Nyimbo 140
Moyo wa Mpainiya
M’mawa uliwonse, tulo tisanathe,
Timadzuka n’kupita
kolalikira uthenga.
Ndipo Mulungu amatitsogolera
Timakondwa anthu
akamamvetsera uthenga.
(KOLASI)
Tinasankha,
kutumikira Yehova.
Timachita zofuna zake.
Tipitirizabe kulalikiraku,
Tikatero timasonyeza
Chikondi.
Pofika madzulo, timatopa ndithu
Komabe timapeza
chimwemwe potumikira
Madalitso Yehova amatipatsa
Nthawi zonse
timamuthokoza potithandiza.
(KOLASI)
Tinasankha,
kutumikira Yehova.
Timachita zofuna zake.
Tipitirizabe kulalikiraku,
Tikatero timasonyeza
Chikondi.
(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 92:2; Aroma 14:8.)