Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 95 tsamba 222-tsamba 223 ndime 1
  • Sanasiye Kulalikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sanasiye Kulalikira
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • “Ife Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Amasulidwa m’Ndende
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • ‘Sitingaleke Kulankhula za Yesu’
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Yehova Ndiye Wolamulira Wathu!
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 95 tsamba 222-tsamba 223 ndime 1
Petulo ndi Yohane akulalikira molimba mtima ngakhale kuti akutsutsidwa ndi ansembe komanso Asaduki

MUTU 95

Sanasiye Kulalikira

Munthu wina wosayenda ankakhala pakhomo la kachisi n’kumapemphapempha. Tsiku lina madzulo, munthuyo anaona Petulo ndi Yohane akulowa m’kachisi. Iye anati: ‘Ndithandizeni!’ Petulo anamuyankha kuti: ‘Ndikupatsa chinthu chabwino kwambiri kuposa ndalama. M’dzina la Yesu dzuka n’kuyamba kuyenda.’ Kenako anamugwira n’kumudzutsa ndipo anayambadi kuyenda. Anthu anasangalala kwambiri moti ambiri anakhala ophunzira.

Koma ansembe ndi Asaduki anakwiya kwambiri. Iwo anagwira atumwiwo n’kupita nawo kukhoti ndipo anawafunsa kuti: ‘Mphamvu yochiritsira munthuyu mwaitenga kuti?’ Petulo ananena kuti: ‘Yesu amene munamupha uja ndi amene watipatsa mphamvu.’ Ndiyeno atsogoleri achipembedzo ananena mokalipa kuti: ‘Musiyiretu kunena za Yesu.’ Koma atumwiwo anayankha kuti: ‘Ife sitisiya ndipo tizinenabe.’

Petulo ndi Yohane atangomasulidwa, anapita kwa ophunzira ena kukawauza zimene zinachitikazo. Iwo anapemphera limodzi kuti: ‘Chonde Yehova tithandizeni kuti tikhale olimba mtima kuti tizilalikirabe.’ Yehova anawapatsa mzimu woyera ndipo anapitiriza kulalikira ndi kuchiritsa anthu. Anthu ambiri anakhala ophunzira. Koma Asaduki zinkawapwetekabe moti anamanga atumwiwo n’kuwatsekera m’ndende. Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo usiku kuti akatsegule zitseko za ndendeyo n’kuuza atumwiwo kuti: ‘Bwererani kukachisi muzikaphunzitsa anthu.’

Tsiku lotsatira, Khoti Lalikulu la Ayuda linauzidwa kuti: ‘Zitseko za ndende n’zotseka koma anthu aja mulibe. Iwo ali kukachisi ndipo akuphunzitsa anthu.’ Anthu anapita kukawamanganso n’kupita nawo ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Atafika, mkulu wa ansembe anati: ‘Kodi sitinakuuzeni kuti musiye kunena za Yesu?’ Koma Petulo anayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”

Atsogoleri achipembedzo anakwiya kwambiri moti ankafuna kupha atumwiwo. Koma Mfarisi wina dzina lake Gamaliyeli anaimirira n’kunena kuti: ‘Anthu inu samalani. Anthuwatu ayenera kuti akuthandizidwa ndi Mulungu. Kodi mukufuna kulimbana ndi Mulungu?’ Anthuwo anamvera mawu ake moti anangowakwapula atumwiwo n’kuwauza kuti azipita ndipo asakalalikirenso. Koma atumwiwo sanasiye kulalikira. Iwo ankalalikirabe mwakhama m’kachisi komanso kunyumba ndi nyumba.

“Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29

Mafunso: N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu sanasiye kulalikira? Kodi Yehova anawathandiza bwanji?

Machitidwe 3:1-26; 4:1-31; 5:12-42

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena