MUTU 69
Gabirieli Analankhula ndi Mariya
Elizabeti anali ndi m’bale wake wachitsikana dzina lake Mariya. Iye ankakhala mumzinda wa Nazarete ku Galileya. Mtsikanayu anali pa chibwenzi ndi kalipentala wina dzina lake Yosefe. Ndiyeno patatha miyezi 6 Elizabeti ali woyembekezera, mngelo Gabirieli anapita kwa Mariya n’kumuuza kuti: ‘Moni Mariya. Yehova wakukomera mtima kwambiri.’ Mariya sanamvetse zimene mngeloyu ankatanthauza. Ndiyeno Gabirieli anamuuza kuti: ‘Udzakhala woyembekezera n’kubereka mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu. Iye adzakhala Mfumu ndipo Ufumu wake sudzatha.’
Mariya anafunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zidzatheka bwanji, chifukwa sindinagonepo ndi mwamuna.’ Gabirieli anamuuza kuti: ‘Mulungu sangalephere kuchita chilichonse. Mzimu woyera udzafika pa iwe ndipo udzakhala ndi mwana. Kodi ukudziwa kuti panopa m’bale wako Elizabeti ndi woyembekezera?’ Zitatero, Mariya anayankha kuti: ‘Ndine kapolo wa Yehova. Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.’
Mariya anauyamba ulendo wopita kukaona Elizabeti. Pa nthawiyi, Elizabeti ankakhala mumzinda winawake wakumapiri. Atafika, n’kupereka moni, mwana amene anali m’mimba mwa Elizabeti anayamba kudumpha. Ndiyeno Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera n’kuyamba kunena kuti: ‘Mariya, Yehova wakudalitsa. Ndi mwayi waukulu kuti mayi wa Ambuye wanga wafika m’nyumba mwanga.’ Mariya anati: ‘Moyo wanga ukulemekeza Yehova.’ Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa miyezi itatu ndipo kenako anabwerera kwawo ku Nazareti.
Yosefe atamva zoti Mariya ndi woyembekezera ankafuna kuthetsa chibwenzi. Koma ali m’tulo mngelo anamuuza kuti: ‘Usaope kutenga Mariya kuti akhale mkazi wako chifukwa sanachite choipa chilichonse.’ Choncho Yosefe anatengadi Mariya n’kumakakhala naye kwawo.
“Yehova amachita chilichonse chimene wafuna kumwamba ndi padziko lapansi.”—Salimo 135:6