Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 75 tsamba 178-tsamba 179 ndime 4
  • Mdyerekezi Anayesa Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mdyerekezi Anayesa Yesu
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Tifunika Kukana Ziyeso
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • “Tsutsani Mdyerekezi” Monga Anachitira Yesu
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Zimene Yesu Anachita Atayesedwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuphunzira Kuchokera Kuziyeso za Yesu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 75 tsamba 178-tsamba 179 ndime 4
Yesu akukana kudumpha pamwamba pa kachisi

MUTU 75

Mdyerekezi Anayesa Yesu

Yesu akukana kusandutsa miyala kuti ikhale mkate

Yesu atabatizidwa mzimu woyera unamutsogolera kupita kuchipululu. Sanadye chilichonse kwa masiku 40 choncho anali ndi njala kwambiri. Ndiyeno Mdyerekezi anabwera kudzamuyesa ndipo anamuuza kuti: ‘Ngati ndinudi Mwana wa Mulungu, uzani miyalayi kuti isanduke mitanda ya mkate.’ Koma Yesu anamuyankha potchula zimene Malemba amanena. Anati: ‘Malemba amanena kuti munthu safunika chakudya chokha kuti akhale ndi moyo. Amafunikanso kumvera mawu alionse ochokera m’kamwa mwa Yehova.’

Kenako Mdyerekezi anauza Yesu kuti: ‘Ngati ndinudi Mwana wa Mulungu, mudumphe kuchokera pamwamba pa kachisi. Pajatu Malemba amanena kuti Mulungu adzatumiza angelo ake kuti adzakunyamuleni kuti musavulale.’ Koma Yesu anayankhanso pogwiritsa ntchito Malemba. Iye anati: ‘Malemba amanena kuti usamuyese Yehova.’

Yesu akukana kupatsidwa maufumu ndi Satana

Kenako Mdyerekezi anaonetsa Yesu maufumu onse a padziko lapansi ndi chuma chawo. Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Ndikupatsani maufumu onsewa ndi chuma chonsechi ngati mutagwada pansi kamodzi kokha n’kundilambira.’ Koma Yesu anayankha kuti: ‘Choka Satana! Malemba amati, uyenera kulambira Yehova yekha basi.’

Yesu atanena zimenezi, Mdyerekezi anamusiya ndipo angelo anabwera kudzamupatsa chakudya. Izi zitatha, Yesu anayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Imeneyi ndi ntchito imene Mulungu anamutuma kuti adzachite. Anthu ankakonda zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ankamutsatira kulikonse kumene wapita.

“[Mdyerekezi] akamanena bodza, amangosonyeza mmene alili, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”​—Yohane 8:44

Mafunso: Kodi Mdyerekezi anayesa Yesu ndi mayesero atatu ati? Nanga Yesu anamuyankha bwanji?

Mateyu 4:1-11; Maliko 1:12, 13; Luka 4:1-15; Deuteronomo 6:13, 16; 8:3; Yakobo 4:7

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena