Gawo 3
Yesetsani Kuchita Zinthu Zosangalatsa Mulungu
Kodi mungayankhe bwanji mutafunsidwa kuti: ‘Kodi Yehova akufuna chiyani kwa inuyo?’ (Mika 6:8) Zimene aneneri 12 analemba, zingakuthandizeni kudziwa yankho la funso limeneli. M’mutu 8 mpaka 10 m’buku lino, muona kuti zimene aneneri 12 analemba, zingakuthandizeni kuti muzilankhula zoona nthawi zonse. Komanso muona kuti zingakuthandizeni kudziwa mmene mungapewere zachiwawa. Muonanso malangizo othandiza kwambiri okhudza moyo wabanja amene mungawagwiritse ntchito m’banja mwanu.