Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fg phunziro 6 mafunso 1-5
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?
  • Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Akufa Adzauka?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Munthu Amene Anali Wakufa Masiku Anai
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Kodi Chimachitika ndi Chiyani Tikamwalira?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Chimachitika Nchiyani pa Imfa?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
fg phunziro 6 mafunso 1-5

PHUNZIRO 6

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?

1. Kodi pali uthenga wabwino wotani wokhudza anthu amene anamwalira?

Malita ndi Mariya akulandira m’bale wawo Lazaro yemwe waukitsidwa

Pamene Yesu ankafika m’tauni ya Betaniya, yomwe inali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu, panali patadutsa masiku anayi mnzake Lazaro atamwalira. Kenako Yesu pamodzi ndi Malita ndi Mariya, omwe anali azichemwali ake a Lazaro, anapita kumanda kumene mchimwene wawoyo anaikidwa. Posapita nthawi, kumandako kunadzaza anthu. Kenako Yesu anaukitsa Lazaro, ndipo mukhoza kuona m’maganizo mwanu chisangalalo chimene Malita ndi Mariya anali nacho ataona kuti m’bale wawo waukitsidwa.​—Werengani Yohane 11:21-24, 38-44.

Malita anali akudziwa kale za uthenga wabwino wokhudza anthu amene anamwalira. Iye ankadziwa kuti Yehova adzaukitsa akufa ndipo adzakhalanso ndi moyo padziko lapansili.​—Werengani Yobu 14:14, 15.

2. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

Adamu akulengedwa, kenako atamwalira

Mulungu anauza Adamu kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”—GENESIS 3:19.

Anthu anapangidwa kuchokera kufumbi. (Genesis 2:7; 3:19) Anthufe si mizimu imene ikukhala m’matupi okhala ndi minofu. Koma ndife zolengedwa zooneka, zokhala ndi thupi, ndipo mkati mwathu mulibe chinthu chomwe chimapitirizabe kukhala ndi moyo tikamwalira. Munthu akamwalira, ubongo wake umafanso, ndipo zinthu zonse zimene ankaganiza zimathera pomwepo. N’chifukwa chaketu Lazaro sananene chilichonse chokhudza zimene zinkamuchitikira pa nthawi imene anamwalira, popeza munthu akafa sadziwa chilichonse.​—Werengani Salimo 146:4; Mlaliki 9:5, 6, 10.

Kodi anthu oipa akamwalira, Mulungu amawawotcha ndi moto? Popeza Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti munthu akafa sadziwa chilichonse, mfundo yakuti Mulungu amawotcha anthu ndi yabodza, ndipo imangochititsa kuti anthu aziimba Mulungu mlandu wa zinthu zimene iye sachita n’komwe. Ndipotu Mulungu amanyansidwa kwambiri anthu akamazunza anzawo powawotcha ndi moto kapena akamamunamizira kuti iye amachita zimenezi.​—Werengani Yeremiya 7:⁠31.

Onerani vidiyo yakuti Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

3. Kodi anthu amene anamwalira angathe kulankhula nafe?

Anthu akufa sangalankhule kapena kumva. (Salimo 115:17) Komabe pali angelo ena oipa ndipo amalankhula ndi anthu ponamizira kuti ndi anthu amene anamwalira. (2 Petulo 2:4) Ndipotu Yehova amaletsa kulankhula ndi anthu akufa.​—Werengani Deuteronomo 18:10, 11.

4. Kodi ndi anthu ati amene adzaukitsidwe?

Munthu amene waukitsidwa m’Paradaiso akuphunzira za Mulungu. Kenako munthuyo akuphunzitsa anthu ena amene nawonso aukitsidwa.

Anthu mamiliyoni ambirimbiri amene ali m’manda adzauka n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi. Ngakhalenso anthu ena amene sankamudziwa Mulungu ndipo ankachita zoipa adzaukitsidwa.​—Werengani Luka 23:43; Machitidwe 24:15.

Anthu amene adzaukitsidwe adzakhala ndi mwayi woti aphunzire za Mulungu ndi kusonyeza kuti akukhulupirira Yesu pomumvera. (Chivumbulutso 20:11-13) Oukitsidwawo akamadzachita zinthu zabwino adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Werengani Yohane 5:28, 29.

5. Kodi mfundo yakuti akufa adzaukitsidwa ikutiuza chiyani za Yehova?

N’zotheka kuti akufa adzaukitsidwe chifukwa Mulungu anatumiza Mwana wake kudzatifera. Choncho tikaganizira mfundo imeneyi timaona kuti Yehova ndi wachikondi komanso kukoma mtima kwake n’kwakukulu. Kodi akufa akadzauka, inuyo mukufunitsitsa kudzaonana ndi ndani?​—Werengani Yohane 3:16; Aroma 6:23.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 6, 7 ndi 10 m’buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena