MUTU 59
Anyamata 4 Amene Anamvera Yehova
Nebukadinezara atatenga akalonga a ku Yuda n’kupita nawo ku Babulo, anasankha nduna ina dzina lake Asipenazi kuti iziyang’anira akalongawo. Nebukadinezara anauza Asipenazi kuti asankhe anyamata athanzi komanso anzeru. Anamuuza kuti anyamatawo asamaliridwe komanso aphunzitsidwe kwa zaka zitatu n’cholinga choti adzakhale akuluakulu a boma ku Babuloko. Anyamata amenewa anayeneranso kuwaphunzitsa kuwerenga, kulemba komanso kulankhula chilankhulo cha Akasidi. Ankafunikanso kumawapatsa chakudya chimene mfumu ndi anthu ogwira ntchito kunyumba kwake ankadya. Pagulu la anyamatawa panali Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya. Koma Asipenazi anawapatsa mayina achibabulo akuti, Belitesazara, Shadireki, Misheki ndi Abedinego. Kodi zimene ankawaphunzitsazo zinachititsa kuti anyamatawa asiye kutumikira Yehova? Ayi.
Iwo anatsimikiza kuti apitirizabe kumvera Yehova. Ankadziwa kuti sakuyenera kudya chakudya cha mfumu chifukwa Chilamulo cha Yehova chinkaletsa zina mwa zakudya zimenezo. Choncho anauza Asipenazi kuti: ‘Chonde musamatipatse chakudya cha mfumu.’ Koma Asipenazi anawayankha kuti: ‘Mukapanda kumadya zakudya za mfumu muwonda ndipo mfumu indipha.’
Ndiyeno Danieli anapeza nzeru. Anauza Asipenazi kuti: ‘Muzitipatsa masamba ndi madzi kwa masiku 10. Kenako mudzayerekeze mmene tizidzaonekera ndi mmene anyamata ena azidzaonekera.’ Asipenazi anavomera.
Patatha masiku 10, Danieli ndi anzake atatuwo ankaoneka athanzi kuposa anyamata ena onse. Yehova anasangalala chifukwa choti anyamatawa anamumvera ndipo anapatsa Danieli nzeru moti ankatha kudziwa tanthauzo la masomphenya ndi maloto.
Zaka zitatu zija zitatha Asipenazi anapita ndi anyamata onse kwa Nebukadinezara. Mfumuyo italankhula nawo, anaona kuti Danieli, Hananiya, Sadirake ndi Azariya anali anzeru komanso ochangamuka kuposa anyamata enawo. Choncho anawasankha kuti azigwira ntchito kunyumba kwake. Mfumuyi inkafunsira nzeru kwa anyamatawa chifukwa Yehova anawathandiza kukhala ndi nzeru kuposa anzeru onse a m’dzikolo.
Ngakhale kuti anyamata 4 amenewa ankakhala kudziko la eni, sanaiwale kuti anali anthu a Mulungu. Kodi iwenso utakhala kumalo koti kulibe makolo ako, ungapitirizebe kumvera Yehova?
“Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamngʼono. Mʼmalomwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika pa zimene umalankhula, makhalidwe ako, chikondi, chikhulupiriro ndi khalidwe loyera.”—1 Timoteyo 4:12