Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yc phunziro 2 tsamba 6-7
  • Rabeka Ankafuna Kusangalatsa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Rabeka Ankafuna Kusangalatsa Yehova
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Yofanana
  • Rabeka Anali Wofunitsitsa Kukondweretsa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
  • “Inde Ndipita”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kupezera Isake Mkazi
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Rebeka Anali Mkazi Wolimbikira Ntchito Ndiponso Woopa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Phunzitsani Ana Anu
yc phunziro 2 tsamba 6-7

PHUNZIRO 2

Rabeka Ankafuna Kusangalatsa Yehova

Rabeka ankakonda Yehova. Mwamuna wake anali Isaki ndipo nayenso ankakonda Yehova. Kodi ukudziwa kuti Rabeka anakumana bwanji ndi Isaki? Nanga Rabeka anasonyeza bwanji kuti ankafuna kusangalatsa Yehova? Tiye tione zimene zinachitika.

Makolo ake a Isaki anali Abulahamu ndi Sara. Iwo ankakhala m’dziko la Kanani ndipo anthu a kumeneko sankalambira Yehova. Koma Abulahamu ankafuna kuti mwana wake adzakwatire mkazi wolambira Yehova. Choncho anatuma wantchito wake Eliezere kuti apite ku Harana kuti akapezere Isaki mkazi. Ku Harana n’kumene kunkakhala abale ake a Abulahamu.

Rabeka anapita ndi Eliezere kuti akakwatiwe ndi Isaki

Eliezere anayenda ulendowu ndi antchito ena a Abulahamu. Ulendowu unali wautali kwambiri. Anatenga ngamila 10 zomwe zinanyamula zakudya ndi mphatso. Koma kodi Eliezere akanasankha bwanji mtsikana woti akakhale mkazi wa Isaki? Atafika ku Harana, Eliezere ndi antchito ena aja anaima pachitsime chifukwa ankadziwa kuti sipapita nthawi yaitali anthu asanabwere kudzatunga madzi. Ndiyeno anapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti, ‘Ndikapempha mtsikana kuti andipatseko madzi oti ndimwe, iye n’kundipatsa komanso n’kumwetsa ngamilazi, ndidziwa kuti mtsikana ameneyo ndi amene mwamusankha.’

Kenako Rabeka anafika pachitsimepo. Baibulo limanena kuti Rabeka anali wokongola kwambiri. Eliezere anamupempha madzi ndipo anayankha kuti: ‘Eni imwani. Nditungiranso madzi ngamila zanu.’ Tangoganiza, kutungira madzi ngamila zimene zinali ndi ludzu kwambiri. Pamenepatu Rabeka anafunika kuyenda maulendo ambirimbiri kuti atunge madzi okwanira ngamila zonsezo. Kodi ukuona zimene akuchita pachithunzipo?— Eliezere anadabwa kwambiri ndi mmene Yehova anayankhira pemphero lake.

Eliezere anam’patsa Rabeka mphatso zambirimbiri. Rabeka anaitanira Eliezere ndi antchito ena aja kunyumba kwawo. Atafika, Eliezere anafotokoza chifukwa chimene Abulahamu anamutumira kumeneko komanso mmene Yehova anayankhira pemphero lake. Abale ake a Rabeka anagwirizana ndi zoti Rabeka akakhale mkazi wa Isaki.

Rabeka anayenda maulendo ambirimbiri kuti atunge madzi okwanira ngamila zonse

Kodi ukuganiza kuti Rabeka ankafunadi kukwatiwa ndi Isaki?— Rabeka ankadziwa kuti Yehova ndi amene analondolera Eliezere kuti afike kwawo. Ndiyeno abale ake a Rabeka atamufunsa ngati akufuna kupita ku Kanani kuti akakhale mkazi wa Isaki, iye anayankha kuti: “Inde ndipita.” Nthawi yomweyo ananyamuka limodzi ndi Eliezere. Atafika ku Kanani, anakwatiwa ndi Isaki.

Yehova anadalitsa Rabeka chifukwa chakuti anachita zimene Yehovayo ankafuna. Moti patapita zaka zambiri, zidzukulu za Rabeka zinabereka Yesu. Iwenso Yehova akhoza kukudalitsa ngati utamachita zinthu zomusangalatsa ngati mmene Rabeka anachitira.

WERENGANI MAVESI AWA

  • Genesis 12:4, 5; 24:1-58, 67

MAFUNSO:

  • Kodi Rabeka anali ndani?

  • N’chifukwa chiyani Abulahamu sankafuna kuti Isaki akwatire mkazi wa ku Kanani?

  • Kodi Eliezere anasankha bwanji Rabeka kuti akhale mkazi wa Isaki?

  • Kodi tingatani kuti tifanane ndi Rabeka?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena