Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 94 tsamba 220-tsamba 221 ndime 1
  • Ophunzira a Yesu Analandira Mzimu Woyera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ophunzira a Yesu Analandira Mzimu Woyera
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Akuyembekezera m’Yerusalemu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • ‘M’Dzina la Mzimu Woyera’
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Yehova Ndiye Wolamulira Wathu!
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 94 tsamba 220-tsamba 221 ndime 1
Anthu a ku Yerusalemu akudabwa kumva ophunzira a Yesu akulankhula nawo m’zilankhulo zawo

MUTU 94

Ophunzira a Yesu Analandira Mzimu Woyera

Patadutsa masiku 10 Yesu atapita kumwamba, ophunzira ake analandira mzimu woyera. Linali tsiku la mwambo wa Pentekosite m’chaka cha 33 C.E. Ku Yerusalemu munali anthu ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana amene anabwera kumwambowu. Ophunzira a Yesu okwana 120 anasonkhana m’chipinda china cham’mwamba. Mwadzidzidzi, panachitika zinthu zodabwitsa. Tinthu tina tooneka ngati malawi a moto tinaoneka pamutu pa wophunzira aliyense ndipo onsewo anayamba kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana. Kenako mkokomo wangati mphepo yamphamvu unamveka panyumba yonseyo.

Anthu amene anabwera ku Yerusalemu aja anamva mkokomowu ndipo anathamangira kunyumba yomwe kunali ophunzirawo kuti akaone chimene chikuchitika. Anadabwa kwambiri atamva kuti ophunzirawo akulankhula zilankhulo zosiyanasiyana. Anthuwo anati: ‘Komatu anthuwa ndi a ku Galileya. Ndiye zikutheka bwanji kuti azilankhula zilankhulo zathu?’

Kenako Petulo ndi atumwi ena anaimirira n’kuyamba kulankhula ndi anthuwo. Petulo anawafotokozera kuti Yesu anaphedwa ndipo Yehova anamuukitsa. Ndiyeno ananena kuti: ‘Panopa Yesu ali kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu ndipo watipatsa mzimu woyera umene anatilonjeza. N’chifukwa chake mukuona zodabwitsazi.’

Anthuwo anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene Petulo ananena moti anafunsa kuti: “Tichite chiyani pamenepa?” Iye anawauza kuti: ‘Lapani machimo anu ndipo mubatizidwe m’dzina la Yesu. Mukatero nanunso mulandira mzimu woyera.’ Pa tsikuli anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa. Zitatero, ophunzira anayamba kuwonjezeka mofulumira kwambiri ku Yerusalemu. Mzimu woyera unkathandiza kwambiri atumwi ndipo anakhazikitsa mipingo kuti azitha kuphunzitsa anthu zinthu zonse zimene Yesu anawalamula.

“Ngati ukulengeza mawu amene ali mʼkamwa mwakowo, akuti Yesu ndi Ambuye, ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa, udzapulumuka.”​—Aroma 10:9

Mafunso: Kodi n’chiyani chinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E.? N’chiyani chinachititsa kuti anthu ambiri abatizidwe?

Machitidwe 1:15; 2:1-42; 4:4; Yohane 15:26

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena