Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 63 tsamba 150-tsamba 151 ndime 1
  • Dzanja Linalemba Pakhoma

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dzanja Linalemba Pakhoma
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Zolembedwa ndi Manja pa Khoma
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Koresi Wamkulu
    Galamukani!—2013
  • Anthu a Mulungu Atuluka m’Babulo
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mawu Anayi Amene Anasintha Dziko
    Samalani Ulosi wa Danieli!
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 63 tsamba 150-tsamba 151 ndime 1
Dzanja Linalemba Pakhoma

MUTU 63

Dzanja Linalemba Pakhoma

Patapita nthawi, Belisazara anakhala mfumu ya Babulo. Tsiku lina madzulo anakonza phwando ndipo anaitana nduna zake zokwana 1,000. Kenako anauza atumiki ake kuti akatenge makapu agolide amene Nebukadinezara anatenga m’kachisi wa Yehova. Iye ndi nduna zakezo anayamba kumwera vinyo m’makapuwo n’kumatamanda milungu yawo. Koma mwadzidzidzi, anangoona dzanja la munthu likulemba mawu odabwitsa pakhoma la m’chipinda chimene ankachitira phwandolo.

Belisazara anachita mantha kwambiri. Anaitana anthu a matsenga n’kuwauza kuti: ‘Aliyense amene angandiuze tanthauzo la mawuwa, ndimuika kukhala wolamulira wachitatu mu ufumu wa Babulo.’ Koma palibe anatha kumuuza tanthauzo la mawuwo. Kenako mfumukazi inabwera n’kudzamuuza kuti: ‘Pali munthu wina dzina lake Danieli amene ankauza Nebukadinezara tanthauzo la zinthu zosiyanasiyana. Akhozatu kukuuzani tanthauzo la mawuwa.’

Danieli atafika, Belisazara anamuuza kuti: ‘Ngati ungathe kuwerenga mawuwa n’kundiuza kumasulira kwake, ndikupatsa mkanda wagolide komanso ndikuika kuti ukhale wolamulira wachitatu mu ufumuwu.’ Koma Danieli anayankha kuti: ‘Sindikufuna mphatso zanuzo. Komabe ndikuwerengerani mawuwa ndiponso ndikuuzani kumasulira kwake. Bambo anu, a Nebukadinezara, anali odzikweza ndipo Yehova anawachepetsa. Inuyo mukudziwa zimene zinawachitikira, koma mukunyoza Yehova ndipo mukumwera vinyo m’makapu agolide a m’kachisi wake. Choncho Yehova walemba mawu awa: Mene, Mene, Tekeli ndi Parasini. Mawuwa akutanthauza kuti Amedi ndi Aperisiya adzagonjetsa Babulo ndipo inu simukhalanso mfumu.’

Asilikali a Mfumu Koresi akuwoloka mtsinje kukalowa pageti la mzinda wa Babulo

Pa nthawiyo zinkaoneka ngati palibe angagonjetse mzinda wa Babulo. Mzindawu unkaoneka kuti unali wotetezeka ndi mpanda wolimba komanso mtsinje waukulu. Koma usiku womwewo, Amedi ndi Aperisiya anaukira mzindawu. Mfumu ya Aperisiya, dzina lake Koresi, inapatutsa madzi a mumtsinje ndipo asilikali ake anawoloka n’kukafika pageti la mzindawu. Atafika, anapeza kuti pagetipo m’posatseka. Choncho analowa n’kulanda mzindawo komanso kupha mfumu. Ndiyeno Koresi anayamba kulamulira Babulo.

Pasanathe chaka, Koresi ananena kuti: ‘Yehova wandiuza kuti ndimangenso kachisi wake wa ku Yerusalemu. Anthu ake amene akufuna kukathandiza nawo ntchitoyi, angathe kupita.’ Choncho mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza, Ayuda ambiri anabwerera ku Yerusalemu. Apa n’kuti patatha zaka 70 kuchokera pamene Yerusalemu anawonongedwa. Koresi anabwezeretsa makapu asiliva komanso zinthu zina zimene Nebukadinezara anatenga m’kachisi wa Yehova. Kodi waona mmene Yehova anagwiritsira ntchito Koresi pothandiza anthu ake?

“Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa, ndipo wakhala malo amene ziwanda zimakhala.”​—Chivumbulutso 18:2

Mafunso: Kodi mawu amene analembedwa pakhoma ankatanthauza chiyani? Kodi Yehova anauza Koresi kuti achite chiyani?

Ezara 1:1-11; Danieli 5:1-30; Yesaya 44:27, 28; 45:1, 2; Yeremiya 25:11, 12

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena