Nyimbo 82
Tsanzirani Khristu Pokhala Anthu Ofatsa
Losindikizidwa
1. Yesu anali woposa ’nthu onse.
Sanafune kutchuka, sananyade.
Anapatsidwa ntchito yofunika
Komabe anali wodzichepetsa.
2. Amene muli ndi mavuto nonse,
Goli lake akuti munyamule
Ndipo inu mudzatsitsimulidwa.
Ambuye wathu Yesu ndi wofatsa.
3. Anati: “Nonsenu ndinu abale.”
Musadzikweze, mutumikirane.
Ofatsa kwa M’lungu ndi ofunika,
Dziko lapansili adzalandira.
(Onaninso Mat. 5:5; 23:8; Miy. 3:34; Aroma 12:16.)