Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 61 tsamba 146-tsamba 147 ndime 3
  • Anakana Kulambira Fano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anakana Kulambira Fano
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Sakanagwada
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kulambira Nkwa Mulungu
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Chikhulupiriro Chawo Chinapulumuka Chiyeso Choopsa
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Kodi Mulungu Wako Ndani?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 61 tsamba 146-tsamba 147 ndime 3
Shadireki, Misheki ndi Abedinego anakana kulambira fano la golide

MUTU 61

Anakana Kulambira Fano

Patadutsa nthawi kuchokera pamene Mfumu Nebukadinezara analota, anapanga fano lalikulu la golide. Fanoli analiimika m’chigwa cha Dura ndipo anaitana anthu onse a maudindo akuluakulu m’boma kuphatikizapo Shadireki, Misheki ndi Abedinego. Anthuwo atasonkhana, mfumu inalamula kuti: ‘Mukangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira, mugwade n’kulambira fanoli. Aliyense amene sagwadira fanoli aponyedwa mung’anjo ya moto.’ Kodi anyamata atatu a Chiheberiwo anatani? Kodi analola kugwadira fanolo kapena anatsimikiza kulambira Yehova yekha?

Kenako mfumu inalamula kuti nyimbo iyambe. Aliyense anagwada ndi kulambira fano lija. Koma Shadireki, Misheki ndi Abedinego sanagwade. Anthu ena ataona, anauza mfumu kuti: ‘Anyamata atatu a Chiheberi aja akukanatu kulambira fanoli.’ Nebukadinezara anaitanitsa anyamatawo n’kuwauza kuti: ‘Ndikupatsani mwayi wina woti mulambire fanoli. Ngati simulambira ndikuponyani mung’anjo ya moto ndipo palibe mulungu amene angakupulumutseni m’manja mwanga.’ Iwo anayankha kuti: ‘Musavutike n’kutipatsa mwayi wina. Mulungu wathu akhoza kutipulumutsa. Koma ngati satipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sitingalambire fano lanuli.’

Nebukadinezara atamva zimenezi, anapsa mtima kwambiri. Iye anauza anthu kuti: ‘Sonkhezerani ng’anjo kuwirikiza ka 7 kuti ikhale yotentha kuposa mmene imakhalira!’ Ndiyeno analamula asilikali ake kuti: ‘Amangeni ndipo muwaponye mung’anjomo!’ Ng’anjoyo inali itatentha kwambiri moti asilikaliwo atangoyandikira, anafa nthawi yomweyo. Aheberi atatu aja anaponyedwadi mung’anjomo. Koma Nebukadinezara atasunzumira, anaona kuti mung’anjo muja munali anthu 4 osati atatu. Ataona izi, anachita mantha kwambiri ndipo anafunsa nduna zake kuti: ‘Kodi si paja tinaponya anthu atatu m’motowu? Inetu ndikuonamo anthu 4, ndipo winayo akuoneka ngati mngelo!’

Kenako Nebukadinezara anafika pafupi ndi ng’anjo ija n’kufuula kuti: ‘Tulukani inu atumiki a Mulungu wam’mwambamwamba!’ Anthu onse anadabwa kuona Shadireki, Misheki ndi Abedinego akutuluka koma sanapse paliponse. Khungu, tsitsi komanso zovala zawo sizinapse ndiponso sankamveka fungo lamoto.

Ndiyeno Nebukadinezara anati: ‘Mulungu wa Shadireki, Misheki ndi Abedinego ndi Mulungu wamkulu. Anatumiza mngelo wake kudzawapulumutsa. Palibe mulungu wina wofanana naye.’

Kodi iweyo ungakhale wokhulupirika kwa Yehova ngakhale utakumana ndi mavuto, ngati mmene anachitira anyamata a Chiheberi atatuwa?

Mfumu Nebukadinezara akudabwa ataona kuti Shadireki, Misheki ndi Abedinego akutuluka mung’anjo ya moto asanapse

“Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”​—Mateyu 4:10

Mafunso: Kodi Shadireki, Misheki ndi Abedinego anakana kuchita chiyani? Nanga Yehova anawapulumutsa bwanji?

Danieli 3:1-30

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena