Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Okondedwa Ofalitsa Anzathu a Uthenga Wabwino:
Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala m’gulu la anthu amene akulambira Mulungu woona Yehova. Ndife “antchito anzake,” ndipo watipatsa ntchito yapadera yopulumutsa miyoyo, yomwe ndi yolalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu. (1 Akor. 3:9; Mat. 28:19, 20) Kuti tikwanitse kugwira bwino ntchito yomwe ikuchitika padziko lonse imeneyi mwamtendere komanso mogwirizana, tiyenera kuchita zinthu mwadongosolo.—1 Akor. 14:40.
Bukuli likuthandizani kudziwa mmene mpingo wachikhristu ukugwirira ntchito masiku ano. Likuthandizaninso kudziwa udindo umene muli nawo monga wa Mboni za Yehova. Mukamayamikira mwayi umene muli nawo komanso kukwaniritsa udindo wanu, mudzakhala ‘olimba m’chikhulupiriro.’—Mac. 16:4, 5; Agal. 6:5.
Choncho tikukulimbikitsani kuti muphunzire bukuli mosamala kwambiri. Muziona mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuphunzirazo pa moyo wanu. Mwachitsanzo, ngati mwangovomerezedwa kumene kukhala wofalitsa wosabatizidwa, kodi muyenera kuchita chiyani kuti mubatizidwe n’kukhala wa Mboni za Yehova? Ngati ndinu wobatizidwa, kodi mungatani kuti mupitirize kupita patsogolo mwauzimu komanso kuwonjezera utumiki wanu? (1 Tim. 4:15) Kodi mungathandize bwanji kuti mumpingo mukhale mtendere? (2 Akor. 13:11) Mayankho a mafunso amenewa akupezeka m’bukuli.
Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi mungatani kuti muyenerere kukhala mtumiki wothandiza kenako n’kudzakhala mkulu? Popeza anthu ambiri akubwera m’gulu la Mulungu, pakufunika abale ambiri oyenerera kuti azitsogolera m’mipingo. Bukuli likuthandizani kuona zimene mungachite kuti mukwanitse kukhala ndi zolinga zauzimu zimenezi.—1 Tim. 3:1.
Tikukhulupirira ndi mtima wonse kuti bukuli likuthandizani kuyamikira mwayi umene muli nawo wokhala m’gulu la Yehova. Timakukondani kwambiri ndipo timakupemphererani kuti mukhale pakati pa anthu amene adzasangalale polambira Atate wathu wakumwamba Yehova mpaka kalekale.—Sal. 37:10, 11; Yes. 65:21-25.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova