Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp1 tsamba 287
  • Chitsanzo Chabwino—Timoteyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino—Timoteyo
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Nkhani Yofanana
  • Timoteo—‘Mwana Weniweni m’Chikhulupiriro’
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Mwana Wanga Wokondedwa Ndi Wokhulupirika Mwa Ambuye”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Paulo, Sila ndi Timoteyo
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Timoteyo Anali Wokonzeka Komanso Wofunitsitsa Kutumikira
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
yp1 tsamba 287

Chitsanzo Chabwino​—Timoteyo

Timoteyo ali ndi zaka pafupifupi 20 anali wokonzeka kuchoka pakhomo pa makolo ake, osati pothawa zochitika za pakhomopo, koma kuti azikagwira ntchito ya umishonale limodzi ndi mtumwi Paulo. Pa msinkhu umenewu n’kuti Timoteyo ali kale ndi udindo chifukwa “abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anamuchitira umboni wabwino.” (Machitidwe 16:2) Paulo ankakhulupirira kuti Timoteyo akhoza kuchita zambiri potumikira Mulungu, ndipo n’zimenedi anachita. M’zaka zotsatira Timoteyo anayenda m’madera ambiri n’kumakhazikitsa mipingo komanso kulimbikitsa abale. Makhalidwe abwino amene Timoteyo anali nawo anapangitsa kuti Paulo azimukonda ndipo patapita zaka 11, Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: “Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima.”​—Afilipi 2:20.

Kodi inuyo mukuchita zinthu zosonyeza kuti mukufuna kuti muzigwiritsidwa ntchito? Ngati mukufunitsitsa kutumikira Mulungu, dziwani kuti mudzapeza madalitso ambiri. Yehova amakonda kwambiri achinyamata amene ‘amadzipereka mofunitsitsa.’ (Salimo 110:3) Komanso simuyenera kukayikira zoti Yehova Mulungu “si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu.”​—Aheberi 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena