NYIMBO 26
“Munachitiranso Ine”
1. Yesu alitu ndi nkhosa zina ndipo
Zimatumikira ndi odzozedwa.
Zimene nkhosazo
Zingawachitire,
Yesu adzawabwezera zomwezo.
(KOLASI)
‘Mwakuwathandiza, mwandithandiza.
Zonse zimene munawachitira
Munachitiranso ine amene.
Zonse zomwe munawachitira
Munachitiranso ine amene.’
2. Pamene ndinali wanjala ndi ludzu
Munandithandiza mwamsanga ndithu.
‘Mbuye, tinachita
Liti zimenezi?’
Ndiye Mfumuyo idzayankha kuti:
(KOLASI)
‘Mwakuwathandiza, mwandithandiza.
Zonse zimene munawachitira
Munachitiranso ine amene.
Zonse zomwe munawachitira
Munachitiranso ine amene.’
3. Mwakhulupirika pochita zabwino,
Polalikira ndi abale anga.
Choncho Mfumuyo
Idzauza nkhosazo:
‘Landirani dziko, moyo wosatha.’
(KOLASI)
‘Mwakuwathandiza, mwandithandiza.
Zonse zimene munawachitira
Munachitiranso ine amene.
Zonse zomwe munawachitira
Munachitiranso ine amene.’
(Onaninso Miy. 19:17; Mat. 10:40-42; 2 Tim. 1:16, 17.)