Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 31 tsamba 78
  • Yoswa ndi anthu a ku Gibiyoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yoswa ndi anthu a ku Gibiyoni
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Agibeoni Anzeru
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Dzuwa Liima
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Zimene Yoswa Anakumbukira
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 31 tsamba 78
Anthu a ku Gibiyoni avala zovala zong’ambika ndipo akukakumana ndi Yoswa ndi asilikali ake

MUTU 31

Yoswa ndi Anthu a ku Gibiyoni

Anthu ena a ku Kanani anamva zimene zinachitika ku Yeriko. Ndiyeno mafumu angapo anagwirizana kuti amenyane ndi Aisiraeli. Koma anthu a ku Gibiyoni anaganizira pulani ina. Anapita kwa Yoswa atavala zovala zong’ambika n’kunena kuti: ‘Tachokera kudziko lakutali kwambiri. Tamva za Yehova komanso zimene anakuchitirani ku Iguputo ndi ku Mowabu. Lonjezani kuti simudzamenyana nafe ndipo ife tikhala akapolo anu.’

Yoswa anakhulupirira zimene ananenazi ndipo analonjeza kuti sadzamenyana nawo. Patangodutsa masiku atatu, anazindikira kuti anthuwo sanali akutali. Anali a m’dziko la Kanani lomwelo. Ndiyeno Yoswa anafunsa anthuwo kuti: ‘N’chifukwa chiyani munatinamiza?’ Iwo anayankha kuti: ‘Timaopa, chifukwa tikudziwa kuti Yehova Mulungu wanu ndi amene akukumenyerani nkhondo. Chonde musatiphe.’ Yoswa anasunga lonjezo lake ndipo sanawaphe.

Pasanapite nthawi yaitali, mafumu 5 a ku Kanani anakonza zoti amenyane ndi anthu a ku Gibiyoni. Ndiyeno Yoswa ndi asilikali ake anayenda usiku wonse kupita kukawathandiza. Nkhondo inayamba m’mawa ndipo Akananiwo anayamba kuthawa n’kubalalikira mbali zonse. Ndiyeno kulikonse kumene ankathawirako Yehova ankawagwetsera zimatalala zikuluzikulu. Kenako Yoswa anapempha Yehova kuti aimitse dzuwa. N’chifukwa chiyani iye anapempha zimenezi chikhalirecho dzuwa linali lisanaimepo? N’chifukwa choti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Yehova anayankha ndipo dzuwa silinalowe kwa tsiku lonse mpaka Aisiraeli atagonjetsa mafumu onsewo ndi asilikali awo.

Yoswa akuyang’ana kumwamba ndipo akupempha Yehova kuti aimitse dzuwa

“Tangotsimikizani kuti mukati ‘Indeʼ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayiʼ akhaledi ayi, chifukwa mawu owonjezera pamenepa ndi ochokera kwa woipayo.”​—Mateyu 5:37

Mafunso: Kodi anthu a ku Gibiyoni anachita chiyani kuti apulumuke? Kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli?

Yoswa 9:1-27; 10:1-15

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena