Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fg phunziro 13 mafunso 1-4
  • Kodi Pali Uthenga Wabwino Wotani Wokhudza Zipembedzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Uthenga Wabwino Wotani Wokhudza Zipembedzo?
  • Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi N’chiyani Chidzachitikire Zipembedzo?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Zipembedzo Zonyenga Zimaphunzitsa Zabodza Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Pewani Kulambira Konyenga!
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
fg phunziro 13 mafunso 1-4

PHUNZIRO 13

Kodi Pali Uthenga Wabwino Wotani Wokhudza Zipembedzo?

1. Kodi zipembedzo zonse n’zabwino?

Munthu akuwerenga Baibulo

M’zipembedzo zonse mumapezeka anthu ena oona mtima. Uthenga wabwino ndi wakuti Mulungu amaona anthu oterowo ndipo amawakonda. Komabe, chomvetsa chisoni n’chakuti anthu akugwiritsa ntchito chipembedzo pochita zinthu zoipa. (2 Akorinto 4:3, 4; 11:13-15) Mogwirizana ndi zimene malipoti ena amanena, zipembedzo zina zafika poyamba kuchita nawo zauchigawenga, kupha anthu ambirimbiri nthawi imodzi, kulowerera nkhondo komanso kuchitira ana nkhanza. Zimenezi zimakhumudwitsa kwambiri anthu amene amakhulupirira Mulungu moona mtima.​—Werengani Mateyu 24:3-5, 11, 12.

Pamene chipembedzo choona chikulemekeza Mulungu, chipembedzo chonyenga chikuchita zinthu zosamusangalatsa. Chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa mfundo zosachokera m’Baibulo, monga ziphunzitso zabodza zokhudza Mulungu ndiponso zimene zimachitika munthu akafa. Koma Yehova akufuna kuti anthu adziwe zoona zokhudza iyeyo.​—Werengani Ezekieli 18:4; 1 Timoteyo 2:3-5.

2. Kodi pali uthenga wabwino wotani wokhudza zipembedzo?

Mulungu sapusistidwa ndi zipembedzo zomwe zimanena kuti zimamukonda pamene kwenikweni zimakonda dziko la Satanali. (Yakobo 4:4) Mawu a Mulungu amanena kuti zipembedzo zonse zonyenga zimatchedwa “Babulo Wamkulu.” Dzina limeneli linachokera pa dzina la mzinda wakale wa Babulo, kumene chipembedzo chonyenga chinayambira pambuyo pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa. Posachedwapa, Mulungu awononga zipembedzo zonyenga zomwenso zimachitira anthu nkhanza.​—Werengani Chivumbulutso 17:1, 2, 5, 16, 17; 18:8.

Palinso uthenga wina wabwino. Yehova sanaiwale anthu oona mtima amene ali m’zipembedzo zonyenga padziko lonse, omwe akufunitsitsa kumulambira. Iye akugwirizanitsa anthu amenewa powaphunzitsa choonadi.​—Werengani Mika 4:2, 5.

3. Kodi anthu amene akufunadi kulambira Mulungu woona ayenera kuchita chiyani?

Anthu akucheza misonkhano yachikhristu itatha

Chipembedzo choona chikugwirizanitsa anthu

Yehova amakonda anthu amene amakonda choonadi komanso amene amakonda zinthu zabwino. Iye akuwalimbikitsa kuti achoke m’chipembedzo chonyenga. Anthu amene amakonda Mulungu akusinthadi mofunitsitsa kuti akondweretse Mulunguyo.​—Werengani Chivumbulutso 18:4.

Mu nthawi ya atumwi, anthu a mitima yabwino anasangalala kwambiri atamva uthenga wabwino womwe atumwiwo ankalalikira. Iwo anaphunzira zinthu zatsopano kuchokera kwa Yehova, n’kuyamba kukhala ndi moyo wosangalala komanso ali ndi chiyembekezo chabwino. Anthu amenewa ndi chitsanzo chabwino kwa ife masiku ano chifukwa anamvera uthenga wabwino ndipo anachita zimenezi posonyeza kuti kumvera Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wawo.​—Werengani 1 Atesalonika 1:8, 9; 2:13.

Yehova akulandira anthu onse amene achoka kuchipembedzo chonyenga kuti akhale limodzi ndi anthu amene amamulambira. Mukamvera Yehova n’kubwera m’gulu lake, mudzakhala naye pa ubwenzi, mudzapeza anthu okukondani omwe muzidzalambira nawo Yehova komanso mudzapeza moyo wosatha.​—Werengani Maliko 10:29, 30; 2 Akorinto 6:17, 18.

4. Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti padziko lonse anthu akhale osangalala?

Zoti chipembedzo chonyenga chiwonongedwa posachedwapa ndi uthenga wabwino. Zimenezi zidzachititsa kuti anthu asamaponderezedwenso padziko lonse. Ndipo chipembedzo chonyenga sichidzasocheretsa anthu komanso kuwagawanitsa. Anthu onse adzagwirizana polambira Mulungu woona mmodzi.​—Werengani Chivumbulutso 18:20, 21; 21:3, 4.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 ndi 16, m’buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena