Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 65 tsamba 154-tsamba 155 ndime 1
  • Esitere Anapulumutsa Anthu a Mtundu Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Esitere Anapulumutsa Anthu a Mtundu Wake
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mordekai ndi Estere
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Estere
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 65 tsamba 154-tsamba 155 ndime 1
Mfumukazi Esitere akukaonekera kwa Mfumu Ahasiwero

MUTU 65

Esitere Anapulumutsa Anthu a Mtundu Wake

Mfumukazi Esitere

Esitere anali mtsikana wa Chiyuda ndipo ankakhala mumzinda wa Susani ku Perisiya. Banja lawo linatengedwa ndi Nebukadinezara kuchokera ku Yerusalemu. Ndiyeno ku Perisiyako ankaleredwa ndi wachibale wake, dzina lake Moredekai, yemwe ankagwira ntchito kwa Mfumu Ahasiwero.

Pa nthawi ina, Mfumu Ahasiwero ankafuna mfumukazi yatsopano. Ndiye atumiki ake anamubweretsera akazi onse okongola a m’dzikolo. Esitere analinso gulu lomweli. Mfumuyo inasankha Esitere kuti akhale mfumukazi. Koma Moredekai anauza Esitere kuti asaulule zoti iye ndi Myuda.

M’dzikolo munali munthu wina dzina lake Hamani. Iye ankayang’anira nduna za mfumu koma anali wonyada kwambiri ndipo ankafuna kuti aliyense azimuweramira. Koma Moredekai sankaweramira Hamani. Choncho Hamani anakwiya kwambiri moti ankafuna kupha Moredekai ndipo atamva zoti Moredekai ndi Myuda, anakonza zoti aphe Ayuda onse. Anauza mfumu kuti: ‘Ayudatu ndi anthu oopsa kwambiri moti muyenera kuwapha onse.’ Zitatero mfumuyo inamupatsa mphamvu yokonza lamulo ndipo inamuuza kuti: ‘Chita chilichonse chimene ukuona kuti chithandiza.’ Hamani anakonza lamulo louza anthu kuti aphe Ayuda onse pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Koma Yehova ankaona zonsezi.

Esitere sankadziwa za lamuloli. Choncho Moredekai anamutumizira chikalata chonena za lamuloli komanso uthenga wakuti: ‘Pita ukalankhule ndi mfumu za nkhaniyi.’ Esitere anati: ‘Aliyense wopita kwa mfumu asanaitanidwe, amaphedwa. Patha masiku 30 mfumu isanandiitane. Koma ndipitabe. Akakandiloza ndi ndodo, ndiye kuti sindiphedwa. Koma akakapanda kutero ndiye kuti ndikaphedwa.’

Esitere anapitadi kwa mfumu ndipo inamuloza ndi ndodo. Kenako inamufunsa kuti: ‘Esitere, ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Esitere anayankha kuti: ‘Ndikupempha kuti inuyo ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndikonze.’ Atapita kuphwandolo, anawapempha kuti abwerenso tsiku lotsatira. Pa ulendo wachiwiriwu, mfumu inafunsanso Esitere kuti: ‘Ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Iye anayankha kuti: ‘Pali munthu wina amene akufuna kupha ineyo komanso anthu a mtundu wanga. Chonde, tipulumutseni.’ Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ndani akufuna kukuphani?’ Iye anati: ‘Ndi Hamani woipa ali apayu.’ Ahasiwero anakwiya kwambiri moti analamula kuti Hamani aphedwe nthawi yomweyo.

Komano panalibe munthu aliyense, ngakhale mfumuyo, amene akanafafaniza lamulo lija. Choncho mfumuyo inasankha Moredekai kuti akhale mkulu wa nduna zake ndipo anamupatsa mphamvu yokonza lamulo latsopano. Ndiyeno Moredekai anakonza lamulo lopatsa Ayuda mphamvu kuti akadzaukiridwa adzathe kudziteteza. Tsiku la 13 la mwezi wa Adara litafika, Ayuda anadziteteza kwa adani awo ndipo anawagonjetsa. Kuchokera pa nthawiyi Ayuda anayamba kukondwerera tsiku limeneli chaka chilichonse.

“Adzakupititsani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa ndinu otsatira anga, kuti iwowo komanso anthu a mitundu ina aphunzire za ine.”​—Mateyu 10:18

Mafunso: Kodi Hamani anakonzera Ayuda chiwembu chotani? Kodi Esitere anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova?

Esitere 2:5-20; 3:1-15; 4:1-17; 5:1-8; 7:1-10; 8:1-14; 9:1-28

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena