Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 4 tsamba 10-11
  • Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Moyo Unali Wotani m’Paradaiso?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Chigawo 4
    Mverani Mulungu
  • Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kufa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 4 tsamba 10-11

CHIGAWO 4

Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana?

Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, choncho anafa. Genesis 3:6, 23

Hava akudya chipatso choletsedwa kenako akupatsa Adamu

Hava anamvera njoka ndipo anadya chipatso cha mtengo woletsedwawo. Atatero, anatengako chipatso china n’kukapatsa mwamuna wake Adamu, ndipo iyenso anadya.

Adamu ndi Hava akutuluka m’Paradaiso

Zimene anachitazo zinali zolakwika chifukwa linali tchimo. Zitatero Mulungu anawathamangitsa m’Paradaiso mmene iwo ankakhala.

Adamu ndi Hava anakalamba kenako kufa

Iwo pamodzi ndi ana awo anayamba kukhala moyo wovutika kwambiri. Kenako, iwo anakalamba n’kufa. Iwo atafa, sanapite kudziko lamizimu ayi, chifukwa mwa munthu mulibe chilichonse chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira.

Munthu akafa amangokhala ngati fumbi. Genesis 3:19

Anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana pa nthawi yosiyanasiyana

Tonsefe timafa chifukwa ndife ana a Adamu ndi Hava. Anthu akufa sangathe kuchita chilichonse monga kumva kapena kuona.​—Mlaliki 9:5, 10

Mtsikana wamwalira ndipo abale ake akulira

Sichinali cholinga cha Yehova kuti anthu azifa. Choncho, posachedwapa iye adzaukitsa anthu onse amene anamwalira. Anthu amenewo akadzamvera Mulungu, adzakhala ndi moyo wosatha.

  • N’chifukwa chiyani timafa?​—Aroma 5:12.

  • Imfa sidzakhalaponso.​—1 Akorinto 15:26.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena