Nyimbo 14
Zinthu Zonse Zidzakhala Zatsopano
1. “Zizindikiro” zikusonyezadi
Kuti Yesu akulamulira.
Wapambana nkhondo ya kumwamba,
Posachedwa ayeretsa dziko.
(KOLASI)
Kondwa! Chifukwa Mulungu,
Alitu ndi anthu ake.
Sipadzakhalanso kulira,
Pena zopweteka ndi imfa;
Zidzakhala: ‘Zatsopano zonse.’
Mawuwa ndi oona.
2. Anthu aone Yerusalemuyo,
Mkwatibwi wa Mwanawankhosayo.
Atavala mochititsa chidwi,
Yehova ndiye kuwala kwake.
(KOLASI)
Kondwa! Chifukwa Mulungu,
Alitu ndi anthu ake.
Sipadzakhalanso kulira,
Pena zopweteka ndi imfa;
Zidzakhala: ‘Zatsopano zonse.’
Mawuwa ndi oona.
3. Mzindawu udzasangalatsa anthu.
Zipata zake sadzazitseka.
Anthu adzayenda muku’nika;
Atumikinu unikirani.
(KOLASI)
Kondwa! Chifukwa Mulungu,
Alitu ndi anthu ake.
Sipadzakhalanso kulira,
Pena zopweteka ndi imfa;
Zidzakhala: ‘Zatsopano zonse.’
Mawuwa ndi oona.
(Onaninso Mat. 16:3; Chiv. 12:7-9; 21:23-25.)