NYIMBO 19
Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
Losindikizidwa
1. Yehova M’lungu wakumwamba,
Lerotu ndi lapadera.
Kale patsikuli munatisonyeza
Chikondi, nzeru ndi mphamvu.
Magazi a mwana wankhosa
Anapulumutsa anthu,
Kenako Yesu anakhetsa magazi
Kukwaniritsa ulosiwu.
2. Tikuona mkate ndi vinyo
Zomwe zikutikumbutsa
Kufunika kwa Nsembe ya
Yesu Khristu.
Ndi mphatso yapaderadi.
Madzulo ano tiyenera
Kuchita chikumbutsochi
Pokumbukira
Zomwe zinachitika
Kuti dipo liperekedwe.
3. Tasonkhana pamaso panu.
Tamva kuitana kwanu.
Titamande inu
Ndi Mwana wanunso.
Munatikonda kwambiri.
Mwambowu ndi wolimbitsadi
Chikhulupiriro chathu.
Tiyendebe motsatira Yesu Khristu
Ndipo tidzapezadi moyo.
(Onaninso Luka 22:14-20; 1 Akor. 11:23-26.)