MUTU 60
Ufumu Umene Udzalamulire Mpaka Kalekale
Tsiku lina usiku, Nebukadinezara analota maloto odabwitsa. Malotowo anamuvutitsa kwambiri moti sanagonenso. Kenako anaitana amatsenga ake n’kuwauza kuti: ‘Ndiuzeni zimene ndalota.’ Amatsengawo anati: ‘Inuyo mutiuze zimene mwalota ndipo ifeyo tikumasulirani malotowo.’ Koma Nebukadinezara anawauza kuti: ‘Ayi. Inuyo mundiuze zimene ndalota, apo ayi ndikuphani.’ Iwo anamuuzanso kachiwiri kuti: ‘Tiuzeni malotowo ndipo ife tikumasulirani.’ Iye anati: ‘Nonsenu mukungofuna kundipusitsa. Tanenani. Ndalota chiyani?’ Iwo anamuyankha kuti: ‘Palibe munthu amene angathe kuchita zimenezi. Zimene mukufunazi n’zosatheka.’
Nebukadinezara anakwiya kwambiri moti analamula kuti amuna onse anzeru m’dzikolo aphedwe. Apa ndiye kuti nayenso Danieli, Shadireki, Misheki ndi Abedinego akanaphedwa. Danieli atamva zimenezi anapempha mfumu kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake. Kenako iye ndi anzakewo anapemphera kwa Yehova kuti awathandize. Ndiye kodi Yehova anatani?
Kudzera m’masomphenya, Yehova anauza Danieli maloto a Nebukadinezara komanso tanthauzo lake. Tsiku lotsatira Danieli anapita kwa atumiki a mfumu n’kuwauza kuti: ‘Musaphe munthu aliyense. Ine ndikauza mfumu zimene analota.’ Atumikiwo anamutenga n’kupita naye kwa mfumu. Danieli anauza mfumuyo kuti: ‘Mulungu wakudziwitsani zimene zidzachitike m’tsogolo. Zimene munalota ndi izi: Munaona chifaniziro chachikulu. Mutu wake unali wagolide, chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva, mimba ndi ntchafu zake zinali zakopa, miyendo yake inali yachitsulo ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanikirana ndi dongo. Kenako mwala unadulidwa kuphiri ndipo unamenya mapazi a chifanizirocho. Chifanizirocho chinaphwanyika n’kusanduka fumbi lomwe linauluzika ndi mphepo. Ndiyeno mwala uja unakula n’kukhala phiri lalikulu ndipo linadzaza padziko lonse lapansi.’
Kenako Danieli anati: ‘Tanthauzo la maloto anuwa ndi ili: Ufumu wanu ndi mutu wagolidewo. Siliva akuimira ufumu womwe udzabwere pambuyo panu. Kenako padzabwera ufumu wina wangati kopa umenenso udzalamulire padziko lonse. Pambuyo pa umenewo padzabwera ufumu wolimba ngati chitsulo. Pomaliza padzabwera ufumu wogawanika, mbali zake zina zidzakhala zolimba ngati chitsulo koma zina zidzakhala zosalimba ngati dongo. Mwala umene unakula n’kukhala phiri, ukuimira Ufumu wa Mulungu. Ufumuwu udzaphwanya maufumu onse ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.’
Nebukadinezara atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. Kenako anati: ‘Mulungu wako ndi amene wakuululira malotowa. Palibenso Mulungu wina wofanana naye.’ Nebukadinezara anapatsa Danieli udindo woti aziyang’anira anthu onse anzeru. Anamuikanso kukhala wolamulira chigawo chonse cha Babulo. Kodi waona mmene Yehova anayankhira pemphero la Danieli?
“Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene mʼChiheberi amatchulidwa kuti Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:16