Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 11 tsamba 32-tsamba 33 ndime 2
  • Abulahamu Anasonyeza Kuti Anali Wokhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Abulahamu Anasonyeza Kuti Anali Wokhulupirika
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Ayesa Abrahamu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Umboni Waukulu Wakuti Mulungu Amatikonda
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Abulahamu Anali “Bwenzi” la Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Abulahamu Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 11 tsamba 32-tsamba 33 ndime 2
Abulahamu ndi Isaki akupita ku Moriya

MUTU 11

Abulahamu Anasonyeza Kuti Anali Wokhulupirika

Abulahamu anaphunzitsa mwana wake Isaki kuti azikonda Yehova komanso kukhulupirira malonjezo ake onse. Koma Isaki ali ndi zaka pafupifupi 25, Yehova anapempha Abulahamu kuti achite zinthu zovuta kwambiri. Kodi anamuuza kuti achite chiyani?

Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Tenga mwana wako mmodzi yekhayo ndipo ukamupereke nsembe kuphiri la Moriya.’ Abulahamu sankadziwa chifukwa chake Yehova anamuuza kuti achite zimenezi, komabe iye anamvera.

M’mawa wa tsiku lotsatira, anatenga Isaki komanso antchito ake awiri n’kuyamba ulendo wopita kuphiri la Moriya. Atayenda kwa masiku atatu, anayamba kuona phirilo chapatali. Abulahamu anauza antchito ake aja kuti adikire penapake, pamene iye ndi Isaki akukapereka nsembe. Abulahamu anapatsa Isaki nkhuni kuti anyamule ndipo iye anatenga mpeni. Koma Isaki anafunsa bambo akewo kuti: ‘Nanga nkhosa yokapereka nsembeyo ili kuti?’ Abulahamu anayankha kuti: ‘Mwana wanga, Yehova apereka nkhosa yoti tipereke nsembe.’

Atafika paphiripo, anamanga guwa loti aperekerepo nsembe. Ndiyeno Abulahamu anamanga Isaki manja ndi miyendo n’kumugoneka paguwapo.

Isaki ali paguwa atamangidwa ndipo abulahamu watenga mpeni

Kenako anatenga mpeni kuti amuphe. Koma nthawi yomweyo, anamva mngelo wa Yehova akufuula kuti: ‘Abulahamu, usamuvulaze mwanayo. Tsopano ndadziwa kuti umakhulupirira Mulungu chifukwa umafuna kupereka nsembe mwana wako.’ Zitatero, Abulahamu anaona nkhosa itakodwa m’ziyangoyango, chapafupi. Mwamsanga anamasula Isaki ndipo anatenga nkhosayo n’kuipereka nsembe.

Kuyambira tsiku limenelo, Yehova anayamba kutchula Abulahamu kuti mnzake. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Ndi chifukwa choti Abulahamu ankachita zilizonse zimene Yehova ankafuna ngakhale zitakhala kuti sakuzimvetsa.

Abulahamu akumumasula Isaki

Yehova anabwerezanso lonjezo limene anamuuza Abulahamu kuti: ‘Ndidzakudalitsa komanso ndidzachulukitsa ana ako kapena kuti mbadwa zako.’ Apa Yehova ankatanthauza kuti adzadalitsa anthu onse abwino kudzera m’banja la Abulahamu.

“Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.”​—Yohane 3:16

Mafunso: Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Yehova? Kodi Yehova anamulonjeza chiyani Abulahamu?

Genesis 22:1-18; Aheberi 11:17-19; Yakobo 2:21-23

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena