Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa
Panthawi inayake pamoyo wanu, mwina munafunsapo kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu amavutika chonchi?’ Kwa zaka zambiri, anthu akhala akuvutika kwambiri chifukwa cha nkhondo, umphawi, masoka, umbanda, kupanda chilungamo, matenda, ndi imfa. Pa zaka handiredi zapitazi anthu avutika kwambiri kuposa kale lonse. Kodi zonsezi zidzatha?
Inde zidzatha, ndipo zidzatha posachedwapa. Yankho limeneli ndi lolimbikitsa kwabasi. Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limati: “Woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Adzalandira dziko lapansi ndi kukondwera ndi mtendere wochuluka kwa nthawi yaitali bwanji? “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:10, 11, 29.
Mulungu akadzachotsa zinthu zoipa ndi mavuto, dziko lapansi lidzasanduka paradaiso. Panthawi imeneyo anthu adzakhala ndi moyo wosatha, ndipo adzakhala ndi thanzi labwino kwambiri ndiponso osangalala. Mawu a Mulungu akulonjeza kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:4.
M’dziko latsopano limenelo, ngakhale anthu akufa adzaukitsidwa kuti nawonso asangalale ndi madalitso amenewa. “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) N’chifukwa chake Yesu Kristu anatha kuuza munthu amene anasonyeza chikhulupiriro mwa iye, amene kale ankachita zoipa koma analapa, kuti: “Udzakhala ndine m’Paradaiso.”—Luka 23:43.
Kodi Mavuto Anayamba Chifukwa Chiyani?
Popeza Mulungu anakonza zoti anthu akhale ndi tsogolo labwino kwambiri loterolo, n’chifukwa chiyani analola kuti mavuto ayambe? Ndipo n’chifukwa chiyani walola kuti mavuto akhalepo kwa nthawi yaitali chonchi?
Mulungu polenga Adamu ndi Hava anawalenga ndi matupi ndi maganizo angwiro. Anawaika m’munda wa paradaiso n’kuwapatsa ntchito yosangalatsa yoti azigwira. Baibulo limati: “Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Adamu ndi Hava akanamvera Mulungu, akanakhala ndi ana angwiro, ndipo dziko lonse likanasanduka paradaiso, kumene anthu akanatha kukhala ndi moyo wosatha mwamtendere ndiponso mwachimwemwe.
Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava ufulu wabwino kwambiri wotha kusankha zochita, kuti ukhale chibadwa cha anthu. Sanawalenge ngati wilibala yomwe singathe kusankha kopita koma imangopita komwe akuikankhira. Komabe, kuti apitirizebe kukhala achimwemwe, anafunika kugwiritsa ntchito bwino ufulu wawo wosankha kuti amvere malamulo a Mulungu. Monga momwe Mulungu ananenera: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” (Yesaya 48:17) Kugwiritsa ntchito molakwika ufulu wosankha kukanabweretsa mavuto aakulu, chifukwa anthu sanalengedwe kuti angathe kudzilamulira okha bwinobwino popanda Mulungu. Baibulo limati: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
N’zomvetsa chisoni kuti makolo athu oyamba anaganiza kuti akhoza kusiya kudalira Mulungu zinthu n’kuwayenderabe bwinobwino. Koma pamene anakana ulamuliro wa Mulungu, Mulungu anasiya kuwasamalira ndipo anakhala opanda ungwiro. Choncho anayamba kutha mphamvu mpaka anakalamba n’kufa. Popeza ndife ana awo, tinatengera kupanda ungwiro kumeneko ndipo timafanso.—Aroma 5:12.
Nkhani Yaikulu Ndi Yoti: Kodi Woyenera Kulamulira Ndani?
N’chifukwa chiyani Mulungu sanawononge Adamu ndi Hava n’kulenganso anthu ena awiri? Chifukwa choti, mfundo yakuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse inakayikiridwa. Funso limene linakhalapo n’loti, Ndani amene ali woyenera kulamulira, ndipo ndi ulamuliro wa ndani umene uli wabwino? Funso linanso lomwe linabuka kuwonjezera pamenepo linali loti, Kodi anthu zinthu zingawayendere bwino Mulungu atati asamawalamulire? Mulungu wapatsa anthu nthawi yokwanira kuti ayesere kudzilamulira okha popanda iyeyo. Pochita zimenezi Mulungu anafuna kuti asonyeze poyera ngati zinthu zingawayendere bwino anthu akamalamulidwa ndi iyeyo kapena akamadzilamulira okha. Nthawi imene anthu anafunikira kukhala nayo inayenera kukhala yokwanira kuti ayesere mitundu yosiyanasiyana ya ndale, chikhalidwe, za malonda, ndi chipembedzo mosadalira Mulungu.
Kodi zotsatirapo zake zakhala zotani? Mbiri ya anthu pa zaka zambirimbiri yasonyeza kuti mavuto akungowonjezekera. M’zaka 100 zapitazi, anthu akumana ndi mavuto aakulu kuposa m’mbuyo monsemu. Anthu mamiliyoni ambiri anaphedwa ndi Anazi a ku Germany panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Anthu okwana pafupifupi 100 miliyoni aphedwa pankhondo zosiyanasiyana. Umbanda ndi chiwawa zili paliponse. Padziko lonse lapansi anthu ambirimbiri amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Matenda opatsirana pogonana akupitirizabe kufalikira. Anthu ambirimbiri amafa chaka chilichonse chifukwa cha njala ndi matenda. Mabanja akusokonekera ndipo makhalidwe akulowa pansi kulikonse. Palibe boma lililonse la anthu lomwe lingathe kuthetsa mavuto amenewa. Palibe boma lomwe lakwanitsa kuthetsa ukalamba, matenda, ndi imfa.
Zinthu zimene zikuchitikira anthu panopa zikugwirizana ndi zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika masiku athu ano. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti nthawi yathu ino ndi “masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu pamene “zidzafika nthawi zowawitsa.” Ndipo monga momwe Baibulo linanenera, ‘anthu oipa ndi onyenga, akuipa chiipire.’—2 Timoteo 3:1-5, 13.
Mavuto Atsala Pang’ono Kutha
Umboni wonse ukusonyeza kuti panopa tikuyandikira mapeto a nthawi yomvetsa chisoni imene anthu ayesera kuti adzilamulire okha osadalira Mulungu. Pali umboni wambiri womwe ukusonyeza poyera kuti anthu sangathe kudzilamulira okha osadalira Mulungu. Ndi ulamuliro wa Mulungu wokha womwe ungabweretse mtendere, chimwemwe, thanzi labwino, ndi moyo wosatha. Choncho nthawi yomwe Yehova walola kuti kukhale zinthu zoipa ndi mavuto yatsala pang’ono kutha. Posachedwapa Mulungu adzalowererapo pa zochita za anthu powononga dongosolo la zinthu lonseli, lomwe lalephera kuthandiza anthu.
Ulosi wa m’Baibulo umati: “Masiku a mafumu aja [maulamuliro a anthu omwe alipo panopa] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthawi zonse . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [maulamuliro apanopa] nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Kutsimikizira kuti Yehova ndi amene ali woyenera kulamulira pogwiritsa ntchito Ufumu wake wakumwamba, ndiye chiphunzitso chachikulu cha m’Baibulo. Poneneratu chizindikiro chofunika kwambiri cha “masiku otsiriza,” Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
Chimaliziro chikadzafika, kodi ndani adzapulumuke? Baibulo limayankha kuti: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.” (Miyambo 2:21, 22) Oongoka mtima ndi anthu amene amaphunzira chifuniro cha Yehova ndipo amachichita. Yesu Kristu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Zoonadi, “dziko lapansi lipita, . . . koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.”—1 Yohane 2:17.
Malemba akuchokera m’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina. Komabe, Chinyanjacho tachilemba m’kalembedwe katsopano. Pamene tasonyeza NW, ndiye kuti lembalo lachokera m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures—With References.