Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fg phunziro 1 mafunso 1-3
  • Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?
  • Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzitsidwa ndi Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mulungu Analengeranji Dziko Lapansili?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mulungu Ali ndi Cholinga Chotani Chokhudza Dziko Lapansili?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
fg phunziro 1 mafunso 1-3

PHUNZIRO 1

Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

1. Kodi Mulungu akutiuza uthenga wotani?

Anthu akusangalala padziko lapansi

Mulungu akufuna kuti anthu azisangalala ndi moyo padziko lapansi pano. Iye analenga dziko lapansi ndi chilichonse chimene chili m’dzikoli chifukwa chakuti amakonda anthu. Posachedwapa Mulungu adzachotsa zinthu zonse zimene zikuyambitsa mavuto pakati pa anthu kuti anthu m’dziko lililonse azikhala mosangalala.​—Werengani Yeremiya 29:11.

Palibe boma limene lakwanitsa kuthetsa chiwawa, matenda kapena imfa. Komabe pali uthenga wabwino. Uthenga wake ndi wakuti posachedwapa, Mulungu athetsa maboma onse a anthu ndipo m’malo mwake akhazikitsa boma lake. Anthu amene azidzalamuliridwa ndi boma la Mulungu adzakhala mwamtendere komanso adzakhala ndi thanzi labwino.​—Werengani Yesaya 25:8; 33:24; Danieli 2:44.

2. N’chifukwa chiyani uthenga wabwino ukufunika kulengezedwa mwamsanga?

Mavuto amene anthu akukumana nawo sangathe pokhapokha Mulungu atachotsa anthu oipa padziko lapansi. (Zefaniya 2:3) Ndiyeno kodi anthu oipawo adzawachotsa liti padzikoli? Mawu a Mulungu analosera za mavuto amene anthu akukumana nawo masiku ano. Choncho, zinthu zoipa zimene zikuchitikazi ndi umboni wakuti nthawi yoti Mulungu awononge oipa ili pafupi kwambiri.​—Werengani 2 Timoteyo 3:1-5.

3. Kodi tikuyenera kuchita chiyani?

Tiyenera kuphunzira za Mulungu kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Baibulo lili ngati kalata imene bambo wachikondi walembera ana ake. Bukuli limatiuza zoyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino panopa, komanso kuti tidzapeze moyo wosatha padziko lapansi m’tsogolo muno. N’zoona kuti anthu ena atakuonani mukuphunzira Baibulo kuti mulimvetse bwino, sangasangalale. Koma musalole kuti wina aliyense akulepheretseni kuphunzira Mawu a Mulungu amene angakuthandizeni kudzapeza moyo wosatha m’tsogolo.​—Werengani Miyambo 29:25; Chivumbulutso 14:6, 7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena