Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kp tsamba 12-15
  • ‘Nthaŵi ya Chiweruzo’ Yafika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Nthaŵi ya Chiweruzo’ Yafika
  • Dikirani!
  • Nkhani Yofanana
  • Mzinda Waukulu Udzawonongedwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • “Thaŵani Pakati pa Babulo”
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • “Babulo” Wosatetezereka Aweruziridwa ku Chiwonongeko
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Dikirani!
kp tsamba 12-15

‘Nthaŵi ya Chiweruzo’ Yafika

CHIVUMBULUTSO, buku lomaliza la m’Baibulo, limatiuza kuti pali mngelo amene akuuluka pakati pa mlengalenga ndipo ali ndi “Uthenga Wabwino wosatha, [woti] aulalikire.” Akunena ndi mawu aakulu kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.” (Chivumbulutso 14:6, 7) ‘Nthaŵi ya chiweruzo’ imeneyo ikuphatikizapo kulengeza ndiponso kupereka chiweruzo cha Mulungu. Idzakhala pachimake pa “masiku otsiriza.” Panopa tikukhala m’masiku otsiriza amenewo.—2 Timoteo 3:1.

Kufika kwa ‘nthaŵi ya chiweruzo’ ndi uthenga wabwino kwa anthu okonda chilungamo. Ndi nthaŵi imene Mulungu adzabweretse mpumulo kwa atumiki ake amene avutika kwambiri m’dongosolo la zinthu lachiwawa ndi lopanda chikondi lino.

Panopa, ‘nthaŵi ya chiweruzo’ isanathe mwa kuwonongedwa kwa dongosolo la zinthu loipa lilipoli, akutilimbikitsa kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero.” Kodi mukuchita zimenezo? Zimenezi zimatanthauza zambiri, osati kungonena kuti, “Ndimakhulupirira Mulungu.” (Mateyu 7:21-23; Yakobo 2:19, 20) Kuopa Mulungu koyenera kuyenera kutichititsa kumulemekeza. Kuyenera kutichititsa kupeŵa zoipa. (Miyambo 8:13) Kuyenera kutithandiza kukonda zabwino ndi kudana ndi zoipa. (Amosi 5:14, 15) Ngati timalemekeza Mulungu, tidzamvera chilichonse chimene amanena. Sitidzatanganidwa ndi zinthu zina n’kumalephera kupeza nthaŵi yoŵerengera Mawu ake, Baibulo, nthaŵi zonse. Tidzamukhulupirira nthaŵi zonse ndiponso ndi mtima wathu wonse. (Salmo 62:8; Miyambo 3:5, 6) Anthu amene amalemekezadi Mulungu amadziŵa kuti iye pokhala Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, ndiye Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, ndipo chifukwa chakuti amamukonda, amagonjera kwa iye monga Wolamulira miyoyo yawo. Ngati tikuona kuti tiyenera kuganiziranso nkhani zimenezi mosamalitsa, m’pofunika kwambiri kuti titero mwamsanga.

Nthaŵi yopereka chiweruzo imene mngeloyo anaitchula imatchedwanso “tsiku la Yehova.” “Tsiku” loterolo linafika pa Yerusalemu wakale m’chaka cha 607 B.C.E. chifukwa chakuti anthu okhala mu Yerusalemuyo sanamvere machenjezo amene Yehova ankapereka kudzera mwa aneneri ake. Chifukwa chakuti anali kuganiza kuti tsiku la Yehova lili kutali, zinawonjezera kuika miyoyo yawo pangozi. Yehova anali atawachenjeza kuti: “Lili pafupi lifulumira kudza.” (Zefaniya 1:14) “Tsiku la Yehova” linanso linafika pa Babulo wakale m’chaka cha 539 B.C.E. (Yesaya 13:1, 6) Pokhulupirira malinga awo ndi milungu yawo, Ababulo ananyalanyaza machenjezo amene aneneri a Yehova anapereka. Koma mu usiku umodzi wokha, Babulo woopsayo anagonjetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi.

Kodi masiku ano tikuyembekezera kukumana n’chiyani? “Tsiku la Yehova” lina, koma lokhudza anthu ambiri ndiponso loopsa kwambiri. (2 Petro 3:11-14) Chiweruzo cha Mulungu chalengezedwa pa ‘Babulo Wamkulu.’ Malinga ndi Chivumbulutso 14:8, mngelo akulengeza kuti: ‘Wagwa Babulo wamkulu.’ Zimenezo zachitika kale. Sangalepheretsenso anthu a Yehova kulambira Yehovayo. Katangale wake ndi kuloŵerera kwake m’nkhondo zaululidwa poyera. Panopa kuwonongedwa kwake kuli pafupi. Pachifukwa chimenecho, Baibulo likulimbikitsa anthu kulikonse kuti: “Tulukani mmenemo [mu Babulo Wamkulu] . . . kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.”—Chivumbulutso 18:4, 5.

Kodi Babulo Wamkulu n’chiyani? Ndi zipembedzo zonse padziko lapansi zimene zochita zake zimafanana ndi za Babulo wakale. (Chivumbulutso, machaputala 17, 18) Taonani kufanana kwina uku:

• Ansembe a ku Babulo wakale ankachita nawo kwambiri zinthu zandale m’dzikolo. Zipembedzo zambiri zimachitanso zimenezo masiku ano.

• Ansembe a ku Babulo nthaŵi zambiri ankalimbikitsa dzikolo kumenya nkhondo. Zipembedzo za masiku ano n’zomwe zimakhala patsogolo kudalitsa asilikali akamapita kukamenyana ndi mayiko ena.

• Ziphunzitso ndi zochita za Babulo wakale zinachititsa anthu a m’dzikolo kuchita chiwerewere chosaneneka. Atsogoleri a chipembedzo masiku ano amanyalanyaza mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino, ndipo zotsatirapo zake n’zoti atsogoleri achipembedzo ndiponso anthu wamba opita kutchalitchi amachita chiwerewere koopsa. N’zochititsanso chidwi kuona kuti, chifukwa chakuti Babulo Wamkulu akamachita zinthu ndi dzikoli ndi ndale zake amakhala ngati hule, buku la Chivumbulutso limamutchula kuti mkazi wachigololo.

• Baibulo limanenanso kuti Babulo Wamkulu ‘akudyerera.’ Mu Babulo wakale, makachisi anali ndi malo aakulu, ndipo ansembe anatchuka pa nkhani zamalonda. Masiku ano, kuwonjezera pa malo opempherera, Babulo Wamkulu amachita malonda kwambiri ndiponso ali ndi katundu wambiri. Ziphunzitso zake ndi maholide ake zimabweretsera Babulo Wamkuluyo komanso anthu ena azamalonda chuma chambiri.

• Kugwiritsa ntchito mafano, matsenga, ndi ufiti kunali kofala mu Babulo wakale, monganso momwe zilili m’madera ambiri masiku ano. Imfa inkaonedwa ngati njira yopitirira ku moyo wina. Mu Babulo munali akachisi ndi matchalitchi ambiri olemekeza milungu yake, koma Ababulo ankadana ndi anthu olambira Yehova. Zikhulupiriro ndi zochita zomwezo n’zimene zikupezekanso mu Babulo Wamkulu masiku ano.

Mu nthaŵi zakale, Yehova anachititsa mayiko amphamvu pandale ndi pazankhondo kulanga anthu amene anapitiriza kusamumvera ndi kunyalanyaza zolinga zake. N’chifukwa chake Samariya anawonongedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E. Yerusalemu anawonongedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E. kenaka ndi Aroma mu 70 C.E. Babulo nayenso anawonongedwa ndi Amedi ndi Aperisi mu 539 B.C.E. Ponena za masiku ano, Baibulo linaneneratu kuti maboma andale, monga chilombo, adzatembenukira “mkazi wachigololo” n’kumuvula, kuvumbula poyera khalidwe lake lenileni. Adzamuwonongeratu.—Chivumbulutso 17:16.

Kodi maboma a dzikoli adzachitadi zimenezo? Baibulo limanena kuti Mulungu adzaika zimenezi “kumtima kwawo.” (Chivumbulutso 17:17) Zidzakhala zadzidzidzi, zodabwitsa, ndiponso zochititsa mantha, osati zoonekeratu kuti zikubwera kapena zochitika pang’onopang’ono.

Kodi mufunika kuchita chiyani? Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikadali m’chipembedzo chimene chimaphunzitsa ndi kuchita zinthu zimene zimasonyeza kuti chili mbali ya Babulo Wamkulu?’ Ngakhale ngati simuli m’chipembedzo choterocho, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndalola kuti mzimu wake undikhudze?’ Mzimu wotani? Mzimu wololera khalidwe lotayirira, wokonda chuma ndi zosangalatsa m’malo mokonda Mulungu, kapena mzimu wonyalanyaza dala Mawu a Yehova (ngakhale m’zinthu zooneka ngati zazing’ono). Ganizani mofatsa musanayankhe.

Kuti tikondweretse Yehova, m’pofunika kwambiri kuti zimene timachita ndiponso zimene mtima wathu umalakalaka zizisonyeza kuti sitilidi mbali ya Babulo Wamkulu. Tichite zimenezi mwachangu chifukwa nthaŵi yatsala yochepa. Potidziŵitsa kuti mapeto adzafika modzidzimutsa, Baibulo limati: “Chotero [mwamsangamsanga, NW] Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.”—Chivumbulutso 18:21.

Koma padzachitikanso zina. Monga mbali ina ya ‘nthaŵi ya chiweruzo’ imeneyo, Yehova Mulungu adzaweruza dongosolo lonse la ndale padziko lapansi, atsogoleri ake, ndi onse amene amanyalanyaza ulamuliro wake woyenera kudzera mu Ufumu wake wakumwamba umene uli m’manja mwa Yesu Kristu. (Chivumbulutso 13:1, 2; 19:19-21) Masomphenya a ulosi amene analembedwa pa Danieli 2:20-45 akusonyeza ulamuliro wa ndale zadziko kuyambira nthaŵi ya Babulo wakale kufika nthaŵi yathu ino monga fano lalikulu lopangidwa ndi golide, siliva, mkuwa, chitsulo, ndi dongo. Ponena za nthaŵi yathu ino, ulosiwo unati: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse.” Ndipo ponena za zimene Ufumuwo udzachite pa ‘nthaŵi ya chiweruzo’ ya Yehova, Baibulo limati: “Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [a anthu] nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.

Baibulo limachenjeza olambira oona kuti asakonde ‘za m’dziko lapansi,’ kutanthauza kuti, asakonde njira ya moyo imene dziko lodana ndi Mulungu woona limalimbikitsa. (1 Yohane 2:15-17) Kodi zimene mumasankha ndi zimene mumachita zimasonyeza kuti mulidi ku mbali ya Ufumu wa Mulungu? Kodi mumaikadi Ufumuwo poyamba m’moyo wanu?—Mateyu 6:33; Yohane 17:16, 17.

[Bokosi patsamba 14]

Kodi Mapeto Adzafika Liti?

‘Munthaŵi imene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.’—Mateyu 24:44.

“Dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.”—Mateyu 25:13.

‘Silidzazengereza.’—Habakuku 2:3.

[Bokosi patsamba 14]

Kodi Mukanasintha Moyo Wanu Mukanadziŵa Tsiku Lake?

Ngati mukanadziŵa kuti chiweruzo cha Mulungu sichibwera kwa zaka zina zingapo, kodi mukanasintha mmene mukukhalira moyo wanu? Ngati mukuona kuti mapeto a dongosolo la zinthu lakaleli achedwa kuposa mmene munali kuganizira, kodi mwalola kuti zimenezo zikulepheretseni kutumikira Yehova mwachangu ngati mmene munali kuchitira kale?—Ahebri 10:36-38.

Kusadziŵa kwathu tsiku lenileni limene dongosolo lakaleli lidzathe kumatipatsa mpata wosonyeza kuti timatumikira Mulungu n’cholinga choyenera. Anthu amene akumudziŵa Yehova amadziŵa kuti kukhala wachangu kwakanthaŵi kochepa pamene mapeto atsala pang’ono kufika sikudzamukhutiritsa Mulungu, amene amaona mmene mtima wa munthu ulili.—Yeremiya 17:10; Ahebri 4:13.

Anthu amene amakondadi Yehova amamuika pamalo oyamba nthaŵi zonse. Mofanana ndi anthu ena, Akristu oona angagwire ntchito zina. Koma cholinga chawo sikufuna kulemera, koma kupeza zofunika pamoyo ndi zina zoti angapatseko ena. (Aefeso 4:28; 1 Timoteo 6:7-12) Amasangalala ndi zinthu zosangalatsa zoyenera ndi zinthu zina zongofuna kudzisangulutsa nazo, koma cholinga chawo n’choti atsitsimulidwe, osati kungochita nawo zimene aliyense akuchita. (Marko 6:31; Aroma 12:2) Mofanana ndi Yesu Kristu, amasangalala kwambiri pochita chifuniro cha Mulungu.—Salmo 37:4; 40:8.

Akristu oona amafuna kukhala ndi moyo wosatha akutumikira Yehova. Chiyembekezo chimenechi amachionabe kuti n’chamtengo wapatali ngakhale atayembekezera madalitso enaake kwa nthaŵi yaitali koposa mmene ena a iwo amaganizira.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]

Nkhani ya Ulamuliro

Kuti timvetse chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti pakhale kuvutika kwambiri kotereku, tiyenera kumvetsa nkhani ya ulamuliro.

Chifukwa chakuti Yehova ndi Mlengi, ali ndi ufulu wolamulira dziko lapansi ndi onse amene amakhalamo. Komabe, Baibulo limafotokoza kuti kumayambiriro kwa mbiri ya anthu, ulamuliro wa Yehova unatsutsidwa. Satana Mdyerekezi ananena kuti Yehova ankangofuna kuletsa zinthu monyanyira, ndiponso kuti ananamiza makolo athu oyambirira za zimene zidzachitike ngati atapanda kumvera malamulo a Mulungu n’kuchita zinthu mmene iwo anali kufunira. Satana Mdyerekezi ananenanso kuti zinthu zikanakhala bwino makolo athuwo akanati azidzilamulira okha osati kulamulidwa ndi Mulungu.—Genesis, machaputala 2, 3.

Ngati Mulungu akanawononga oukirawo nthaŵi yomweyo, zimenezo zikanasonyeza mphamvu zake, koma sizikanathetsa nkhani zimene zinabukazo. M’malo mowononga oukirawo nthaŵi yomweyo, Yehova walola kuti angelo ndiponso anthu onse aone zotsatirapo za kupanduka. Ngakhale kuti zimenezi zachititsa kuti anthu avutike, zatipatsanso mwayi woti tibadwe.

Kuwonjezera apo, ngakhale kuti zinali zopweteka kwambiri kwa iye, Yehova mwachikondi anakonza zoti anthu amene adzamumvere ndi kukhulupirira nsembe ya dipo ya Mwana wake adzapulumutsidwe ku uchimo ndi zotsatirapo zake ndipo adzakhale mu Paradaiso. Ngati pangafunike kutero, angachite zimenezi mwa kuukitsa munthu kwa akufa.

Kulola kuti nthaŵi idutse pothetsa nkhaniyo kwapatsanso atumiki a Mulungu mwayi woti asonyeze kuti angathe kumvera Mulungu chifukwa cha chikondi chake ndiponso angathe kukhala okhulupirika kwa Yehova pa zochitika za mtundu uliwonse. Kuthetsa nkhani ya ulamuliro, komanso nkhani yokhudzana ndi imeneyi ya kukhulupirika kwa anthu, n’kofunika kwambiri kuti chilengedwe chonse chizimvera malamulo moyenerera. Popanda zimenezo, sizingatheke kukhala ndi mtendere weniweni.a

[Mawu a M’munsi]

a Nkhani zimenezi komanso tanthauzo lake zafotokozedwa mwatsatanetsatane m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi]

Ulamuliro wapadziko lonse wa ndale udzatha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena