Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 52 tsamba 126-tsamba 127 ndime 1
  • Gulu Lamphamvu la Asilikali a Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gulu Lamphamvu la Asilikali a Yehova
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Elisa Anaona Magaleta Oyaka Moto​—Kodi Inunso Mukuwaona?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Nyamula Mwana Wako”
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Chitsanzo cha Kudzimana ndi Kukhulupirika
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 52 tsamba 126-tsamba 127 ndime 1
Eliya ndi mtumiki wake azunguliridwa ndi gulu la asilikali a Siriya

MUTU 52

Gulu Lamphamvu la Asilikali a Yehova

Beni-hadadi anali mfumu ya Siriya ndipo ankakonda kupita kukamenyana ndi Aisiraeli. Koma nthawi zonse mneneri Elisa ankadziwitsa mfumu ya Isiraeli ndipo mfumuyo inkathawa. Ndiyeno Beni-hadadi anaganiza zotuma asilikali ake kuti akagwire Elisa. Iye anamva kuti Elisayo ali ku Dotani.

Asilikali a Siriya anafika ku Dotani usiku n’kuzungulira mzindawo. M’mawa, mtumiki wa Elisa atatuluka panja anaona gulu lalikulu la asilikali. Iye anachita mantha kwambiri ndipo anafuula kuti: ‘Mayo ine mbuyanga! Titani?’ Koma Elisa anamuuza kuti: ‘Usaope, ifetu tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.’ Ndiyeno Yehova anatsegula maso a mtumikiyo ndipo anaona kuti m’mapiri onse ozungulira mzindawo munali mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.

Elisa ndi mtumiki wake akuona gulu la nkhondo la angelo litawazungulira

Pamene asilikali a Siriya ankafuna kugwira Elisa, iye anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova achititseni khungu.’ Mwadzidzidzi, asilikali aja anapezeka kuti sakuzindikira kumene ali ngakhale kuti ankaona. Zitatero Elisa anawauza kuti: ‘Mwasocheratu. Bwerani kuno ndikuperekezeni kwa munthu amene mukufuna.’ Asilikaliwo anayamba kumutsatira mpaka kukafika ku Samariya kumene mfumu ya Aisiraeli inkakhala.

Apa m’pamene asilikaliwo anazindikira kumene ali. Mfumuyo itawaona inafunsa Elisa kuti: ‘Kodi ndiwaphe?’ Kodi Elisa anaona ngati umenewu unali mwayi woti aphe anthu amene ankafuna kumuphawo? Ayi. M’malomwake anauza mfumuyo kuti: ‘Musawaphe. Apatseni chakudya adye kenako muwalole kuti azipita.’ Choncho mfumuyo inawakonzera phwando lalikulu. Atamaliza kudya ananyamuka n’kumapita kwawo.

Asilikali a Siriya akudya chakudya u Samariya

“Ndipotu ife sitikayikira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi zimene amafuna, amatimvera.”​—1 Yohane 5:14

Mafunso: Kodi Yehova anateteza bwanji Elisa ndi mtumiki wake? Kodi ukuganiza kuti Yehova angakutetezenso iweyo?

2 Mafumu 6:8-24

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena