Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 68 tsamba 162-tsamba 163 ndime 1
  • Elizabeti Anakhala ndi Mwana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Elizabeti Anakhala ndi Mwana
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Kubadwa kwa Wokonza Njira
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Iwo Anafupidwa Chifukwa Choyenda Mosachimwa
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mauthenga Awiri Ochokera kwa Mulungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Wokonza Njira Abadwa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 68 tsamba 162-tsamba 163 ndime 1
Zekariya akuuza anthu kuti dzina la mwana wake likhala Yohane

MUTU 68

Elizabeti Anakhala ndi Mwana

Patatha zaka zoposa 400 kuchokera pamene mpanda wa Yerusalemu unakonzedwa, wansembe wina ankakhala pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Dzina lake anali Zekariya ndipo mkazi wake anali Elizabeti. Iwo anakhala m’banja zaka zambiri koma analibe mwana. Tsiku lina Zekariya akupereka nsembe m’nyumba yopatulika, anaona mngelo Gabirieli. Zekariya anachita mantha kwambiri, koma Gabirieli anamuuza kuti: ‘Usaope. Ndakubweretsera uthenga wabwino wochokera kwa Yehova. Mkazi wako adzakhala ndi mwana ndipo dzina lake lidzakhala Yohane. Yehova akufuna kuti Yohaneyo adzagwire ntchito yapadera.’ Zekariya anafunsa kuti: ‘Ndingakhulupirire bwanji zimene mukunenazi? Ine ndi mkazi wanga ndife okalamba ndipo n’zosatheka kukhala ndi mwana.’ Gabirieli anati: ‘Mulungu ndi amene wandituma kuti ndidzakuuze zimenezi. Koma poti sukukhulupirira, ukhala wosalankhula mpaka mwanayo adzabadwe.’

Zekariya anakhala m’nyumba yopatulikayo kwa nthawi yaitali mosiyana ndi masiku onse. Ndiyeno atatuluka, anthu ankafuna kudziwa chimene chinamuchedwetsa. Koma Zekariya sankatha kulankhula. Ndiyeno anangoyamba kulankhula pogwiritsa ntchito manja. Anthuwo anazindikira kuti iye walandira uthenga wochokera kwa Mulungu.

Patapita nthawi, zimene mngelo uja ananena zinachitikadi. Elizabeti anakhala woyembekezera ndipo kenako anabereka mwana wamwamuna. Anzake a Elizabeti komanso achibale ake anabwera kudzaona mwanayo ndipo anasangalala kwambiri. Ndiyeno Elizabeti anawauza kuti: ‘Dzina la mwanayu ndi Yohane.’ Anthuwo anati: ‘Koma m’banja lanu mulibe aliyense amene ali ndi dzina limeneli. Bwanji atenge dzina la bambo ake lakuti Zekariya?’ Zitatero, Zekariya analemba kuti: ‘Dzina lake ndi Yohane.’ Atangolemba zimenezi, anayamba kulankhula. Nkhani ya mwanayu inafalikira mu Yudeya monse ndipo anthu ankadabwa kuti: ‘Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani akadzakula?’

Zekariya anadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndiyeno ananena kuti: ‘Yehova atamandike. Analonjeza Abulahamu kuti adzatumiza Mesiya kuti atipulumutse. Yohane adzakhala mneneri ndipo adzakonza njira ya Mesiya.’

Pa nthawi yomweyi, zinthu zina zochititsa chidwi zinachitikiranso m’bale wake wa Elisabeti, dzina lake Mariya. M’mutu wotsatira tikambirana nkhani yake.

“Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”​—Mateyu 19:26

Mafunso: Kodi Gabirieli anauza chiyani Zekariya? Kodi Yehova ankafuna kuti Yohane agwire ntchito yapadera iti?

Mateyu 11:7-14; Luka 1:5-25, 57-79; Yesaya 40:3; Malaki 3:1

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena