Mutu 9
Pewani ‘Kufunafuna Zinthu Zazikulu’
1, 2. (a) Kodi Baruki anakumana ndi vuto lotani m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu? (b) Kodi Yehova anathandiza bwanji Baruki?
BARUKI anali mlembi wokhulupirika wa Yeremiya, koma pofika m’chaka chachinayi cha ulamuliro woipa wa Mfumu Yehoyakimu, kapena cha m’ma 625 B.C.E., iye anatopa. Mneneri Yeremiya anauza mlembiyu kuti alembe mumpukutu mawu onse amene Yehova ankauza mneneriyu okhudza mzinda wa Yerusalemu ndi Yuda. Iye anauza Baruki kuti alembe mawu onse amene Yehova anakhala akuuza Yeremiyayo pa zaka 23 zimene anali atachita utumiki wake monga mneneri kudzafika pa nthawiyo. (Yer. 25:1-3; 36:1, 2) Baruki sanawerengere Ayuda mawu a mumpukutuwo pa nthawiyo, koma anachita zimenezi m’chaka chotsatira. (Yer. 36:9, 10) Kodi panali chinachake chimene Baruki ankada nacho nkhawa?
2 Baruki anadandaula kuti: “Tsoka ine! pakuti Yehova wawonjezera chisoni pa zopweteka zanga. Ndatopa ndi kuusa moyo kwanga.” Mwina inunso nthawi ina munadandaulapo kuti mwatopa, kaya chamumtima kapena motulutsa mawu. Kaya Baruki anadandaula chamumtima kapena motulutsa mawu, Yehova ankamva. Mulungu, amene amadziwa za mumtima mwa munthu, ankadziwa chimene chinkachititsa Baruki kuda nkhawa, ndipo anamuthandiza mokoma mtima kudzera mwa Yeremiya. (Werengani Yeremiya 45:1-5.) Koma mwina mungafunse kuti, N’chifukwa chiyani Baruki anatopa choncho? Kodi anatopa ndi utumiki umene anapatsidwa kapena chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo pochita utumikiwo? Zikuoneka kuti vuto linali lochokera mumtima mwake, chifukwa iye ‘ankafunafuna zinthu zazikulu.’ Kodi ‘zinthu zazikuluzo’ zinali chiyani? Kodi Yehova anamulonjeza kuti akamvera malangizo ake adzam’patsa chiyani? Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Baruki?
KODI ‘ZINTHU ZAZIKULUZO’ ZINALI CHIYANI?
3. Kodi vuto lauzimu la Baruki linagona pati?
3 Baruki ayenera kuti ankadziwa kuti ‘zinthu zazikuluzo’ zinali chiyani. Mlembiyu ankadziwa kuti “maso [a Mulungu] amayang’anitsitsa njira za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse.” (Yobu 34:21) Utumiki umene Baruki ankachita, wolemba mawu aulosi amene Yeremiya ankamuuza, si umene unam’chititsa kuti aziona ngati alibe “malo ampumulo.” Vuto linali mumtima mwake, ndipo linali lokhudza zinthu zimene iye ankaona kuti n’zazikulu. Popeza kuti Baruki anayamba kufunafuna kwambiri “zinthu zazikulu,” anayamba kunyalanyaza zinthu zofunika kwambiri zokhudzana ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. (Afil. 1:10) Baibulo la Dziko Latsopano limafotokoza momveka bwino zimene Baruki ankachita, chifukwa linagwiritsa ntchito mawu akuti “ukufunafunabe.” Choncho sikuti Baruki anangoganizira ‘zinthu zazikuluzo’ kamodzi kokha ayi. Iye anali atayamba kale kufunafuna ‘zinthu zazikulu’ pamene Yehova ankamuchenjeza kuti asiye. Ngakhale kuti mlembi wokhulupirika wa Yeremiyayu ankachita nawo chifuniro cha Mulungu, pa nthawi yomweyomweyo ankalakalakanso “zinthu zazikulu.”
4, 5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti “zinthu zazikulu” zimene Baruki ankafuna mwina zinali zokhudza kutchuka, ndipo n’chifukwa chiyani chenjezo la Yehova linali loyenera?
4 N’kutheka kuti zinthu zazikulu zimene Baruki ankafuna zinali zokhudzana ndi kufuna kutchuka. Ngakhale kuti Baruki anali mlembi wa Yeremiya, n’kutheka kuti iye sanali mlembi wa Yeremiya yekha. Lemba la Yeremiya 36:32 limanena kuti Baruki ankagwira ntchito monga “mlembi,” ndipo ofufuza zinthu zakale apeza umboni wosonyeza kuti Baruki anali ndi udindo waukulu m’boma. Ndipotu winanso amene ankagwira ntchito imeneyi anali “Elisama mlembi,” yemwe anali m’gulu la akalonga a Yuda. Zimenezi zikusonyeza kuti Baruki nayenso ayenera kuti ankapita “kuchipinda chodyera cha mlembi” chimene chinali “kunyumba ya mfumu” chifukwa ankagwira ntchito limodzi ndi Elisama. (Yer. 36:11, 12, 14) Choncho zikuoneka kuti Baruki anali munthu wophunzira kwambiri ndipo ankagwira ntchito m’nyumba ya mfumu. M’bale wake Seraya anali mkulu woyang’anira zinthu za Mfumu Zedekiya ndipo anatsagana ndi mfumuyi pamene inkapita kukagwira ntchito yofunika kwambiri ku Babulo. (Werengani Yeremiya 51:59.) Monga mkulu woyang’anira zinthu za mfumu, Seraya anali ndi udindo waukulu kwambiri. Mfumuyo ikakhala pa ulendo Seraya ayenera kuti ankayang’anira katundu wa mfumu komanso ankakonza za malo ake ogona.
5 M’pomveka kuti munthu amene anazolowera kugwira ntchito yolemekezeka, akanatopa ndi ntchito yolemba mauthenga osiyanasiyana achiweruzo opita kwa Ayuda. Ndipotu Baruki akanatha kuchotsedwa pa udindo wake kapenanso kuchotsedwa ntchito kumene chifukwa chothandiza mneneri wa Mulungu. Komanso ganizirani zimene zikanam’chitikira ngati Yehova akanagwetsa chilichonse chimene Mulunguyo anamanga monga mmene lemba la Yeremiya 45:4 likunenera. “Zinthu zazikulu” zimene Baruki ankaziganizira zija, kaya ankafuna kuti azipatsidwa ulemu waukulu m’nyumba ya mfumu kapena ankafuna kulemera, sizikanam’thandiza. Ngati Baruki ankafuna udindo wina waukulu mu ulamuliro wa Ayuda umene pa nthawiyo unali utatsala pang’ono kutha, m’pomveka kuti Mulungu anamuchenjeza kuti achotse maganizo amenewo.
6, 7. Ngati “zinthu zazikulu” zimene Baruki ankafuna chinali chuma, kodi iye ayenera kuti anali ndi maganizo ati ofanana ndi a anthu ena pa nthawiyo?
6 Komanso n’kutheka kuti kupeza chuma chambiri n’chimodzi mwa “zinthu zazikulu” zimene Baruki ankafuna. Mayiko oyandikana ndi dziko la Yuda ankadalira kwambiri chuma ndi katundu wawo. Mwachitsanzo, mayiko a Mowabu komanso Amoni ankadalira ‘ntchito zawo ndi chuma chawo.’ Ndipo mouziridwa ndi Yehova, Yeremiya anafotokoza kuti Babulo anali ndi “chuma chochuluka.” (Yer. 48:1, 7; 49:1, 4; 51:1, 13) Komabe Mulungu anapereka chiweruzo choti mayikowa awonongedwe.
7 Choncho ngati Baruki ankafuna chuma kapena katundu wambiri, mungamvetse chifukwa chake Yehova anamuchenjeza kuti asakhale ndi maganizo amenewo. Mulungu ‘atatambasula dzanja lake ndi kuwononga’ Ayuda, nyumba zawo ndiponso minda yawo zinaperekedwa kwa adani awo. (Yer. 6:12; 20:5) Yerekezerani kuti munalipo pa nthawi ya Baruki ndipo munkakhala mumzinda wa Yerusalemu. Anthu ambiri m’dziko lanu, kuphatikizapo akalonga, ansembe komanso mfumu, akuona kuti ayenera kumenyana ndi Ababulo amene abwera kudzakuukirani. Koma inu mwamva uthenga wa Yeremiya wakuti: “Tumikirani mfumu ya Babulo kuti mukhale ndi moyo.” (Yer. 27:12, 17) Kodi kukhala ndi chuma chambirimbiri mumzindawo kukanakuthandizani kuti mumvere mosavuta lamulo la Mulunguli? Kodi poganizira za chuma chimenecho, mukanakhala wokonzeka kumvera chenjezo la Yeremiya limeneli kapena mukanangochita zimene anthu ambiri akuchita? Kumbukirani kuti Ababulo anatenga zinthu zonse zamtengo wapatali mu Yuda ndi mu Yerusalemu, kuphatikizapo za m’kachisi, n’kupita nazo ku Babulo. Choncho kufunitsitsa kupeza chuma kukanakhala kosathandiza. (Yer. 27:21, 22) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?
Kodi Yehova anathandiza bwanji Baruki mokoma mtima kuti asakhale ndi mtima wofunafuna “zinthu zazikulu”? N’chifukwa chiyani mukuona kuti n’chinthu chanzeru kumvera Mulungu akamatichenjeza?
“NDIDZAKUPATSA MOYO WAKO MONGA CHOFUNKHA CHAKO”
8, 9. N’chifukwa chiyani munganene kuti Baruki analandira mphatso yamtengo wapatali pamene analandira moyo wake monga chofunkha?
8 Tsopano ganizirani mfundo iyi: Kodi Baruki akanalandira chiyani chifukwa chomvera malangizo a Mulungu? Akanalandira moyo wake. Mulungu analonjeza Baruki kuti mulimonse mmene zingakhalire, adzamupatsa moyo “monga chofunkha” chake. (Werengani Yeremiya 45:5.) Pa nthawi imene mzinda wa Yerusalemu unkawonongedwa, anthu ochepa okha ndi amene anapulumuka. Kodi anthu ake anali ndani? Anthu amene anamvera malangizo a Mulungu oti adzipereke kwa Akasidi, ndi omwe anapulumuka. (Yer. 21:9; 38:2) Mwina ena angafunse kuti, ‘Kodi anthuwo anangopatsidwa zokhazo basi chifukwa cha kumvera kwawo?’
9 Kuti tiyankhe funso limeneli, ganizirani mmene zinthu zinalili mu Yerusalemu pa nthawi imene Ababulo anazungulira mzindawo. Anthu a mumzindawu anavutika koopsa chifukwa panapita nthawi yaitali adani atauzungulira. Izi n’zosiyana ndi zimene zinachitikira mzinda wa Sodomu umene unawonongedwa mofulumira kwambiri. Choncho tinganene kuti zinthu zinaliko bwino pamene mzinda wa Sodomu unkawonongedwa kusiyana ndi mmene zinalili pamene Yerusalemu ankawonongedwa. (Maliro 4:6) Baruki analemba ulosi wonena kuti anthu a mu Yerusalemu adzafa ndi lupanga, njala kapenanso miliri. Iye ayenera kuti anaona ulosi umenewu ukukwaniritsidwa. Chakudya chinatheratu mu Yerusalemu, ndipo zinali zochititsa mantha kwambiri kuona azimayi, omwe mwachibadwa ndi anthu “achifundo,” akuphika ana awo n’kumadya. (Maliro 2:20; 4:10; Yer. 19:9) Koma Baruki anapulumuka. Inde, pa nthawi yovutayi, moyo unali chofunkha kapena kuti unali ngati mphatso yoperekedwa kwa anthu opambana pa nkhondo. Baruki ayenera kuti anamvera malangizo a Mulungu akuti asafunefune “zinthu zazikulu.” Chifukwa cha zimenezi, Yehova anamudalitsa ndipo anapulumuka.—Yer. 43:5-7.
KODI INUNSO MUKUFUNAFUNA “ZINTHU ZAZIKULU”?
10, 11. Kodi nkhani ya Baruki ikugwirizana bwanji ndi zimene zikuchitika masiku ano komanso zimene zingakuchitikireni inuyo panokha?
10 Ngakhale kuti Baruki ankachita chifuniro cha Mulungu mwakhama, kwakanthawi ndithu ankalimbana ndi mtima wofuna “zinthu zazikulu.” Yehova anamuchenjeza kuti akapitiriza kufunafuna zinthu zazikulu adzakumana ndi mavuto, ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti apewe kufa mwauzimu komanso kutaya moyo wake. Mofanana ndi Baruki, ifenso tingayesedwe kwambiri ndipo mwina mtima wathu ungayambe kulakalaka kwambiri zinthu zinazake, ngakhale kuti tikutumikira Yehova mwakhama.
11 Baruki ayenera kuti ankavutika kwambiri ndi mtima wofuna kutchuka. Mwina nthawi zina ankadzifunsa kuti: ‘Kodi ndingatani kuti nditeteze ntchito yanga monga “mlembi”? Nanga ndingatani kuti andikweze pa ntchito?’ Kodi ifeyo zimenezi zingatichitikire? Dzifunseni kuti, ‘Kodi mumtimamu ndimalakalaka n’takhala pa ntchito yapamwamba m’dzikoli panopa kapena m’tsogolo?’ Achinyamata ena achikhristu angadzifunse kuti, ‘Kodi mtima wofuna kuphunzira kwambiri n’cholinga choti nditchuke kapena ndipeze chuma ungandichititse kuti ndiyambe kufunafuna “zinthu zazikulu”?’
12. Kodi m’bale wina anafunafuna bwanji zinthu zazikulu za Yehova, ndipo munganene chiyani pa zimene anasankha?
12 M’bale wina amene panopa akutumikira kulikulu la Mboni za Yehova la padziko lonse, anasankhidwa ali ndi zaka 15 kuti apite kuyunivesite ndipo anamulonjeza kuti adzamulipirira maphunziro akewo. Koma iye anakana kupita kuyunivesite n’kusankha ntchito ya upainiya, ndipo zimenezi zinakhumudwitsa kwambiri aphunzitsi ake. Komabe, iye anapitiriza kukonda kwambiri kuphunzira zinthu zatsopano. Choncho anapita kukakhala mmishonale pachilumba china chakutali. Kumeneko ankafunikira kuphunzira chinenero chimene chinkalankhulidwa ndi anthu opitirira pang’ono 10,000 okha. Pachilumbachi panalibe buku lotanthauzira mawu m’chinenero chimenechi, choncho anayamba kulemba yekha mawu ndi matanthauzo ake. Patapita nthawi, iye anadziwa chinenerochi ndipo anapatsidwa ntchito yomasulira mabuku athu ena. Kenako, pogwiritsira ntchito mawu ndi matanthauzo amene iye analemba aja, panasindikizidwa buku loyamba lotanthauzira mawu m’chinenero chimenechi. Nthawi inayake m’baleyu anauza anthu ambirimbiri pa msonkhano wachigawo kuti: “Ndikanavomera kupita kuyunivesite, zimene ndikanachita chifukwa cha maphunziro amenewo zikanangotchukitsa ineyo. Koma panopa ndimaonedwa kuti ndine munthu wosaphunzira, choncho sindilandira ulemu chifukwa cha zimene ndachita. Ulemerero wonse umapita kwa Yehova.” (Miy. 25:27) Kodi mukuganiza kuti zimene anasankha ali ndi zaka 15 zija zinali zanzeru? Kwa zaka zambiri, iye wachita zinthu zosiyanasiyana potumikira Mulungu pakati pa anthu ake. Kodi inuyo mukufuna kuti luso limene muli nalo mudzaligwiritse ntchito bwanji? Kodi mwatsimikiza ndi mtima wonse kuligwiritsa ntchito potamanda Yehova m’malo moligwiritsa ntchito pofuna kutchuka?
13. N’chifukwa chiyani makolo ena akuyenera kuganizira mofatsa za vuto limene Baruki anakumana nalo?
13 Pali chinthu chinanso choopsa chimene chingachitike: Munthu angayambe kufunafuna “zinthu zazikulu” chifukwa cha anthu amene amawakonda kapena angachite zimenezi kudzera mwa anthuwo. Ndipo nthawi zina angalimbikitse anthu amenewo kuti azifunafuna “zinthu zazikulu.” Mwina mwaonapo makolo ena m’dzikoli akuyesetsa kuthandiza mwana wawo kuti achite zambiri pa moyo wake kuposa zimene makolowo anachita. Mwinanso makolowo amafuna kuti mwana wawo adzakhale wotchuka n’cholinga choti iwowo azidzamunyadira. Mwina mwamva ena akunena kuti: “Sindikufuna kuti mwana wanga azidzagwira ntchito yowawa ngati yangayi” kapena “Ndikufuna kuti mwana wanga apite kuyunivesite kuti asadzavutike ngati mmene ndinavutikira ineyo.” Nawonso makolo achikhristu angakhale ndi maganizo amenewa. N’zoona kuti munthu anganene kuti, ‘Sikuti ndikufunafuna zinthu zazikulu ayi.’ Koma kodi n’kutheka kuti akuchita zimenezi mwakabisira, kudzera mwa munthu wina, monga mwana wake? Baruki ayenera kuti anayesedwa n’kuyamba kufuna kutchuka kudzera mu udindo kapena ntchito imene ankagwira. Chimodzimodzinso masiku ano, kholo lingayambe kufunafuna kutchuka kudzera mwa mwana wake. Koma kodi Mulungu, “amene amayesa mitima,” sangazindikire zimenezo ngati mmene anachitira ndi Baruki? (Miy. 17:3) Tiyeneratu kupempha Mulungu kuti asanthule mtima wathu, ngati mmene Davide anachitira. (Werengani Salimo 26:2; Yeremiya 17:9, 10.) Yehova angagwiritse ntchito njira zosiyanasiyana, monga nkhani ya Baruki imene tikukambiranayi, kuti atichenjeze za kuopsa kofunafuna “zinthu zazikulu.”
Kodi n’kutheka kuti Baruki ankafunafuna bwanji “zinthu zazikulu”? Kodi mukuphunzirapo chiyani pamenepa?
KUOPSA KODALIRA “ZINTHU ZAMTENGO WAPATALI”
14, 15. Kodi chuma chingakhale bwanji “zinthu zazikulu” kwa ife?
14 N’zotheka kuti “zinthu zazikulu” zimene Baruki ankafunafuna zinali chuma. Monga taonera kale, ngati Baruki akanakonda kwambiri zinthu zimene anali nazo ku Yuda, zikanamuvuta kwambiri kumvera lamulo la Mulungu lakuti adzipereke kwa Akasidi. Mwina inuyo munaona kuti munthu wolemera kawirikawiri amadalira “zinthu [zake] zamtengo wapatali.” Koma Baibulo limatitsimikizira kuti chitetezo chimene iye amapeza m’zinthu zimenezo chimangokhala cha “m’maganizo mwake.” (Miy. 18:11) Atumiki onse a Yehova zinthu zingawayendere bwino ngati atamadzikumbutsa kufunika koona chuma m’njira yoyenera monga mmene Mawu a Mulungu amanenera. (Werengani Miyambo 11:4.) Komabe, ena anganene kuti, ‘Kodi cholakwika n’chiyani ndi kukhala ndi zinthu za m’dzikoli n’kumasangalala nazo?’
15 Ngati Mkhristu atamakonda kwambiri chuma, angayambe kulakalaka zinthu za m’dziko losakhalitsali. Yeremiya ndi Baruki sanachite zimenezi. Ndipo patapita zaka zambiri, Yesu anachenjeza anthu amene adzakhale ndi moyo pa nthawi imene “Mwana wa munthu adzaonekera.” Yesu anawauza kuti: “Kumbukirani mkazi wa Loti.” Masiku anonso tingati Akhristu akuchenjezedwa kuti: ‘Kumbukirani Yeremiya ndi Baruki.’ (Luka 17:30-33) Ngati timakonda kwambiri chuma, zingativute kuti titsatire malangizo a Yesu amenewa. Koma musaiwale kuti Baruki atamvera chenjezo la Mulungu, anakhalabe ndi moyo.
16. Fotokozani zimene zinachitikira atumiki ena a Mulungu, zomwe zikusonyeza kuti iwo sankakonda kwambiri chuma.
16 Taganizirani mmene zinthu zinalili kwa abale athu m’dziko la Romania pa nthawi ya ulamuliro wachikomyunizimu. Akuluakulu a boma akamafufuza zinthu m’nyumba za anthu a Mboni, nthawi zina ankawalanda katundu wawo, makamaka zinthu zimene akuluakulu a bomawo akanatha kukagulitsa. (Maliro 5:2) Pa nthawi ya ulamuliro umenewu, abale ndi alongo ambiri analolera kuti katundu wawo alandidwe. Enanso anasiya katundu ndi chuma chawo pamene anasamutsidwa kwawo, komabe iwo anapitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wosagawanika. Kodi inuyo mutakumana ndi mayesero ngati amenewo mungakhalebe wokhulupirika kwa Mulungu, kapena mungalephere chifukwa chokonda kwambiri chuma?—2 Tim. 3:11.
17. Kodi anthu ena anathandiza bwanji Yeremiya ndi Baruki m’nthawi yawo?
17 N’zochititsa chidwi kuti Yeremiya ndi Baruki ankathandizidwa ndi anthu ena pa nthawiyo. Mwachitsanzo, Zefaniya anali mneneri pa nthawi ya ulamuliro wa Yosiya, pamene Yeremiya analinso mneneri. Kodi Yeremiya anaganiza chiyani atamva mawu amene tikuwapeza pa Zefaniya 1:18? (Werengani.) Yeremiya ayenera kuti anauza Baruki mfundo zouziridwa ndi Mulungu za palembali. Munthu wina amene anali mneneri pa nthawi ya Yeremiya anali Ezekieli amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo mu 617 B.C.E. Zimene ankachita komanso uthenga umene ankalengeza unkakhudza kwambiri Ayuda amene anatsala kwawo. Choncho Yeremiya ayenera kuti anamva uthenga wa Ezekieli ndipo nayenso Ezekieli ayenera kuti anamva uthenga wa Yeremiya. Umodzi mwa uthenga wa Ezekieli umene Yeremiya anamva ndi umene ukupezeka pa Ezekieli 7:19. (Werengani.) Mawu a palembali ayenera kuti anathandiza kwambiri Yeremiya ndi Baruki, ndipo ifenso angatithandize. Pa tsiku la Yehova anthu adzaitana milungu yawo kuti iwapulumutse, koma milunguyo kapenanso chuma chawo sichidzawapulumutsa.—Yer. 2:28.
KODI INUYO MUDZALANDIRA ‘MOYO WANU MONGA CHOFUNKHA CHANU’?
18. Kodi tingakonde kuti tidzalandire “moyo” wandani monga chofunkha, ndipo tingatani kuti tidzalandire moyo umenewu?
18 Tiyenera kukumbukira kuti Yehova watilonjeza kuti adzatipatsa “moyo” wathu monga chofunkha. Ngakhale atumiki ena a Mulungu atafa chifukwa chozunzidwa pa ‘chisautso chachikulu,’ pamene nyanga za chilombo zimene zikuimira magulu andale zidzaukire zipembedzo, atumiki okhulupirikawo adzalandirabe mphoto yawo. Sitikukayikira kuti iwo adzakhalanso ndi “moyo” ndipo adzasangalala ndi “moyo weniweniwo” m’dziko latsopano. (Chiv. 7:14, 15; 1 Tim. 6:19) Koma n’zodziwikiratu kuti atumiki ambiri a Mulungu amene adzakhalebe okhulupirika pa nthawi imeneyo adzatuluka m’chisautso chachikulu. Choncho simuyenera kukayikira kuti Mulungu akamadzawononga anthu a mitundu yonse, sipadzapezeka mtumiki wake wokhulupirika amene adzakhale m’gulu la “anthu ophedwa ndi Yehova.”—Yer. 25:32, 33.
Sankhani zinthu zomwedi n’zamtengo wapatali (Yerekezerani ndi tsamba 46.)
19. Kodi kukambirana chitsanzo cha Yeremiya ndi Baruki kwakuthandizani bwanji kuti mukhale wotsimikiza ndi mtima wonse kupewa kufunafuna “zinthu zazikulu”?
19 Ena angakhumudwe akaganiza kuti adzapulumuka ndi “moyo” wawo wokha monga chofunkha, komatu zimenezo siziyenera kutikhumudwitsa. Kumbukirani kuti pamene anthu a mu Yerusalemu ankafa ndi njala, Yehova anapulumutsa Yeremiya. Kodi anamupulumutsa bwanji? Mfumu Zedekiya anamanga Yeremiya n’kumutsekera m’Bwalo la Alonda ndipo ankamupatsa “mtanda wobulungira wa mkate tsiku ndi tsiku. Mkate umenewu unali kuchokera kumsewu wa ophika mkate ndipo anapitiriza kum’patsa mkatewo kufikira mkate wonse utatha mumzindamo.” (Yer. 37:21) Zimenezi zinathandiza kuti Yeremiya asafe ndi njala, ndipo zikusonyeza kuti Yehova angagwiritse ntchito njira iliyonse imene wasankha pothandiza anthu ake. Ndipo tikudziwa kuti Mulungu adzathandizadi anthu ake, chifukwa wawatsimikizira kuti adzawapatsa moyo wosatha. Baruki anapulumuka pamene mzinda wa Yerusalemu unkawonongedwa chifukwa anasiya ‘kufunafuna zinthu zazikulu.’ Ifenso tikuyembekezera kudzapulumuka pa Aramagedo ndi kutamanda Yehova titalandira “moyo” wathu monga chofunkha chimene tidzasangalale nacho kwamuyaya.
N’chifukwa chiyani n’chinthu chanzeru masiku ano kupewa kufunafuna “zinthu zazikulu,” n’kumachita zinthu zimene zingatithandize kudzalandira “moyo” wathu monga chofunkha?