Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 58 tsamba 140-tsamba 141 ndime 3
  • Mzinda wa Yerusalemu Unawonongedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mzinda wa Yerusalemu Unawonongedwa
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Ulosi Wokhudza Mesiya—Mtengo Waukulu Wamkungudza
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Kutumikira Mulungu “M’masiku Otsiriza”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Babulo Wamphamvu—Mphamvu Yaikulu ya Dziko Yachitatu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Yehova Adzaweruza Aliyense Malinga ndi Ntchito Zake
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 58 tsamba 140-tsamba 141 ndime 3
Yerusalemu ndi kachisi zikuyaka

MUTU 58

Mzinda wa Yerusalemu Unawonongedwa

Nthawi zambiri, Ayuda ankasiya Yehova n’kumalambira milungu yabodza. Yehova anayesetsa kuwathandiza kwa zaka zambiri. Ankawatumizira aneneri ambiri kuti awachenjeze koma iwo sankawamvera. M’malomwake ankangowaseka. Kodi Yehova anathetsa bwanji vuto lolambira mafanoli?

Nebukadinezara, yemwe anali mfumu ya Babulo, ankagonjetsa mayiko ambiri. Pa ulendo woyamba umene anagonjetsa Yerusalemu, anagwira Mfumu Yehoyakini, akalonga, asilikali komanso anthu ena aluso ndipo anapita nawo ku Babulo. Anatenganso chuma chonse chimene chinali m’kachisi wa Yehova. Kenako, Nebukadinezara anasankha Zedekiya kuti akhale mfumu ya Yuda.

Poyamba, Zedekiya ankamvera Nebukadinezara. Koma kenako anthu a m’mayiko apafupi komanso aneneri abodza anamuuza kuti aukire ulamuliro wa Babulo. Koma Yeremiya anamuuza kuti: ‘Mukasiya kumvera Ababulo, anthu anu ambiri aphedwa ndipo m’dziko lino mukhala njala ndi matenda.’

Zedekiya atangolamulira zaka 8, anasiya kumvera Ababulo. Iye anapempha asilikali a ku Iguputo kuti amuthandize. Ndiyeno Nebukadinezara anatumiza asilikali ake kuti akawononge mzinda wa Yerusalemu. Asilikaliwo atazungulira mzindawo, Yeremiya anauza Zedekiya kuti: ‘Yehova wanena kuti mukangouza Ababulo kuti mwagonja, mzindawu komanso anthu anu apulumuka. Koma mukachita makani, Ababulo awotcha mzindawu ndipo inuyo apita nanu ku ukapolo.’ Zedekiya anayankha kuti: ‘Sindingayerekeze n’komwe kuwauza Ababulo kuti ndagonja!’

Patangopita zaka zitatu ndi hafu, asilikali a Babulo analowa mumzindawo n’kuuwotcha. Iwo anawotcha kachisi, kupha anthu ambiri n’kutenga ena kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.

Zedekiya anayamba kuthawa koma asilikali a ku Babulo anamuthamangitsa. Anamugwira pafupi ndi Yeriko n’kupita naye kwa Nebukadinezara. Mfumuyi inapha ana a Zedekiya iye akuona. Kenako anamuchotsa maso n’kumutsekera m’ndende ndipo anafera momwemo. Koma Yehova anauza Ayuda kuti: ‘Pakatha zaka 70 ndidzakubwezeretsani ku Yerusalemu.’

Kodi ukuganiza kuti achinyamata amene anapita ku Babulo zinawathera bwanji? Kodi iwo anakhalabe okhulupirika kwa Yehova?

“Yehova Mulungu, inu Wamphamvuyonse, ziweruzo zanu ndi zoona komanso zolungama.”​—Chivumbulutso 16:7

Mafunso: Kodi Nebukadinezara anali ndani, nanga anachita zotani ku Yerusalemu? Kodi Zedekiya anali ndani?

2 Mafumu 24:1, 2, 8-20; 25:1-24; 2 Mbiri 36:6-21; Yeremiya 27:12-14; 29:10, 11; 38:14-23; 39:1-9; Ezekieli 21:27

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena