Mutu 1
“Ndaika Mawu Anga M’kamwa Mwako”
1, 2. N’chifukwa chiyani mumakhulupirira zimene mumawerenga m’Baibulo?
“PALI bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.” (Miy. 18:24) Kodi zimene mawu ouziridwawa akunena zinayamba zakuchitikirani? Mumakhulupirira zimene bwenzi lenileni lakuuzani. Munthu amene ndi bwenzi lanu lenileni akakuuzani zinthu zabwino kapena akakufotokozerani zimene akufuna kuchita, mumazikhulupirira. Akakuuzani zinthu zoti musinthe, mwina mumavomereza ndipo mumasinthadi. Mumachita zimenezi chifukwa iye wasonyeza kwa nthawi yaitali kuti amakufunirani zabwino, ngakhale pamene akukuuzani zinthu zimene mukufunika kusintha. Iyeyo amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Inunso mumafuna kuti iyeyo zinthu zizimuyendera bwino, ndipo zimenezi zimathandiza kuti ubwenzi wanu upitirire.
2 Anthu amene Mulungu anawagwiritsa ntchito polemba mabuku a m’Baibulo akhoza kukhala ngati mabwenzi oterowo kwa inu. Mungakhulupirire kuti zimene iwo akunena n’zoonadi komanso kuti zingakuthandizeni pa moyo wanu. Aisiraeli akale ankayenera kuwaona motero “anthu [amene] analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Pet. 1:20, 21) Mulungu anagwiritsa ntchito Yeremiya kuti alembe buku lalikulu kwambiri la ulosi m’Baibulo lodziwika ndi dzina lake, ndipo analembanso buku la Maliro ndi mabuku ena awiri.
3, 4. Kodi anthu ena amaona bwanji mabuku a Yeremiya ndi Maliro, koma n’chifukwa chiyani maganizo amenewo ali olakwika? Perekani chitsanzo.
3 Koma mwina munaona kuti anthu ena amene amawerenga Baibulo amapewa kuwerenga zimene Yeremiya analemba chifukwa amaona kuti n’zosasangalatsa. Mwina iwo amaganiza kuti m’mabuku a Yeremiya ndi Maliro muli machenjezo okhaokha komanso maulosi a zinthu zoopsa zimene zidzachitike m’tsogolo. Kodi umu ndi mmenedi tiyenera kuwaonera mabuku a Yeremiya ndi Maliro?
4 N’zoona kuti m’mabuku amene Yeremiya analemba muli machenjezo komanso uphungu wosapita m’mbali. Komabe mukudziwa kuti nthawi zina bwenzi lenileni lingafunikire kukuchenjezani mosapita m’mbali. Mwachitsanzo atumwi a Yesu, omwe analinso mabwenzi ake, akasonyeza maganizo olakwika, Yesu ankawadzudzula mosapita m’mbali. (Maliko 9:33-37) Koma uthenga waukulu wa Yesu unali wolimbikitsa, ndipo ankathandiza anthu kuti adziwe zimene angachite kuti Mulungu aziwakonda komanso kuti adzasangalale m’tsogolo. (Mat. 5:3-10, 43-45) N’chimodzimodzi ndi zimene Yeremiya analemba, zomwe zili mbali ya “Malemba onse” amene ndi opindulitsa pa “kuwongola zinthu.” (2 Tim. 3:16) Yeremiya ananena momveka bwino mmene Mulungu ankaonera anthu omwe ankanena kuti akutumikira Yehova, koma anali oyenera kulandira chilango chifukwa cha zoipa zimene ankachita. Komabe, m’mabuku a Yeremiya ndi Maliro muli uthenga wopatsa chiyembekezo ndiponso mfundo zofotokoza zimene tingachite kuti tidzapeze madalitso m’tsogolo. Yeremiya analemba maulosi onena za zinthu zosiyanasiyana zimene Mulungu adzachite, ndipo ifeyo masiku ano tikukwaniritsa nawo maulosi amenewo. Komanso m’mabuku awiri amenewa muli mawu osangalatsa ndi olimbikitsa.—Werengani Yeremiya 31:13, 33; 33:10, 11; Maliro 3:22, 23.
5. Kodi zimene Yeremiya analemba zingatithandize bwanji?
5 Zimene Yeremiya analemba zingatithandize kuti tizikhala osangalala m’gulu la anthu a Mulungu masiku ano, komanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo. Chitsanzo cha zimenezi ndi mgwirizano umene uli pakati pa abale padziko lonse. Mabuku amene Yeremiya analemba angatithandize kulimbitsa ubale wathu komanso kugwiritsa ntchito malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Abale, ndikuti pitirizani kukondwera, kusintha maganizo anu, kulimbikitsidwa, kukhala ndi maganizo ogwirizana, ndiponso kukhala mwamtendere. Mukatero, Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.” (2 Akor. 13:11) Zimene Yeremiya analemba zikugwirizananso kwambiri ndi uthenga umene timalalikira. Uthenga wathu ndi wosangalatsa komanso wopatsa chiyembekezo ngakhale kuti timauzanso anthu za masiku otsiriza ndi kuwachenjeza kuti dziko loipali litha posachedwapa. Komanso zimene Yeremiya analemba zingatithandize kwambiri pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Ndipo zimene zikutichitikira masiku ano zikufanana kwambiri ndi zimene zinkachitikira Yeremiya komanso zikufanana ndi zimene zili m’mauthenga ake. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tione mbiri ya mneneri wokhulupirika ameneyu komanso ntchito imene anapatsidwa. Ndipotu Mulungu anauza mneneriyu kuti: “Ndaika mawu anga m’kamwa mwako.”—Yer. 1:9.
6, 7. N’chifukwa chiyani tikukhulupirira kuti Mulungu anali ndi chidwi ndi Yeremiya, ndipo zinthu zinali bwanji mu Yuda pa nthawi imene iye anabadwa?
6 Makolo amene akuyembekezera kubadwa kwa mwana, kawirikawiri amaganizira za tsogolo la mwanayo. Iwo amadzifunsa kuti, kodi mwanayu adzakhala wotani, azidzakonda zinthu zotani, azidzagwira ntchito yanji ndipo zinthu zidzamuyendera bwanji? Makolo anu ayeneranso kuti anaganizirapo za inuyo mwanjira imeneyi. N’kutheka kuti zinalinso chimodzimodzi ndi makolo a Yeremiya. Komabe zimene zinachitika pa nkhani yokhudza Yeremiya zinali zosiyana ndi zimene zimachitikira ana ena. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti Mlengi wa chilengedwe chonse ankaganizira mwapadera zimene Yeremiya adzachite pa moyo wake.—Werengani Yeremiya 1:5.
7 Zoonadi, Yeremiya asanabadwe n’komwe, Mulungu anasankha kudziwiratu tsogolo la mwanayu. Iye anali ndi chidwi ndi Yeremiya, amene anadzabadwira m’banja la wansembe, limene linkakhala kumpoto kwa Yerusalemu. Mwanayu anabadwa chapakati pa zaka za m’ma 600 B.C.E., ndipo nthawi imeneyi inali yovuta ku Yuda chifukwa cha ulamuliro woipa wa Mfumu Manase. (Onani tsamba 19.) Manase analamulira kwa zaka 55 ndipo kwa zaka zambiri pa nthawi imeneyi, anachita zinthu zoipa pa maso pa Yehova. Kenako mwana wake Amoni, amene anamulowa m’malo, anachitanso chimodzimodzi. (2 Maf. 21:1-9, 19-26) Koma zinthu zinasintha kwambiri mu ulamuliro wa mfumu yotsatira ya Yuda. Mfumu imeneyi inali Yosiya, amene anafunafuna Yehova. Pofika m’chaka cha 18 cha ulamuliro wake, Yosiya anali atayeretsa dzikolo pothetsa kulambira mafano. Ndipo makolo a Yeremiya ayenera kuti anasangalala ndi zimenezi, chifukwa Mulungu anapatsa mwana wawoyu utumiki wapadera pa nthawi ya ulamuliro wa Yosiya.—2 Mbiri 34:3-8.
N’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi mabuku a Yeremiya ndi Maliro?
MULUNGU ANASANKHA WOMULANKHULIRA
8. Kodi Yeremiya anapatsidwa ntchito yotani, ndipo iye anatani?
8 Sitikudziwa kuti Yeremiya anali ndi zaka zingati pamene Mulungu anamuuza kuti: “Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.” Koma ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 25, zimene zinali zaka zoyenerera kuti munthu alowe m’gulu la ansembe otumikira pachihema. (Num. 8:24) Kaya anali ndi zaka zingati, Yeremiya anayankha kuti: “Haa! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindingathe kulankhula chifukwa ndine mwana.” (Yer. 1:6) Mwina iye ankakana ntchito imene anapatsidwayo poganiza kuti anali mwana kapena ankadziona kuti sanali woyenera kugwira ntchito yaikulu choncho. Komanso mwina ankaona kuti sangakwanitse kulankhula ndi anthu, ngati mmene ankachitira aneneri ena.
9, 10. Kodi zinthu zinali bwanji mu Yuda pamene Yeremiya ankayamba utumiki wake, koma n’chifukwa chiyani patapita nthawi utumiki wake unadzakhala wovuta?
9 Yeremiya anapatsidwa ntchitoyi pa nthawi imene Mfumu Yosiya ankathetsa kulambira konyenga, komwe kunali konyansa kwambiri, ndi kulimbikitsa kulambira koona. Sitikudziwa ngati Yeremiya ankachitira zinthu limodzi ndi Yosiya kapena ayi, koma n’zoonekeratu kuti imeneyi inali nthawi yabwino kwa mneneri woona aliyense. Nawonso Zefaniya ndi Nahumu, anali aneneri mu Yuda kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yosiya.a Pa nthawi yomweyi kunalinso mneneri wamkazi, dzina lake Hulida. Koma iye analosera zoti mtundu wa Ayuda ukumana ndi mavuto m’tsogolo, ndipo Yeremiya anaona mavuto amenewo akuchitika. (2 Maf. 22:14) Ndipotu nthawi zina Yeremiya anachita kupulumutsidwa ndi anzake monga Ebedi-meleki ndi Baruki kuti asaphedwe. Komanso nthawi zina anzakewa ankamuteteza kwa adani ofuna kumuchitira chiwembu.
10 Kodi mungamve bwanji Mulungu atakuuzani kuti wakupatsani ntchito yapadera kuti mukhale mneneri ndipo mukalengeze uthenga wamphamvu? (Werengani Yeremiya 1:10.) Tiyeni tione chitsanzo chimodzi cha uthenga umene Yeremiya ankafunikira kulengeza. Mu 609 B.C.E., asilikali a ku Babulo anayamba kuyandikira mzinda wa Yerusalemu. Mfumu Zedekiya ankafuna kuti Yeremiya amuuze uthenga womukomera wochokera kwa Mulungu. Koma uthenga umene Mulungu anapereka kwa Zedekiya sunali womukomera.—Werengani Yeremiya 21:4-7, 10.
ANALI MUNTHU NGATI IFE TOMWE
11. N’chifukwa chiyani mwina Yeremiya ankaona kuti n’zovuta kugwira ntchito imene anapatsidwa, komabe analimbikitsidwa bwanji?
11 Tayerekezerani kuti tikufunika kupereka uthenga wodzudzula mwamphamvu komanso wachiweruzo kwa mafumu oipa, ansembe achinyengo ndi kwa aneneri onyenga. Izi n’zimene Yeremiya ankafunika kuchita. Mulungu angatithandize ngati mmene anathandizira Yeremiya. (Yer. 1:7-9) Mulungu ankakhulupirira kuti Yeremiya amene anali wachinyamata, akwanitsa utumiki umene anamupatsa, ndipo anamulimbitsa mtima ndi mawu akuti: “Ine lero ndakusandutsa mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, mzati wachitsulo ndi makoma amkuwa kuti dziko lonseli lisakugonjetse. Ndithu kuti mafumu a Yuda, akalonga ake, ansembe ake ndi anthu a m’dzikoli asakugonjetse. Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzapambana, pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.’”—Yer. 1:18, 19.
12. N’chifukwa chiyani tingamvetse mosavuta mavuto amene Yeremiya anakumana nawo?
12 Tisaganize kuti Yeremiya anali munthu winawake wamphamvu kwambiri. Iye anali munthu ngati ife tomwe. Komanso tizikumbukira kuti Yeremiya anakumana ndi mavuto ofanana ndi amene ifenso tikukumana nawo masiku ano, ngakhale kuti iye anakhala ndi moyo zaka zambirimbiri zapitazo. Mofanana ndi Yeremiya, timachita zinthu ndi anthu osiyanasiyana pa moyo wathu watsiku ndi tsiku komanso pochita zinthu za kumpingo. Zonsezi zikusonyeza kuti tingaphunzire zambiri kwa Yeremiya, amene mofanana ndi mneneri Eliya, anali “munthu monga ife tomwe.” (Yak. 5:17) Tiyeni tione zitsanzo za zinthu zina zimene tingaphunzire kwa Yeremiya.
13, 14. N’chifukwa chiyani Akhristu ena amene akukumana ndi mavuto angamvetse bwino mmene Yeremiya ankamvera pozunzidwa ndi Pasuri, monga momwe chithunzi cha patsamba 10 chikusonyezera?
13 N’zachidziwikire kuti nanunso muyenera kuti mwakumanapo ndi zinthu zabwino komanso zokhumudwitsa pa moyo wanu. Yeremiya anakumananso ndi zinthu zotero. Pa nthawi ina, Pasuri, yemwe anali wansembe wotchuka, anamenya Yeremiya kenako n’kulamula kuti aikidwe m’matangadza. Kwa maola ambiri, mapazi, manja, ndiponso khosi lake zinamangidwa m’matangadzawo, ndipo iye ankamva ululu woopsa. Kuwonjezera pa ululuwo, anthu otsutsa ayenera kuti ankamunyoza pa nthawi imene iye anali m’matangadzamo. Kodi mukuganiza kuti inuyo mungathe kupirira pamene anthu akukunyozani, ngakhalenso kukumenyani?—Yer. 20:1-4.
14 Tikaganizira zowawa zonse zimene Yeremiya anakumana nazo, n’zosadabwitsa kuti iye ananena kuti: “Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa! . . . N’chifukwa chiyani ndinabadwa? Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni, ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?” (Yer. 20:14-18) Inde, panali zifukwa zomveka zimene zinachititsa Yeremiya kukhumudwa. Kodi inuyo munakhumudwapo kwambiri moti munayamba kudziona ngati wachabechabe? Kodi munayamba mwaganizapo kuti ntchito yonse yomwe mwagwira ilibe phindu lililonse, ndiponso kuti palibe ubwino uliwonse wopitirizira kutumikira Yehova? Anthu onse amene anakhalapo ndi maganizo oterewa angalimbikitsidwe poganizira zimene Yeremiya anakumana nazo, komanso mmene zinthu zinamuyendera pamapeto pake.
N’chiyani chimene chikukuchititsani chidwi mukaganizira ntchito imene Yehova anapatsa Yeremiya? N’chifukwa chiyani mungathe kumvetsa bwino zimene Yeremiya anakumana nazo?
15. Kodi kuganizira mfundo yakuti Yeremiya ankasinthasintha mmene ankamvera mumtima mwake kungatithandize bwanji?
15 Mneneri Yeremiya ananena mawu okhumudwa amene timawerenga pa Yeremiya 20:14-18 atangomaliza kumene kunena kuti anthu aimbire Yehova ndi kumutamanda. (Werengani Yeremiya 20:12, 13.) Kodi inunso nthawi zina mumasintha mofulumira kwambiri mmene mukumvera mumtima mwanu? Kodi zinakuchitikiranipo kuti munali wosangalala kwambiri, koma kenako munasintha mofulumira n’kukhala wokhumudwa? Mosakayikira, kuganizira mofatsa zimene zinachitikira Yeremiya kungatithandize tonsefe. Mmene Yeremiya ankamvera mumtima mwake zikuonetseratu kuti anali munthu ngati ife tomwe. Komabe Mlengi anamugwiritsira ntchito kwambiri monga womulankhulira. Choncho tingapindule kwambiri poganizira mofatsa zimene Yeremiya ankachita akakumana ndi zinthu zosiyanasiyana.—2 Mbiri 36:12, 21, 22; Ezara 1:1.
16. Kodi zimene Mulungu anauza Yeremiya pa nkhani ya ukwati zingakhale zothandiza kwa ndani?
16 Anthu ena amafanana ndi Yeremiya pa nkhani yokhudza ukwati. Kodi zinthu zinali bwanji ndi Yeremiya pa nkhani imeneyi? Mulungu anam’patsa malangizo odabwitsa komanso mwina ovuta kuwatsatira. Anamuuza kuti: Usakwatire. (Werengani Yeremiya 16:2.) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anauza Yeremiya zimenezi, ndipo zinamukhudza bwanji Yeremiyayo? Kodi mu nkhani imeneyi, muli mfundo yotani imene ingathandize abale ndi alongo amene sali pa banja, kaya mwakufuna kwawo kapena pa zifukwa zina? Komanso, kodi m’mawu omwe Mulungu anauza Yeremiya muli mfundo iliyonse imene anthu a Mboni amene panopa ali pa banja ayenera kuganizira mozama? Kodi mawu amenewa angathandize bwanji anthu amene ali pa banja koma alibe “ana aamuna kapena ana aakazi”? Kodi nkhani ya Yeremiya ingakuthandizeni bwanji inuyo?
17. Kodi mawu a mneneriyu, amene ali pa Yeremiya 38:20, angatichititse kuganizira za chiyani?
17 N’zochititsa chidwi kuti pa nthawi ina, Yeremiya anachonderera mfumu yomwe inkalamulira ku Yuda kuti: “Chonde, mverani mawu a Yehova amene ndikukuuzani. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino ndipo mudzakhalabe ndi moyo.” (Yer. 38:20) Nkhani imeneyi ikutipatsa chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi ena. Ena mwa anthu amenewa ndi amene sanayambe kutumikira Yehova, koma mwina tingathe kuwathandiza kuti ayambe kutero. Komanso, mmene Yeremiya ankachitira zinthu ndi anthu omwe ankamvera Mulungu, zikutipatsa chitsanzo chabwino masiku ano. Ndithudi, tingaphunzire zambiri kwa Yeremiya.
KODI M’BUKULI MULI ZOTANI?
18, 19. Kodi munthu akhoza kuphunzira mabuku a Yeremiya ndi Maliro m’njira zosiyanasiyana zotani?
18 Buku lino likuthandizani kuphunzira mosamala komanso kupindula ndi mabuku a m’Baibulo a Yeremiya ndi Maliro. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti mtumwi Paulo, mouziridwa ndi Mulungu, analemba kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.” (2 Tim. 3:16) Malemba amenewa akuphatikizapo mabuku a Yeremiya ndi Maliro.
19 Kuti munthu apindule ndi mabuku a Yeremiya ndi Maliro, akhoza kuwaphunzira m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, akhoza kuphunzira vesi lililonse la mabuku awiriwa, n’kuyesetsa kumvetsa tanthauzo lake ndiponso chifukwa chimene vesilo linalembedwera. Kapena, munthu angasankhe kuganizira kwambiri za anthu ndi zochitika za m’mabuku a Yeremiya ndi Maliro, n’kuziyerekezera ndi anthu komanso zochitika za masiku ano. (Yerekezerani ndi Yeremiya 24:6, 7; 1 Akorinto 3:6.) Njira ina ingakhale yofuna kudziwa mmene zinthu zinalili pa nthawi imene mabuku awiriwa ankalembedwa komanso zinthu zomwe zinkachitika pa nthawiyo. (Yer. 39:1-9) Ndipotu, kudziwa zina mwa zinthu zimenezi n’kofunika kuti munthu athe kumvetsa bwino mabuku a Yeremiya ndi Maliro. Choncho Mutu 2, wakuti “Kutumikira Mulungu ‘M’masiku Otsiriza,’” utithandiza kumvetsa bwino momwe zinthu zinalili m’masiku a Yeremiya ndiponso momwe Mulungu anayendetsera zinthu pa nthawiyo.
20. Kodi m’buku lino titsatira njira yotani yophunzirira mabuku a Yeremiya ndi Maliro?
20 Koma m’buku lino tiphunzira mabukuwa m’njira yosiyanako ndi njira zimenezi. Tiwatenga mabuku a Yeremiya ndi Maliro ngati mphatso zochokera kwa Mulungu zotithandiza pa moyo wathu monga Akhristu masiku ano. (Tito 2:12) Kuchita zimenezi kutithandiza kuzindikira kwambiri kuti mabuku awiriwa ali ndi mfundo zambiri ‘zopindulitsa pa kuphunzitsa.’ M’mabukuwa muli malangizo othandiza komanso zitsanzo zomwe zingatithandize kuti tikhale oyenerera bwino, ndiponso okonzeka pamene tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana pa moyo wathu. Ndipo angatithandize kaya sitili pa banja, tili pa banja, ndife akulu, apainiya, ndife amene timapezera banja lathu zinthu zofunika, ndife mayi yemwe sapita kuntchito, kapenanso mwina ndife mwana wa sukulu. M’mabuku awiri ouziridwawa, tonsefe tipezamo malangizo ochokera kwa Mulungu, amene angatithandize kukhala ‘okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Tim. 3:17.
21. N’chifukwa chiyani mukuyembekezera mwachidwi kuphunzira buku lino?
21 Mukamaphunzira mutu uliwonse m’buku lino, muzifufuza mfundo zimene mungazigwiritse ntchito pa moyo wanu. Sitikukayikira kuti mabuku a Yeremiya ndi Maliro atitsimikizira mfundo imene Paulo analemba, yakuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.
Kodi mungaphunzire chiyani m’mabuku a Yeremiya ndi Maliro, zimene zingakuthandizeni pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku?
a Chakumapeto kwa utumiki wa Yeremiya monga mneneri, kunalinso aneneri ena ngati: Habakuku, Obadiya, Danieli ndi Ezekieli. Pamene mzinda wa Yerusalemu unkawonongedwa mu 607 B.C.E., n’kuti Yeremiya atatumikira kwa zaka pafupifupi 40, ndipo anakhalabe ndi moyo zaka zoposa 20 mzindawu utawonongedwa.