MUTU 27
Aisiraeli Ena Anaukira Yehova
Nthawi ina Aisiraeli ali m’chipululu, Kora, Datani, Abiramu ndi anthu ena okwana 250 anaukira Mose. Iwo anati: ‘Tatopa nawe tsopano! N’chifukwa chiyani ukufuna uzitilamulira ndipo wasankha Aroni kuti akhale mkulu wa ansembe? Yehova ali ndi tonsefe, osati iweyo ndi Aroni basi.’ Zimenezi sizinamusangalatse Yehova chifukwa ankaona kuti anthuwo akutsutsana ndi iyeyo.
Mose anauza Kora ndi anthu amene anali kumbali ya Korayo kuti: ‘Mawa mubwere kuchihema ndipo mudzatenge zofukizira ndipo mʼzofukizirazo mudzaikemo moto ndi zinthu zonunkhira zoti mukapereke nsembe. Yehova adzationetsa munthu amene wamusankha.’
Tsiku lotsatira, Kora ndi anthu 250 aja anapitadi kukakumana ndi Mose kuchihema. Kumeneko iwo anapereka nsembe ngakhale kuti sanali ansembe. Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: ‘Chokani musayandikane ndi Kora ndi anzakewo.’
Ngakhale kuti Kora anapita kukakumana ndi Mose kuchihema, Datani, Abiramu ndi mabanja awo anakana kupitako. Yehova anauza Aisiraeli kuti asayandikire matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Nthawi yomweyo Aisiraeli anapita kutali ndi matentiwo. Datani, Abiramu ndi mabanja awo anaima panja pa matenti awo. Ndiye nthawi yomweyo nthaka inang’ambika n’kuwameza. Nakonso kuchihema kuja, moto wochokera kwa Yehova unapsereza Kora ndi anzake 250 aja.
Zitatero Yehova anauza Mose kuti: ‘Tenga ndodo ya mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ulembepo dzina la mtsogoleriyo. Koma pandodo ya fuko la Levi, ulembepo dzina la Aroni. Ndodozi uziike m’chihema ndipo ndodo ya munthu amene ndasankha, idzachita maluwa.’
Tsiku lotsatira Mose anatenga ndodo zonse n’kuwaonetsa atsogoleri aja. Ndodo ya Aroni inali itachita maluwa n’kubereka zipatso zakupsa za amondi. Zimenezi zinatsimikizira kuti Yehova anali atasankha Aroni kuti akhale mkulu wa ansembe.
“Muzimvera amene akukutsogolerani ndipo muziwagonjera.”—Aheberi 13:17