Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 85 tsamba 198-tsamba 199 ndime 1
  • Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kusakhulupirira Kouma Khosi kwa Afarisi
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Afarisi Akana Dala Kukhulupirira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kuchiritsa Munthu Wobadwa Wakhungu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 85 tsamba 198-tsamba 199 ndime 1
Afarisi akufunsa munthu amene poyamba anali wosaona

MUTU 85

Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata

Afarisi ankadana ndi Yesu ndipo ankafuna kuti am’pezere chifukwa kuti amumange. Iwo ankanena kuti Yesu sakuyenera kumachiritsa anthu pa Sabata. Pa tsiku lina la Sabata, Yesu anakumana ndi munthu amene anali ndi vuto losaona amene ankapemphapempha mumsewu. Iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Dikirani muone mmene mphamvu za Mulungu zingamuthandizire munthuyu.’ Kenako Yesu analavulira pansi n’kukanda thope ndi malovuwo. Ndiyeno anapaka thopelo m’maso mwa munthuyo n’kumuuza kuti: “Pita ukasambe m’dziwe la Siloamu.” Munthuyo anapitadi ndipo anayamba kuona.

Anthu anadabwa kwambiri ndi zimenezi moti anati: ‘Kodi munthuyu ndi amene amapemphapempha uja, kapena ndi wina angofanana?’ Munthuyo anati: ‘Ndine ndemwe ndithu ndipo ndinabadwa wosaona.’ Anthuwo anamufunsa kuti: ‘Ndiye chachitika n’chiyani kuti uyambe kuona?’ Atawafotokozera zomwe zachitika, anamutenga n’kupita naye kwa Afarisi.

Munthuyo anauza Afarisiwo kuti: ‘Yesu anakanda thope n’kundipaka m’maso ndipo kenako anandiuza kuti ndikasambe. Ndinapitadi ndipo nditasamba ndinayamba kuona.’ Koma Afarisiwo anati: ‘Ngati Yesu akumachiritsa anthu pa Sabata ndiye kuti mphamvu zake sizingakhale zochokera kwa Mulungu.’ Koma ena anati: ‘Zikanakhala kuti mphamvu zake si zochokera kwa Mulungu, si bwenzi akuchiritsa anthu.’

Afarisi anaitana makolo ake a munthuyo n’kuwafunsa kuti: ‘Zatheka bwanji kuti mwana wanu ayambe kuona?’ Koma makolowo ankaopa chifukwa Afarisi ankachotsa musunagoge munthu aliyense wokhulupirira Yesu. Choncho anangoyankha kuti: ‘Sitikudziwa. Mufunseni mwiniwakeyo.’ Afarisiwo anafunsa munthuyo mafunso ambirimbiri mpaka iye anawayankha kuti: ‘Ndakuuzani kale zonse. N’chifukwa chiyani mukungondifunsabe?’ Afarisiwo anakwiya ndi zimenezi ndipo anamuponyera kunja.

Yesu anapita kumene kunali munthuyo ndipo anamufunsa kuti: ‘Kodi umakhulupirira Mesiya?’ Munthuyo anayankha kuti: ‘Eya ndingamukhulupirire nditakhala kuti ndikumudziwa.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Ineyo ndine Mesiya.’ Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti anali wokoma mtima. Tikutero chifukwa anachiritsa munthuyo komanso anamuthandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro.

“Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.”​—Mateyu 22:29

Mafunso: Kodi Yesu anathandiza bwanji munthu amene anali ndi vuto losaona? N’chifukwa chiyani Afarisi ankadana ndi Yesu?

Yohane 9:1-41

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena