Nyimbo 148
Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha
Yehova, tinali
opanda tsogolo.
Komano dipo
lathandiza tonse.
Tikudzipereka,
kwa inu kosatha.
Tiphunzitse ena,
akudziweninso.
(KOLASI)
Mwana wanu yekha,
munamupereka,
Tidzakuimbirani,
za mphatsoyi kwamuyaya.
Chifundo chanucho
ndi chachikuludi.
Komanso timakonda
dzina lanu.
Yoposa zonsezi
ndi mphatso ya Yesu.
Anatifera kuti
tipulumuke.
(KOLASI)
Mwana wanu yekha,
munamupereka,
Tidzakuimbirani,
za mphatsoyi kwamuyaya.
(KUMALIZA)
Yehova, Atate, tikuthokozatu.
Mphatsoyi munatipatsadi kwamuyaya.
(Onaninso Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9.)