NYIMBO 11
Chilengedwe Chimatamanda Mulungu
Losindikizidwa
1. Munalenga chilengedwe chonse
Ndipotu chimakutamandani.
Ngakhale sichitulutsa mawu,
Chimakutamandani Yehova.
Ngakhale sichitulutsa mawu,
Chimakutamandani Yehova.
2. Anthu omwe amakuopani
Adzapeza nzeru yeniyeni.
Mfundo zanu zoposa golide
N’zothandiza ana ndi akulu.
Mfundo zanu zoposa golide
N’zothandiza ana ndi akulu.
3. Anthu omwe amakumverani
Amakhala ndi moyo wabwino.
Onse oyeretsa dzina lanu
Mudzawapatsatu madalitso.
Onse oyeretsa dzina lanu
Mudzawapatsatu madalitso.
(Onaninso Sal. 12:6; 89:7; 144:3; Aroma 1:20.)