Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 90 tsamba 210
  • Yesu Anaphedwa ku Gologota

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anaphedwa ku Gologota
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Pilato Komanso Herode Sanamupeze Yesu ndi Mlandu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuchokera kwa Pilato Kunka kwa Herode Nkubwereranso
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kuchokera kwa Pilato Kumka kwa Herode ndi Kubwereranso
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kodi Pontiyo Pilato Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 90 tsamba 210
Yesu wapachikidwa pamtengo ndipo msilikali komanso ophunzira ena a Yesu, kuphatikizapo Mariya ndi Yohane, aima chapafupi

MUTU 90

Yesu Anaphedwa ku Gologota

Ansembe aakulu anatenga Yesu n’kupita naye kwa bwanamkubwa wina dzina lake Pilato. Pilatoyo anafunsa anthuwo kuti: ‘Kodi munthuyu walakwa chiyani?’ Iwo anayankha kuti: ‘Akunena kuti ndi mfumu yathu.’ Ndiyeno Pilato anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?’ Yesu anayankha kuti: ‘Ufumu wanga si wapadzikoli.’

Zitatero, Pilato anatumiza Yesu kwa Herode, amene anali wolamulira chigawo cha Galileya, kuti akaone ngati Yesuyo alidi ndi mlandu. Koma Herode anapeza kuti Yesu sanalakwe chilichonse. Choncho anamutumizanso kwa Pilato. Ndiyeno Pilato anauza anthuwo kuti: ‘Ine ndi Herode taona kuti munthuyu ndi wosalakwa. Choncho ndimumasula.’ Koma anthuwo anakuwa kuti: ‘Mupheni! Mupheni!’ Asilikali anayamba kukwapula Yesu, kumulavulira komanso kumumenya. Anamuvekanso chipewa chaminga n’kumamunyoza kuti: ‘Muli bwanji Mfumu ya Ayuda?’ Pilato anauzanso anthuwo kuti: ‘Ine sindinam’peze ndi mlandu uliwonse munthuyu.’ Koma anthuwo anakuwanso kuti: “Apachikidwe ameneyo!” Choncho Pilato anawapatsa Yesu kuti akamupachike.

Ndiyeno anapita naye kumalo otchedwa Gologota ndipo anakamukhomerera pamtengo n’kuimika mtengowo. Koma Yesu anapemphera kuti: ‘Atate, muwakhululukire chifukwa sakudziwa zimene akuchita.’ Anthu anayamba kunyoza Yesu n’kumanena kuti: ‘Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, tsika pamtengopo. Dzipulumutse wekha.’

Wachifwamba wina amene anapachikidwa pafupi ndi Yesu anamuuza kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.” Atatero, Yesu anamulonjeza kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Masana kunagwa mdima m’dziko lonselo kwa maola atatu. Mayi ake komanso ophunzira ake ena anali chapafupi. Yesu anauza Yohane kuti azisamalira Mariya ngati mayi ake enieni.

Kenako Yesu anauza Mulungu kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” Ndiyeno anaweramira pansi n’kumwalira. Pa nthawi imeneyo panachitika chivomerezi champhamvu. Komanso chinsalu cha m’kachisi chomwe chinkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa chinang’ambika pakati. Mkulu wa asilikali ataona zimenezi anati: ‘Uyu analidi Mwana wa Mulungu.’

“Malonjezo a Mulungu, kaya akhale ambiri bwanji, akhala “inde” kudzera mwa iye.”​—2 Akorinto 1:20

Mafunso: N’chifukwa chiyani Pilato analola kuti Yesu aphedwe? Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankaganizira kwambiri za anthu ena kuposa iyeyo?

Mateyu 27:11-14, 22-31, 38-56; Maliko 15:2-5, 12-18, 25, 29-33, 37-39; Luka 23:1-25, 32-49; Yohane 18:28-40; 19:1-30

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena