MUTU 22
Zodabwitsa Zimene Zinachitika pa Nyanja Yofiira
Farao atamva kuti Aisiraeli achoka ku Iguputo, anasintha maganizo. Anauza asilikali ake kuti: ‘Tengani magaleta anga ankhondo, tiwatsatire. Sitimayenera kuwalola kuti apite.’ Choncho Farao ndi asilikali ake anayamba kuthamangira Aisiraeli.
Yehova ankatsogolera anthu ake. Masana ankagwiritsira ntchito mtambo ndipo usiku ankagwiritsa ntchito moto. Aisiraeliwo atafika pa Nyanja Yofiira, Yehova anawauza kuti amange misasa.
Kenako Aisiraeli anaona Farao ndi asilikali ake akuwathamangira. Analibe kothawira chifukwa kutsogolo kwawo kunali nyanja ndipo kumbuyo kwawo n’kumene kunali asilikaliwo. Iwo anachita mantha kwambiri ndipo analirira Mose kuti: ‘Tifa basi! Bola ukanangotisiya ku Iguputo konkuja.’ Koma Mose anawauza kuti: ‘Musachite mantha. Limbani mtima ndipo muona mmene Yehova atipulumutsire.’ Apa Mose anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova.
Ndiyeno Yehova anauza Aisiraeli kuti anyamuke. Usiku umenewo, Yehova anachititsa kuti mtambo uja ukhale pakati pa Aisiraeliwo ndi Aiguputo. Zimenezi zinachititsa kuti kumbali ya Aiguputo kukhale mdima, pamene kumbali ya Aisiraeli kunkawala.
Yehova anauza Mose kuti atambasule dzanja lake n’kuloza panyanja. Ndiyeno Yehova anachititsa mphepo yamphamvu kuwomba panyanjapo usiku wonse. Kenako nyanjayo inagawikana ndipo madzi anaima ngati makoma m’mbali zonse. Aisiraeli anawoloka pouma kupita kutsidya la nyanjayo.
Asilikali a Farao analowa pakati pa makoma amadziwo potsatira Aisiraeli. Zitatero Yehova anachititsa kuti asilikaliwo asokonezeke. Mateyala a magaleta awo anayamba kuguluka. Ataona zimenezi asilikaliwo anafuula kuti: ‘Tiyeni tithawe! Yehova akuwamenyera nkhondo.’
Kenako Yehova anauza Mose kuti: ‘Tambasula dzanja lako ndi kuloza panyanja.’ Nthawi yomweyo madzi aja anabwerera m’malo mwake n’kumiza asilikali onse a Aiguputo. Farao ndi asilikali ake anafera pomwepo. Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.
Aisiraeliwo ataona kuti apulumuka anatamanda Mulungu poimba kuti: “Ndiimbira Yehova, chifukwa walemekezeka kwambiri. Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.” Poimba nyimboyi, azimayi ankavina ndipo ena ankaimba maseche. Aliyense anasangalala kwambiri chifukwa tsopano sanalinso akapolo.
“Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”—Aheberi 13:6