Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 33 tsamba 82-tsamba 83 ndime 2
  • Rute ndi Naomi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Rute ndi Naomi
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Rute ndi Naomi
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • “Kumene Inu Mupite Inenso Ndipita Komweko”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Rute
    Nsanja ya Olonda—2005
  • “Kumene Inu Mupite Inenso Ndipita Komweko”
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 33 tsamba 82-tsamba 83 ndime 2
Naomi akuuza Rute kuti abwerere

MUTU 33

Rute ndi Naomi

Pa nthawi ina, ku Isiraeli kunali njala. Ndiyeno Naomi ananyamuka ndi mwamuna wake komanso ana ake aamuna awiri kupita ku Mowabu. Kenako mwamuna wa Naomi anamwalira. Ana ake aja anakwatira akazi a Chimowabu ndipo akaziwo anali Rute ndi Olipa. Koma patapita nthawi, anawo anamwaliranso.

Naomi atamva kuti njala ku Isiraeli yatha, anaganiza zobwerera kwawo. Rute ndi Olipa ananyamuka naye limodzi koma ali panjira, Naomi anawauza kuti: ‘Ndinu akazi abwino kwambiri. Munkathandiza ana anga komanso ineyo. Koma bwererani kwanu ku Mowabu ndipo mukhoza kukakwatiwanso.’ Rute ndi Olipa anati: ‘Timakukondani kwambiri ndipo sitikufuna kuti tisiyane.’ Naomi anawaumiriza kuti abwerere. Pamapeto pake, Olipa anabwerera koma Rute sanabwerere. Naomi anauza Rute kuti: ‘Iwe, taona Olipa akubwerera kwa anthu ake ndiponso kwa milungu yake. Bwerera naye limodzi, pita kunyumba kwa mayi ako.’ Koma Rute anati: ‘Sindingakusiyeni. Anthu anu adzakhala anthu anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.’ Kodi ukuganiza kuti Naomi anamva bwanji Rute atanena zimenezi?

Naomi ndi Rute anafika ku Isiraeli nthawi yokolola balere itangoyamba. Tsiku lina Rute anapita kukakunkha balere wotsalira m’munda mwa bambo wina dzina lake Boazi. Bamboyu anali mwana wa Rahabi. Atamva zoti Rute anali wa ku Mowabu koma ankakhalabe ndi Naomi, anauza antchito ake kuti azimusiyira barele wina kuti atenge.

Rute akukunkha balere m’munda mwa Boazi

Tsiku lina Rute atabwerera madzulo, Naomi anamufunsa kuti: ‘Kodi lero unakakunkha kuti balere?’ Rute anayankha kuti: ‘M’munda mwa bambo enaake dzina lawo a Boazi.’ Ndiyeno Naomi anati: ‘Amenewotu ndi achibale a mwamuna wanga. Nthawi zonse uzipita m’munda wawo limodzi ndi atsikana ena. Sangakuchite chipongwe.’

Naomi, Boazi, Rute ndi Obedi

Rute ankapitadi kumunda wa Boazi mpaka pamene nyengo yokolola inatha. Boazi anaona kuti Rute ankagwira ntchito mwakhama ndipo anali mkazi wabwino kwambiri. Nthawi imeneyo munthu akamwalira wopanda mwana, wachibale wake ankakwatira mkazi wamasiyeyo. Choncho Boazi anakwatira Rute. Iwo anabereka mwana dzina lake Obedi amene anadzakhala agogo ake a Mfumu Davide. Anzake a Naomi anasangalala kwambiri. Iwo ankanena kuti: ‘Yehova anakupatsa Rute ndipo wakhala akukuthandiza kwambiri. Tsopano wakupatsa chidzukulu. Yehova atamandike.’

“Pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.”​—Miyambo 18:24

Mafunso: Kodi Rute anasonyeza bwanji kuti ankakonda Naomi? Kodi Yehova ankasamalira bwanji Rute ndi Naomi?

Rute 1:1-22; 2:1-23; 3:1-18; 4:1-22; Mateyu 1:5

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena