MUTU 48
Mwana wa Mayi Wamasiye Anaukitsidwa
Pamene ku Isiraeli kunali chilala, Yehova anauza Eliya kuti: ‘Pita ku Zarefati. Kumeneko mayi wina wamasiye azikakupatsa chakudya.’ Eliya atafika mumzindawo, anaona mayi wosauka komanso wamasiye akutola nkhuni. Iye anam’pempha kuti amupatseko madzi. Pamene mayiyo ankapita kukatenga madziwo, Eliya anamuuzanso kuti: ‘Mundibweretserekonso chakudya pang’ono.’ Koma mayiyo anati: ‘Ndilibe chakudya choti ndingakupatseni. Ndangotsala ndi kaufa kochepa ndi timafuta toti ndiphikire chakudya chokwanira ineyo ndi mwana wanga basi.’ Koma Eliya anamuuza kuti: ‘Yehova wanena kuti mukandipatsa, ndiye kuti ufa ndi mafuta anu sizitha mpaka mvula idzagwe.’
Ndiyeno mayiyo anapita kukakonza chakudya n’kupatsa mneneri wa Yehovayo. Mogwirizana ndi zimene Yehova ananena, mayiyo ndi mwana wake anali ndi chakudya pa nthawi yonse yachilalayo. Mtsuko wake wa ufa komanso wa mafuta unkangokhalabe wodzadza.
Kenako panachitika zinthu zomvetsa chisoni. Mwana uja anadwala kwambiri mpaka kumwalira. Ndiyeno mayiyo anapempha Eliya kuti amuthandize. Eliya anatenga mwana wakufayo n’kupita naye kuchipinda cham’mwamba. Anamugoneka pabedi ndipo anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova, ukitsani mwanayu.’ Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani zimene Eliya anapemphazi zinali zodabwitsa? Chifukwa kuyambira kalekale, zimenezi zinali zisanachitikepo. Komanso mayiyu ndi mwana wakeyo sanali Aisiraeli.
Koma mwana uja anakhalanso ndi moyo ndipo anayamba kupuma. Eliya anauza mayiyo kuti: ‘Mwana wanu uja tsopano ali moyo.’ Mayiyo anasangalala kwambiri ndipo anauza Eliya kuti: ‘Ndinudi munthu wa Mulungu. Ndikutero chifukwa mumalankhula zimene Yehova wakuuzani.’
“Ganizirani za akhwangwala: Iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nkhokwe kapena nyumba yosungiramo zinthu, koma Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame?”—Luka 12:24