Bwalo la Akunja
9. Mpanda (Soreg)
10. Khumbi Lachifumu
11. Khumbi la Solomo
KACHISI
Chipata
Bwalo la Ansembe
Chipata
Malo Opatulikitsa Guwa la
Malo Opatulika Nsembe Bwalo la Bwalo la
Yopsereza Israyeli Akazi
Thawale
Lamkuwa
Chipata Khumni la
Mpanda (Soreg) Solomo
Bwalo la Akunja
Chipata
Khumbi Lachifumu
Zipata
Nsanja ya Antonia
Mlatho
Bwalo la Akulu? (Sanihedirini)
CHIGWA CHA TYROPOEON
Thamanda la Siloamu
Ngalande
Nyumba ya Kayafa?
Nyumba ya Kazembe
Gologota?
Gologota?
Thamanda la Betesda
Munda wa Getsemane?
PHIRI LA AZITONA
CHIGWA CHA KIDRONI
Kasupe wa Gihoni
Eni-rogeli
CHIGWA CHA HINOMU (GEHENA)
[Zithunzi patsamba 30]
Kuyang’ana kum’maŵa kudutsa Yerusalemu wamakono: (A) malo a kachisi, (B) munda wa Getsemane, (C) Phiri la Azitona, (D) chipululu cha Yudeya, (E) Nyanja Yakufa
[Chithunzi patsamba 31]
Kuyang’ana kumadzulo muli pa Phiri la Azitona m’nthaŵi ya Yesu