Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 34 tsamba 84-tsamba 85 ndime 2
  • Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Gideon ndi Amuna Ake 300
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Zimene Akulu Angaphunzire pa Chitsanzo cha Gidiyoni
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Yehova Ndi Mnzathu Weniweni
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 34 tsamba 84-tsamba 85 ndime 2
Gidiyoni ndi asilikali ake aliza malipenga, kuphwanya mitsuko, kunyamula zounikira m’mwamba kenako n’kufuula

MUTU 34

Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani

Patapita nthawi, Aisiraeli anasiyanso kulambira Yehova ndipo anayamba kulambira milungu yabodza. Kwa zaka 7, Amidiyani ankaba ziweto za Aisiraeli komanso kuwawonongera mbewu zawo. Pothawa Amidiyaniwo, Aisiraeli ankabisala m’mapanga komanso m’mapiri. Kenako anapempha Yehova kuti awapulumutse. Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo kuti apite kwa Gidiyoni. Mngeloyo anauza Gidiyoni kuti: ‘Yehova wakusankha kuti ukhale msilikali wamphamvu.’ Gidiyoni anafunsa kuti: ‘Kodi munthu wachabechabe ngati ine, ndingapulumutse bwanji Aisiraeli?’

Koma kodi Gidiyoni akanatsimikizira bwanji kuti Yehova anamusankhadi? Iye anaika pansi ubweya wa nkhosa n’kuuza Yehova kuti: ‘Ngati m’mawa, ubweyawu unganyowe ndi mame koma nthaka n’kukhala youma, ndidzadziwa kuti mwandisankhadi kuti ndipulumutse Aisiraeli.’ M’mawa wa tsiku lotsatira anapeza kuti ubweya uja wanyowa koma nthaka ndi youma. Koma Gidiyoni anapemphanso kuti m’mawa wa tsiku lotsatira apeze ubweya uja uli wouma koma nthaka idzakhale yonyowa. Zimenezi zitachitika, Gidiyoni anatsimikizira kuti Yehova anamusankhadi. Ndiyeno anasonkhanitsa asilikali ake kuti akamenyane ndi Amidiyani.

Yehova anauza Gidiyoni kuti: ‘Ndithandiza Aisiraeli kuti apambane pa nkhondoyi. Koma chifukwa uli ndi asilikali ambiri, ungaganize kuti mwapambana ndi mphamvu zanu. Uza aliyense amene akuchita mantha kuti abwerere.’ Choncho asilikali 22,000 anabwerera n’kutsala okwana 10,000. Yehova ananena kuti: ‘Asilikaliwa achulukabe. Pita nawo kumtsinje ndipo ukawauze kuti akamwe madzi. Ndiyeno ukasankhe omwe azikamwa madzi, uku akuyang’ana adani awo.’ Asilikali 300 okha ndi amene anali tcheru pamene ankamwa. Yehova analonjeza kuti asilikali ochepawo adzagonjetsa asilikali a Amidiyani okwana 135,000.

Usiku, Yehova anauza Gidiyoni kuti: ‘Tsopano pitani mukamenyane ndi Amidiyani. Gidiyoni anapatsa asilikali akewo malipenga a nyanga ndi mitsuko ikuluikulu ndipo m’mitsukomo anaikamo zounikira. Iye anawauza kuti: ‘Muzionetsetsa zimene ndikuchita ndipo nanunso muzichita zomwezo.’ Gidiyoni analiza lipenga lake, n’kuphwanya mtsuko uja ndiyeno ananyamula chounikira chake m’mwamba n’kufuula kuti: ‘Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!’ Asilikali 300 aja anachitanso chimodzimodzi. Amidiyani atamva zimenezi anachita mantha ndipo anayamba kuthawa. Chifukwa chosokonezeka, iwo anayamba kuukirana okhaokha. Apa Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa adani awo.

Asilikali achimidiyani akuchita mantha

“Kuti mphamvu yoposa yachibadwa ichokere kwa Mulungu, osati kwa ife.”​—2 Akorinto 4:7

Mafunso: Kodi Yehova anamutsimikizira bwanji Gidiyoni kuti wamusankha kuti akagonjetse Amidiyani? N’chifukwa chiyani Gidiyoni anali ndi asilikali 300 okha?

Oweruza 6:1-16; 6:36-40; 7:25; 8:28

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena