Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 12 tsamba 26-27
  • Kodi Mungatani Kuti Aliyense M’banja Mwanu Azisangalala?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Kuti Aliyense M’banja Mwanu Azisangalala?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Moyo wa Banja Umene Umakondweretsa Mulungu
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Makiyi Aŵiri a Ukwati Wokhalitsa
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Chigawo 12
    Mverani Mulungu
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 12 tsamba 26-27

CHIGAWO 12

Kodi Mungatani Kuti Aliyense M’banja Mwanu Azisangalala?

Chikondi n’chofunika kwambiri kuti aliyense m’banja akhale wosangalala. Aefeso 5:33

Adamu ndi Hava ali m’munda wa Edeni

Zimene Mulungu amafuna pa nkhani ya ukwati n’zakuti mwamuna akhale ndi mkazi mmodzi komanso mkazi akhale ndi mwamuna mmodzi.

Mwamuna akusamalira mkazi wake amene akudwala; mkazi akukonzera mwamuna wake chakudya

Mwamuna wachikondi amakomera mtima mkazi wake ndiponso amamumvetsa.

Mkazi ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi mwamuna wake.

Bambo akulimbikitsa mwana wake kuti azimvetsera pamisonkhano

Ana ayenera kumvera makolo awo.

Khalani okoma mtima ndiponso okhulupirika, osati ankhanza. Akolose 3:5, 8-10

Makolo akuphunzitsa mwana wawo mfundo za m’Baibulo

Mawu a Mulungu amanena kuti mwamuna azikonda mkazi wake ngati mmene amakondera thupi lake, ndiponso kuti mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.

Mkazi wakhumudwa chifukwa choti mwamuna wake akuyang’ana mosirira mkazi wina

Kugonana ndi munthu amene si mkazi kapena mwamuna wanu n’kulakwa. Kukwatira mitala n’kulakwanso.

Banja likuyang’ana dzuwa likulowa

Mawu a Yehova ali ndi mfundo zimene zingathandize mabanja kukhala osangalala.

  • Yesetsani kukhala ndi khalidwe labwino mwa kupewa dama.​—1 Akorinto 6:18.

  • Muzikonda ana anu, muziwaphunzitsa ndiponso muziwateteza.​—Deuteronomo 6:4-9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena