Mutu 17
Kodi Ndi Bwino Kucheza ndi Anzanga a Kusukulu?
“Nthawi zina ndikaona anzanga a kusukulu akucheza ndimasirira ndipo mumtima ndimangoti, ‘Ee, koma ndiye amagwirizanatu! Nanenso ndimafuna nditamacheza nawo.’”—Anatero Joe.
“Sindinkasowa anthu ocheza nawo kusukulu. Koma zimenezi zinandilowetsa m’mavuto aakulu.”—Anatero Maria.
ALIYENSE amafuna kukhala ndi anzake oti azicheza nawo momasuka komanso amene angawadalire pamavuto ndi pamtendere. Ngakhalenso Yesu anali ndi anzake amene ankacheza nawo. (Yohane 15:15) Panthawi imene Yesu ankapachikidwa pa mtengo wozunzikirapo, Yohane yemwe anali mnzake wapamtima anali chapafupi. (Yohane 19:25-27; 21:20) N’zosakayikitsa kuti nanunso mungafune kukhala ndi mnzanu wapamtima yemwe sangakutayeni pamavuto ndi pamtendere.
Mwina mumaona kuti muli ndi anzanu abwino a m’kalasi mwanu, omwe mumacheza nawo momasuka. Mumagwirazana nawo kwambiri ndipo mumasangalala kucheza nawo. Mwina inuyo mumaona kuti iwo sali m’gulu la anthu amakhalidwe oipa. (1 Akorinto 15:33) Mtsikana wina dzina lake Anne anati: “Ndimamasuka kucheza nawo chifukwa chakuti ndimaonana nawo kawirikawiri. N’zosiyana ndi kucheza ndi anthu a kumpingo, chifukwa nthawi zambiri umafunika kusamala kwambiri ndi zimene ukulankhula kapena kuchita. Koma kusukulu umacheza momasuka.” Mwinanso mungamve ngati Lois, yemwe anati: “Ndinkafuna kusonyeza anzanga a kusukulu kuti Mboni za Yehova si zosiyana ndi anthu ena ndipo ndife anthu abwinobwino.” Kodi zimenezi n’zifukwa zomveka zokuchititsani kuti muzigwirizana kwambiri ndi anzanu a kusukulu?
N’chifukwa Chiyani Mufunika Kusamala?
Taganizirani zimene zinachitikira Maria yemwe tamutchula kumayambiriro kwa nkhani ino. Chifukwa chakuti iye ankacheza ndi anthu momasuka, anali ndi anzake ambiri koma sankadziwa anthu omwe sanali oyenerera kucheza nawo. Iye anati: “Ndinkasangalala ndikaona kuti atsikana ndi anyamata omwe akundikonda. Koma pang’ono ndi pang’ono ndinayamba makhalidwe oipa.” Zimenezi zinamuchitikiranso Lois. Iye anati: “Ndinayamba kutengera makhalidwe oipa a anzanga.”
Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa kuti mugwirizane ndi mnzanu mumafunika kuchita zimene iye amakonda. Mukamacheza ndi anthu amene satsatira mfundo za m’Baibulo, khalidwe lanu lingawonongeke. (Miyambo 13:20) N’chifukwa chake mtumwi Paulo ananena kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira.”—2 Akorinto 6:14.
Zimene Mungachite
Kodi pamenepa Paulo ankatanthauza kuti tizipeweratu kucheza ndi anzathu a kusukulu? Ayi, chifukwa Akhristu amafunika kukhala anthu ochezeka kuti akwanitse ntchito yawo ‘yopanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse.’ Iwo afunikira kulalikira amuna ndi akazi amitundu yonse, zipembedzo zonse ndiponso zikhalidwe zonse.—Mateyo 28:19.
Mtumwi Paulo anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi. Iye ankadziwa kucheza ndi “anthu osiyanasiyana” ngakhale kuti anthuwo anali ndi chikhulupiriro chosiyana ndi chake. (1 Akorinto 9:22, 23) Inunso mungatsatire chitsanzo cha Paulo. Muzikhala bwino ndi anzanu. Muzilankhulana nawo bwino. Komabe musalole kuti mutengere kalankhulidwe ndi khalidwe loipa la anzanuwo. Musachedwe kuwauza chifukwa chimene mumatsatirira mfundo za m’Baibulo, ndipo auzeni zimenezi mwaulemu.—2 Timoteyo 2:25.
N’zoona kuti zimenezi zingakuchititseni kukhala wosiyana ndi anzanu, ndipo mwina simungasangalale nazo. (Yohane 15:19) Koma taganizirani izi. Ngati muli m’boti ndipo mukufuna kuti mupulumutse anthu amene akumira, kodi mungawathandize bwanji? Kodi mungatuluke m’botilo n’kudumphira m’madzimo? Ayi, simungachite zimenezo.
N’chimodzimodzinso kusukulu, mumakhala ndi anzanu omwe ndi osatetezeka chifukwa sadziwa Yehova. (Salmo 121:2-8) Ngati mutasiya kumvera malamulo a Yehova kuti anzanu azikukondani, ndiye kuti mungasiyenso kukonda Mulungu ndipo mungamakhale wosasangalala. (Aefeso 4:14, 15; Yakobe 4:4) Zingakhale bwino kwambiri ngati mutathandiza anzanuwo kuti ayambe kutumikira Yehova. Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti mumawakonda kwambiri anzanuwo.
LEMBA LOFUNIKA
‘Ndimachita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso kwa ena.’—1 Akorinto 9:23.
FUNDO YOTHANDIZA
Ngati anzanu a kusukulu akufuna kudziwa zimene mumakhulupirira, aloleni kuti nawonso afotokoze maganizo awo. Amvetsereni akamalankhula. Ndipo ‘ayankheni mofatsa ndi mwaulemu.’—1 Petulo 3:15.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Anthu ambiri amene akutumikira Mulungu masiku ano anaphunzira Baibulo kwa anzawo a kusukulu omwe analimba mtima n’kuwauza zimene amakhulupirira.
ZOTI NDICHITE
Ndikaona kuti ndayamba kucheza kwambiri ndi mnzanga wa kusukulu, ndizichita izi: ․․․․․
Mnzanga wa kusukulu akandinyoza chifukwa cha zimene ndimakhulupirira, ndizichita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani n’zosavuta kupeza anzanu ocheza nawo kusukulu kusiyana ndi kumpingo?
● Kodi kucheza kwambiri ndi mnzanu wa kusukulu yemwe si wa Mboni za Yehova n’koopsa motani?
● Kodi n’chifukwa chiyani muyenera kuuza anzanu a m’kalasi kuti ndinu wa Mboni za Yehova?
[Mawu Otsindika patsamba 143]
“Anthu ambiri kusukulu ankandikonda chifukwa choti ndinkakonda kutengera zochita zawo. Koma zimenezi zitandibweretsera mavuto, ndinadziwa kuti ndinkalakwitsa. Panopa ndimacheza ndi anthu a mumpingo mwathu ndipo ndimawadalira kwambiri.”—Anatero Daniel
[Chithunzi patsamba 146]
Kodi mungathandize bwanji mnzanu amene akumira? Kodi mungadumphire m’madzi momwemo, kapena mungamuponyere chubu chomuthandiza kuti aziyandama?