Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • od tsamba 206-212
  • Mfundo Zomalizira Zokambirana ndi Ofuna Kubatizidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfundo Zomalizira Zokambirana ndi Ofuna Kubatizidwa
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Zakumapeto
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo Labwino
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Bokosi La Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Ubatizo Umatithandiza kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
od tsamba 206-212

MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA

Mfundo Zomalizira Zokambirana ndi Ofuna Kubatizidwa

Ubatizo umachitika pa misonkhano yadera ndi yachigawo ya Mboni za Yehova. Pamapeto pa nkhani ya ubatizo, wokamba nkhaniyo amapempha ofuna kubatizidwa kuti aimirire ndi kuyankha mokweza mafunso awiri otsatirawa:

1. Kodi munalapa machimo anu, kudzipereka kwa Yehova komanso kuvomereza njira yake yopulumutsira anthu kudzera mwa Yesu?

2. Kodi mukudziwa kuti mukabatizidwa muzidziwika kuti ndinu wa Mboni za Yehova komanso kuti muli m’gulu lake?

Ofuna kubatizidwa akayankha kuti inde pa mafunso amenewa, amasonyeza kuti ‘akulengeza poyera’ kuti amakhulupirira dipo ndiponso anadzipereka kwa Yehova. (Aroma 10:9, 10) Nthawi ya ubatizo isanafike, amene akufuna kubatizidwa ayenera kupemphera komanso kusinkhasinkha mafunso amenewa kuti zimene adzayankhe pa tsikuli zidzakhaledi zochokera pansi pa mtima.

Kodi munadzipereka kwa Yehova m’pemphero n’kumulonjeza kuti muzilambira iye yekha komanso muziona kuti chofunika kwambiri pa moyo wanu ndi kuchita chifuniro chake?

Kodi mwatsimikiza kuti mubatizidwa pamsonkhano wotsatira?

Kodi okabatizidwa ayenera kuvala zovala zotani? (1 Tim. 2:9, 10; Yoh. 15:19; Afil. 1:10)

Tiyenera kuvala “mwaulemu ndi mwanzeru,” posonyeza kuti ‘timalemekeza Mulungu.’ Okabatizidwa sayenera kuvala ngati akupita kukasambira kapena kuvala zovala zolemba mawu kapena zojambula zithunzi. Ayenera kuvala zaukhondo, zoyenera, zaulemu komanso zogwirizana ndi mwambowo.

Kodi munthu ayenera kusonyeza khalidwe lotani pamene akubatizidwa? (Luka 3:21, 22)

Zimene Yesu anachita pa nthawi ya ubatizo wake ndi chitsanzo kwa Akhristu masiku ano. Iye ankadziwa kuti ubatizo ndi chinthu chofunika kwambiri ndipo anasonyeza zimenezi mwa zochita zake. Choncho malo a ubatizo si malo ochitira nthabwala zosayenera, kusewera, kusambira kapena zina zilizonse zomwe zingapeputse mwambowo. Komanso Mkhristu amene wangobatizidwa kumeneyo sayenera kuchita zinthu ngati wapambana mpikisano winawake. Ngakhale kuti ubatizo ndi chinthu chosangalatsa, chisangalalocho chiyenera kusonyezedwa moyenera komanso mwaulemu.

Kodi kusonkhana nthawi zonse komanso kuchita zinthu ndi mpingo kudzakuthandizani bwanji kuti muzikwaniritsa lonjezo lanu lodzipereka kwa Yehova?

Mukabatizidwa, n’chifukwa chiyani muyenera kupitirizabe kukhala ndi ndandanda yabwino yophunzira Baibulo panokha komanso yolowa mu utumiki nthawi zonse?

MALANGIZO KWA AKULU

Wofalitsa wosabatizidwa akanena kuti akufuna kubatizidwa, muyenera kumulimbikitsa kuti awerenge mosamala mbali yakuti, “Mafunso kwa Anthu Amene Akufuna Kubatizidwa” yomwe ili patsamba 185-207 m’bukuli. Ayeneranso kuona bwinobwino kamutu kakuti “Mawu kwa Wofalitsa Wosabatizidwa,” komwe kayambira patsamba 182 ndipo kakufotokoza mmene angakonzekerere zimene akulu adzakambirane naye. Monga afotokozera pamenepo, wofuna kubatizidwa angagwiritse ntchito notsi zake zimene analemba ndiponso akhoza kutsegula bukuli pa nthawi imene akukambirana ndi akulu. Koma si kofunika kuti wina akambirane naye mafunsowo asanakumane ndi akulu.

Munthu akafuna kubatizidwa ayenera kudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za akulu. Munthu wofuna kubatizidwayo akamaliza kuwerenga chigawo chakuti, “Mafunso kwa Anthu Amene Akufuna Kubatizidwa,” wogwirizanitsa ntchito za akulu adzamufunsa ngati wadzipereka kwa Yehova m’pemphero kuti azichita chifuniro cha Yehovayo. Ngati wayankha kuti anadzipereka, wogwirizanitsayo adzakonza zoti akulu awiri akumane naye kuti akambirane naye chigawo chakuti, “Mafunso kwa Anthu Amene Akufuna Kubatizidwa.” Mkulu wina angapatsidwe kuti akambirane naye chigawo choyamba ndipo wina angapatsidwe chigawo chachiwiri. Simukuyenera kudikira chilengezo cha msonkhano kuti muyambe kukambirana mafunsowa ndi anthu ofuna kubatizidwa.

Zigawo ziwirizo zingachitidwe maulendo awiri ndipo chilichonse chingatenge pafupifupi ola limodzi, komabe palibe choletsa kupitirira nthawiyi ngati kutakhala kofunika kutero. Zingakhale bwino kuyamba ndi kumaliza chigawo chilichonse ndi pemphero. Mkulu kapena wofuna kubatizidwayo sayenera kukhala pa changu pamene akukambirana mafunsowa. Akulu amene apatsidwa ntchito imeneyi ayenera kuiona kuti ndi yofunika kuiika pamalo oyamba.

Zimakhala bwino kukambirana mafunsowo ndi munthu aliyense payekha osati ndi gulu la anthu angapo. Zimenezi zimathandiza kuti munthu ayankhe mafunso onse ndipo akulu amatha kuona kuti munthuyo akudziwa zinthu zambiri bwanji, ndiponso ngati ndi woyenera kubatizidwa kapena ayi. Komanso munthu angakhale womasuka kuyankha mafunsowo akamafunsidwa payekha. Koma ngati ofuna kubatizidwawo ndi mwamuna ndi mkazi wake, angafunsidwe mafunsowa ali limodzi.

Ngati wofuna kubatizidwayo ndi mlongo, mkulu amene akukambirana naye aonetsetse kuti akhala pamalo oti anthu ena azitha kuwaona koma sangamve zomwe akukambiranazo. Ngati mkuluyo akufuna kukhala ndi munthu wina ayenera kutenga mkulu kapena mtumiki wothandiza malinga ndi chigawo chimene akukambirana ndi munthuyo, monga tafotokozera m’ndime yotsatirayi.

M’mipingo imene muli akulu ochepa, atumiki othandiza omwe asonyeza kuti ndi oganiza bwino komanso ozindikira akhoza kukambirana ndi ofuna kubatizidwa “Chigawo Choyamba: Zimene Akhristu Amakhulupirira.” Koma akulu okha ndi amene ayenera kukambirana ndi ofuna kubatizidwa “Chigawo Chachiwiri: Moyo Wachikhristu.” Ngati mumpingo mulibe abale oyenerera okwanira, woyang’anira dera angadziwitsidwe kuti aone ngati pangafunike kupempha akulu a mpingo wapafupi kuti athandize.

Ngati wofuna kubatizidwayo ndi mwana, makolo ake, ngati ndi a Mboni, angakhalepo pamene akukambirana mafunso ndi akulu. Ngati makolowo sangathe kukhalapo, pangakhale akulu awiri kapena mkulu ndi mtumiki wothandiza, (malinga ndi chigawo chimene akukambirana naye).

Akulu ayenera kutsimikiza kuti munthu amene akufuna kubatizidwayo akumvetsa bwino ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Komanso ayenera kuona ngati munthuyo amayamikiradi choonadi ndipo amasonyeza kuti amalemekeza gulu la Yehova. Ngati akuoneka kuti sanamvetsebe ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo, akuluwo angakonze zoti munthuyo apitirize kuthandizidwa kuti nthawi ina adzayenerere kubatizidwa. Ena angafunike kupatsidwa nthawi kuti asonyeze kuti amaona kuti kulalikira n’kofunika kapena asonyeze kuti amagonjera dongosolo la gulu. Zili ndi akuluwo kuona mmene angagwiritsire ntchito nthawi ya ola limodzilo kapena kuposerapo pa chigawo chilichonse kuti adziwe ngati munthuyo ali woyenerera kubatizidwa. Mwina angagwiritse ntchito nthawi yambiri pa mafunso ena pomwe pa ena sangachedwepo. Komabe ayenera kuonetsetsa kuti akambirana mafunso onse.

Akuluwo ayenera kukumana pambuyo pa chigawo chachiwiri kuti akambirane ndi kuona ngati munthuyo akuyenera kubatizidwa kapena ayi. Ayenera kuganizira mbiri ya munthuyo, zimene angakwanitse kuchita, ndi zinthu zina zokhudza munthuyo. Kwenikweni timafuna kudziwa ngati munthuyo watembenukira kwa Yehova ndi mtima wonse ndipo akumvetsa bwino ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Akathandizidwa mwachikondi, anthu amene akufuna kubatizidwawo amakhala okonzeka kugwira ntchito yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino.

Kenako mkulu mmodzi kapena awiri onsewo angakumane ndi munthuyo n’kumuuza ngati ali woyenera kubatizidwa kapena ayi. Ngati ali woyenerera kubatizidwa, akuluwo ayenera kukambirana naye mbali yakuti, “Mfundo Zomalizira Zokambirana ndi Ofuna Kubatizidwa,” zomwe zili patsamba 206-207. Ngati wofuna kubatizidwayo sanamalize kuphunzira buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndi la Mulungu Azikukondani akulu ayenera kumulimbikitsa kuti akabatizidwa adzamalize kuphunzira mabukuwa. Ayeneranso kumudziwitsa kuti deti lake lobatizidwa lidzalembedwa pa lipoti lake la mpingo lolembapo ntchito za wofalitsa. Komanso ayenera kumukumbutsa kuti akulu amasunga zinthu zokhudza iyeyo ngati zimenezi n’cholinga choti gulu lithe kupitiriza kusamalira Mboni za Yehova padziko lonse komanso kuti iyeyo azitha kutenga nawo mbali pa zinthu zokhudza mpingo ndiponso azithandizidwa mwauzimu. Kuwonjezera pamenepa akulu angakumbutse ofalitsa atsopanowa kuti zinthu zokhudza iwowo zimene zimalembedwa pa lipoti lawo la mpingo amazigwiritsa ntchito mogwirizana ndi mfundo za a Mboni za Yehova zokhudza kusunga chinsinsi, zomwe zimapezeka pa jw.org. Kukambirana naye mfundo zimenezi kuyenera kutenga 10 minitsi basi kapenanso osakwana.

Pakadutsa chaka chimodzi kuchokera pamene munthu anabatizidwa, akulu awiri ayenera kukumana naye kuti amulimbikitse ndi kumupatsa malangizo ena ndi ena. Mmodzi mwa akuluwo ayenera kukhala woyang’anira kagulu ka utumiki ka munthuyo. Ngati wofalitsayo ndi mwana, makolo ake ayenera kukhalapo ngati ali a Mboni. Zokambirana zimenezi ziyenera kukhala zolimbikitsa. Akulu adzafotokoza mmene munthuyo akupitira patsogolo mwauzimu ndi kumuthandiza zimene angachite kuti apitirize kukhala ndi ndandanda yabwino yophunzira Baibulo payekha, kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse, kupezeka pa misonkhano nthawi zonse komanso kuyankha pa misonkhano ndi kulowa mu utumiki wakumunda mlungu uliwonse. (Aef. 5:15, 16) Ngati sanamalizebe kuphunzira buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndi la Mulungu Azikukondani, akuluwo ayenera kukonza zoti munthu wina apitirize kuphunzira naye mabukuwa. Akuluwo ayenera kumuyamikira kwambiri munthuyo. Pa nkhani yomupatsa uphungu kapena malangizo, nthawi zambiri kungokambirana naye mfundo imodzi kapena ziwiri, n’kokwanira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena