Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 99 tsamba 230-tsamba 231 ndime 4
  • Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a Yehova
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • “Wolokerani ku Makedoniya Kuno”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Sila Munthu Wolimbikitsa Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—1999
  • ‘Kodi Ndichitenji Kuti Ndipulumuke?’
    Nsanja ya Olonda—1989
  • ‘Mtendere wa Mulungu Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 99 tsamba 230-tsamba 231 ndime 4
Woyang’anira ndende ku Filipi anapeza zitseko zili zotseguka koma anthu ali momwemo

MUTU 99

Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a Yehova

Ku Filipi kunali mtsikana wina wantchito amene anali ndi chiwanda. Chiwandacho chinkachititsa kuti mtsikanayo azilosera zam’tsogolo ndipo ankalemeretsa mabwana ake. Ndiyeno Paulo ndi Sila atafika ku Filipiko, mtsikanayo ankawatsatira kwa masiku ambiri. Chiwandacho chinkamuchititsa kufuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wam’mwambamwamba!” Paulo atatopa nazo anauza chiwandacho kuti: ‘Ndikukulamula m’dzina la Yesu kuti utuluke mwa mtsikanayu!’ Nthawi yomweyo chiwandacho chinamusiya.

Mabwana a mtsikanayu ataona kuti mwayi wawo wopeza ndalama watha, anakwiya kwambiri. Iwo anagwira Paulo ndi Sila n’kuwakokera kubwalo la olamulira ndipo anati: ‘Anthu awa akuphwanya malamulo ndipo akusokoneza kwambiri mzindawu.’ Ndiyeno akuluakulu a boma analamula kuti Paulo ndi Sila akwapulidwe kenako atsekeredwe m’ndende. Anawaika m’ndende yamdima kwambiri ndipo anawamangirira m’matangadza.

M’ndendemo, Paulo ndi Sila ankaimba nyimbo zotamanda Mulungu ndipo akaidi ena ankamvetsera. Ndiyeno pakati pa usiku, kunachitika chivomerezi chomwe chinagwedeza kwambiri ndendeyo. Zitseko zonse zinatseguka ndipo maunyolo a akaidi onse anamasuka. Woyang’anira ndende uja atathamanga n’kupeza kuti zitseko zatseguka anaganiza kuti akaidi onse athawa. Choncho anatenga lupanga kuti adziphe.

Koma Paulo anamuuza kuti: ‘Usadzivulaze! Tonse tili mommuno!’ Woyang’anira ndendeyo analowa msanga n’kugwada pafupi ndi Paulo ndi Sila. Kenako anafunsa kuti: ‘Ndichite chiyani kuti ndidzapulumuke?’ Iwo anamuyankha kuti: ‘Iweyo ndi banja lako muyenera kukhulupirira Yesu.’ Kenako Paulo ndi Sila anayamba kuphunzitsa woyang’anira ndendeyo ndi banja lake Mawu a Yehova ndipo onse anabatizidwa.

“Anthu adzakugwirani n’kukuzunzani ndipo adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakupititsani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa. Zimenezi zidzakupatsani mpata woti muchitire umboni.”​—Luka 21:12, 13

Mafunso: Kodi Paulo ndi Sila anamangidwa chifukwa chiyani? Kodi chinachitika n’chiyani kuti woyang’anira ndende aphunzire Mawu a Yehova?

Machitidwe 16:16-34

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena