Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 30 tsamba 76
  • Rahabi Anabisa Aisiraeli Okafufuza Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Rahabi Anabisa Aisiraeli Okafufuza Dziko
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Rahabi Ankakhulupirira Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
  • Rahabi Anamvetsera Uthenga
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Rahabi Abisa Azondi
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • ‘Anaonedwa Ngati Wolungama Chifukwa cha Ntchito Zake’
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 30 tsamba 76
Rahabi akubisa Aisiraeli okafufuza dziko pouza asilikali kuti adutse njira ina

MUTU 30

Rahabi Anabisa Aisiraeli Okafufuza Dziko

Aisiraeli awiri amene anatumidwa kukafufuza mzinda wa Yeriko anakafikira m’nyumba ya mayi wina dzina lake Rahabi. Mfumu ya kumeneko itazindikira, inatumiza asilikali kunyumbako. Koma Rahabi anabisa Aisiraeliwo padenga n’kuuza asilikaliwo kuti alowere njira ina. Kenako anauza Aisiraeliwo kuti: ‘Ndikukuthandizani chifukwa ndikudziwa kuti Yehova akukumenyerani nkhondo ndipo mugonjetsa mzindawu. Chonde, lonjezani kuti simudzapha ineyo ndi abale anga.’

Aisiraeliwo anauza Rahabi kuti: ‘Tikulonjeza kuti aliyense amene adzakhale m’nyumba yakoyi sadzaphedwa.’ Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Umangirire chingwe chofiira pawindo kuti iwe ndi abale ako mudzatetezeke.’

Nyumba ya Rahabi ili ndi kansalu kofiira pawindo ndipo yatsala pamene mpanda wa mzinda wa Yeriko wagwa

Rahabi anagwiritsa ntchito chingwe potulutsira Aisiraeliwo pawindo kuti azipita. Iwo anakabisala m’mapiri kwa masiku atatu asanabwerere kumene kunali Yoswa. Kenako Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano ndipo anayamba kukonzekera kuti alande dzikolo. Mzinda woyamba kuugonjetsa unali wa Yeriko. Yehova anawauza kuti azizungulira mzindawo kamodzi pa tsiku kwa masiku 6. Koma pa tsiku la 7 anawauza kuti auzungulire maulendo 7 ansembe akuimba malipenga, kenako asilikali anayamba kuchita phokoso kwambiri. Zitatero, mpanda wa mzindawo unagwa. Koma nyumba ya Rahabi yomwe inalumikizana ndi mpandawo, sinagwe. Rahabi ndi anthu a m’banja lake anapulumuka chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri Yehova.

“Mofanana ndi zimenezi, kodi Rahabi . . . sanaonedwenso kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, atalandira bwino anthu amene ankafufuza dziko lawo nʼkuwathandiza kuti athawe kudzera njira ina?”​—Yakobo 2:25

Mafunso: N’chifukwa chiyani Rahabi anabisa Aisiraeli amene anakafufuza mzinda wa Yeriko? Kodi Aisiraeli anachita zotani pogonjetsa Yeriko? N’chiyani chinachitikira Rahabi ndi anthu a m’banja lake?

Yoswa 2:1-24; 6:1-27; Aheberi 11:30, 31; Yakobo 2:24-26

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena