Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 98 tsamba 228-tsamba 229 ndime 1
  • Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga Wabwino
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo Chouziridwa cha Ntchito Yaumishonale Wachikristu
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Anthu a Yehova Alimbitsidwa m’Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Anapitiriza Kukhala Osangalala Komanso Mzimu Woyera Unkawathandiza Kwambiri”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • “Ankalankhula Molimba Mtima Chifukwa cha Mphamvu ya Yehova”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 98 tsamba 228-tsamba 229 ndime 1
Mtumwi Paulo ndi Baranaba akulalikira kwa bwanamkubwa wina dzina lake Serigio Paulo

MUTU 98

Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga Wabwino

Atumwi anamvera lamulo la Yesu loti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse. Mu 47 C.E., abale a ku Antiokeya anatumiza Paulo ndi Baranaba kuti akalalikire. Anthu awiriwa anazungulira ku Asia Minor ndipo anafika ku Debe, ku Lusitara ndi ku Ikoniyo.

Paulo ndi Baranaba ankalalikira kwa aliyense mosaganizira kuti ndi wolemera kapena wosauka, wamkulu kapena wamng’ono. Ambiri ankamvetsera ndithu. Paulo ndi Baranaba akulalikira kwa bwanamkubwa wina dzina lake Serigio Paulo, munthu wina wamatsenga ankafuna kusokoneza. Ndiyeno Paulo anamuuza kuti: ‘Iwe Yehova akulanga.’ Nthawi yomweyo munthuyo anasiya kuona. Bwanamkubwa uja ataona zimenezo anakhala wokhulupirira.

Paulo ndi Baranaba ankalalikira m’nyumba za anthu, m’misika, m’misewu ndiponso m’masunagoge. Atafika ku Lusitara anachiritsa munthu wina wolumala. Ndiyeno anthu ataona zimenezi ankafuna kuwalambira poganiza kuti iwowo ndi milungu. Koma Paulo ndi Baranaba anawauza kuti: ‘Anthu inu, ifetu ndi anthu ngati inu nomwe. Muzilambira Mulungu yekha.’ Koma kenako kunabwera Ayuda amene anasokoneza maganizo a anthu. Nthawi yomweyo anthuwo anayamba kugenda Paulo ndi miyala kenako anamukokera kunja kwa mzinda poganiza kuti wafa. Koma Paulo anali adakali ndi moyo. Kenako abale anapita kukamutenga n’kupita naye mumzinda. Patapita nthawi, Paulo anabwerera ku Antiokeya.

Mu 49 C.E., Paulo anauyambanso ulendo wina. Atachoka ku Asia Minor, anapita kukalalikira ku Ulaya. Iye anafika ku Atene, ku Filipi, ku Tesalonika komanso m’madera ena. Pa ulendowu anali ndi Sila, Luka komanso mnyamata wina dzina lake Timoteyo. Iwo anagwira limodzi ntchito yokhazikitsa mipingo komanso kuilimbikitsa. Paulo anakhala ku Korinto kwa chaka chimodzi ndi hafu n’cholinga choti alimbikitse abale akumeneko. Iye ankalalikira, kuphunzitsa komanso kulemba makalata opita kumipingo yosiyanasiyana. Koma ankagwiranso ntchito yopanga matenti kuti azipezako ndalama. Kenako Paulo anabwerera ku Antiokeya.

Mtumwi Paulo akulalikira mumsika

Mu 52 C.E., Paulo anauyamba ulendo wachitatu. Atachoka ku Asia Minor anafika ku Filipi, komwe ndi kumpoto kwenikweni ndipo kenako anapita ku Korinto. Iye anakhala zaka zingapo ku Efeso komwe ankaphunzitsa, kuchiritsa anthu komanso kuthandiza mpingo wakumeneko. Tsiku lililonse, ankakamba nkhani muholo yapasukulu ina. Anthu ambiri ankamvetsera uthenga wake ndipo anasintha makhalidwe awo. Paulo atalalikira m’madera ambiri anapita ku Yerusalemu.

“Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.”​—Mateyu 28:19

Mafunso: Pogwiritsa ntchito mapu amene ali mu Baibulo la Dziko Latsopano, (Zakumapeto B 13) fotokozani mmene Paulo anayendera pa maulendo ake.

Machitidwe chaputala 13 mpaka 23

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena