Kumanzere: Thandizo lochokera ku Switzerland lopita kwa abale athu ku Germany, mu 1946; Kumanja: Kumanganso Nyumba ya Ufumu ku Japan pambuyo pa kusefukira kwa madzi, mu 2011
GAWO 6
Thandizo Limene Ufumuwu Umapereka—Kumanga Malo Olambirira Komanso Kuthandiza pa Nthawi ya Mavuto
TAYEREKEZERANI kuti mwalowa mu Nyumba ya Ufumu yanu koma n’kupeza kuti chilichonse chasinthiratu. Mwakhala mukunyadira chifukwa chokhala ndi nyumba imeneyi ndipo mwina mumakumbukira zinthu zina zosangalatsa zimene zinkachitika pa nthawi imene munkagwira nawo ntchito yomanga nyumbayo. Koma panopa ndinu osangalala kwambiri chifukwa chakuti Nyumba ya Ufumuyo yasintha n’kukhala malo othandizirako anthu pa nthawi ya mavuto. Chifukwa cha mvula ya mphepo yomwe yachititsa kuti madzi asefukire m’dera lanulo, Komiti ya Nthambi yakonza zoti anthu amene akhudzidwa ndi vutoli alandire chakudya, zovala, madzi ndiponso zinthu zina. Katunduyo akusanjidwa mwadongosolo ndipo abale ndi alongo akubwera mu Nyumba ya Ufumuyo kudzalandira zinthu zofunikira kwinaku akutuluka misozi yachisangalalo.
Yesu ananena kuti anthu ake azidzadziwika chifukwa chokondana. (Yoh. 13:34, 35) M’chigawochi tikambirana mmene Mboni za Yehova zimasonyezerana chikondi chimenechi pa ntchito zomangamanga komanso kuthandizana pa nthawi ya mavuto. Kusonyezana chikondi kumeneku ndi umboni wakuti Ufumu wa Khristu ukulamulira.